Kodi Mungatani Kuti Musamaope Kwambiri Imfa?
Yankho la m’Baibulo
N’zoona kuti timaopa imfa popeza ndi mdani wathu ndipo timayesetsa kuchita zinthu zoyenerera zotetezera moyo wathu. (1 Akorinto 15:26) Koma anthu ena amaopa kwambiri imfa chifukwa amakhulupirira zinthu zabodza kapena mizimu, ndipo zimenezi zimawachititsa kuti akhale “mu ukapolo moyo wawo wonse.” (Aheberi 2:15) Choncho munthu akadziwa zoona zake pa nkhaniyi, saopa kwambiri imfa ndipo zimenezi zingamuthandize kuti azisangalala ndi moyo.—Yohane 8:32.
Zoona zake zokhudza imfa
Anthu akufa sadziwa kanthu. (Salimo 146:4) Simukuyenera kuopa kuti mukadzamwalira muzikazunzika chifukwa Baibulo limayerekezera imfa ndi tulo.—Salimo 13:3; Yohane 11:11-14.
Anthu akufa sangativulaze. Ngakhale anthu amene anali okonda zachiwawa pamene anali ndi moyo, akamwalira amakhala “anthu akufa.” (Miyambo 21:16) Baibulo limati “chidani chawo ndiponso nsanje yawo zatha kale.”—Mlaliki 9:6.
Sikuti munthu aliyense akamwalira ndiye kuti zake zathera pomwepo. Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Mulungu akulonjeza nthawi imene “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Ponena za nthawi imeneyo, Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” Iwo sadzaopanso ngakhale pang’ono kuti mwina akhoza kufa.—Salimo 37:29.