N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?
Yankho la m’Baibulo
M’Baibulo muli mfundo zotithandiza kuti tilimvetse. Kaya ndife anthu otani, uthenga wa Mulungu umene uli m’Baibulo ‘si wovuta kutsatira, ndipo si wapatali.’—Deuteronomo 30:11.
Mfundo zimene zingakuthandizeni kumvetsa Baibulo
Muzikhala ndi maganizo oyenera. Muziona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Muzikhala ndi mtima wodzichepetsa popeza Mulungu amatsutsa odzikweza. (1 Atesalonika 2:13; Yakobo 4:6) Koma musamangokhulupirira zinthu popanda umboni chifukwa Mulungu amafuna kuti muzigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.”—Aroma 12:1, 2.
Muzipempha nzeru. Pa Miyambo 3:5, Baibulo limati: “Usadalire luso lako lomvetsa zinthu.” M’malomwake, ‘tizipempha kwa Mulungu’ kuti atipatse nzeru zotithandiza kumvetsa Baibulo.—Yakobo 1:5.
Muziphunzira nthawi zonse. Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kwambiri ngati mumaliphunzira nthawi zonse osati modumphadumpha.—Yoswa 1:8.
Muziphunzira mwadongosolo. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo n’kufufuza zimene Malemba amanena pa nkhani inayake. Muziyamba ndi nkhani zosavuta kenako n’kufufuza nkhani zovutirapo. (Aheberi 6:1, 2) Mukamayerekezera lemba lina ndi linzake mudzaona kuti Baibulo limafotokoza lokha zinthu, ngakhale “zinthu zina zovuta kuzimvetsa.”—2 Petulo 3:16.
Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipempha anthu ena kutithandiza kumvetsa Baibulo. (Machitidwe 8:30, 31) A Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibulo mwaulere. Mofanana ndi zimene Akhristu oyambirira ankachita, iwo amagwiritsa ntchito malemba pothandiza anthu kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.—Machitidwe 17:2, 3.
Zinthu zimene si zofunika
Nzeru kapena maphunziro apamwamba. Atumwi 12 a Yesu ankamvetsa Malemba ndiponso kuwaphunzitsa ngakhale kuti anthu ena ankawaona kuti ndi “osaphunzira ndiponso anthu wamba.”—Machitidwe 4:13.
Ndalama. Mukhoza kuphunzira Baibulo popanda kulipira chilichonse. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8.