Kodi Yehova Ndi Ndani?
Yankho la m’Baibulo
Yehova ndi dzina la Mulungu woona limene limapezeka m’Babulo ndipo iye ndi Mlengi wa zinthu zonse. (Chivumbulutso 4:11) Mneneri Abulahamu komanso Mose ankalambira Mulungu woona ngati mmene Yesu ankachitira. (Genesis 24:27; Ekisodo 15:1, 2; Yohane 20:17) Sikuti Yehova ndi Mulungu wa mtundu umodzi wokha wa anthu, koma iye ndi Mulungu wa anthu okhala “padziko lonse lapansi.”—Salimo 47:2.
Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu lotchulidwa m’Baibulo ndipo dzinali ndi la iye yekha basi. (Ekisodo 3:15; Salimo 83:18) Dzinali analimasulira kuchokera ku mneni wa Chiheberi yemwe amatanthauza “kukhala,” ndipo akatswiri ambiri a Baibulo amanena kuti dzinali limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Tanthauzo limeneli limagwirizana bwino ndi udindo umene Yehova ali nawo monga Mlengi komanso Wokwaniritsa zolinga zake. (Yesaya 55:10, 11) Baibulo limatithandizanso kudziwa bwino makhalidwe a Yehova makamaka khalidwe lake lalikulu lomwe ndi chikondi.—Ekisodo 34:5-7; Luka 6:35; 1 Yohane 4:8.
M’Chingelezi, dzina lakuti Yehova linamasuliridwa kuchokera ku zilembo 4 za Chiheberi zoimira dzina la Mulungu יהוה (YHWH). Zilembozi zimatchedwa kuti Tetragrammaton. Ngakhale kuti sitidziwa mmene dzina la Mulungu ankalitchulira m’Chiheberi chakale, koma dzina lakuti “Yehova” linkadziwika kuyambira kalekale m’chinenero cha Chingelezi, ndipo linapezeka koyamba m’Baibulo lomasuliridwa ndi William Tyndale m’chaka cha 1530. a
N’chifukwa chiyani sitidziwa mmene ankatchulira dzina la Mulungu m’Chiheberi chakale?
Kale, Chiheberi ankachilemba pogwiritsa ntchito makonsonanti okha popanda mavawelo. Ndiye munthu akamawerenga Chiheberi ankatha kuikirira mavawelo oyenerera mosavuta. Komabe, Malemba Achiheberi (“Chipangano Chakale”) atamalizidwa kulembedwa, Ayuda ena anayamba kutsatira chikhulupiriro chabodza chokhudzana ndi zamizimu, chakuti n’kulakwa kutchula dzina lenileni la Mulungu. Akamawerenga mokweza lemba lomwe lili ndi dzina la Mulungu, ankaikapo dzina la udindo monga “Ambuye” kapena “Mulungu.” Pamene zaka zinkadutsa, chikhulupiriro chimenechi chinayamba kufalikira ndipo kenako anthu anasiya kutchula dzina la Mulungu mmene ankalitchulira kalelo. b
Anthu ena amaganiza kuti dzina la Mulungu linkatchulidwa kuti “Yahweh,” pamene ena amaona kuti linkatchulidwa m’njira zinanso zosiyanasiyana. Mumpukutu wa ku Nyanja Yakufa womwe uli ndi chigawo cha buku la Levitiko m’Chigiriki, anagwiritsa ntchito dzina lakuti Iao potengera mmene linalembedwera m’Chiheberi chakale. Olemba mabuku Achigiriki oyambirira amanenanso kuti dzinali linkatchulidwa kuti Iae, I·a·beʹ ndi I·a·ou·eʹ, koma palibe umboni wosonyeza kuti dzinali ankalitchuladi chonchi m’Chiheberi c chakale.
Maganizo olakwika okhudza dzina la Mulungu m’Baibulo
Maganizo olakwika: Mabaibulo omwe anamasulira dzina la Mulungu kuti “Yehova” anachita kuwonjezeramo dzinali.
Zoona zake: Zilembo 4 za Chiheberi zoimira dzina la Mulungu zimapezeka nthawi zokwanira 7,000 m’Baibulo. d Pa zifukwa zodziwa okha, omasulira Baibulo ambiri anasankha kuchotsa dzina la Mulungu n’kuikamo dzina la udindo monga “Ambuye.”
Maganizo olakwika: Mulungu Wamphamvuyonse safunikira kukhala ndi dzina lake lenileni.
Zoona zake: Mulungu anauza yekha anthu omwe ankalemba Baibulo kuti agwiritse ntchito dzina lake nthawi masauzande angapo ndipo amafuna kuti anthu omwe amamulambira nawonso azigwiritsa ntchito dzinali. (Yesaya 42:8; Yoweli 2:32; Malaki 3:16; Aroma 10:13) Ndipotu Mulungu anadzudzula aneneri onyenga omwe ankafuna kuchititsa anthu kuti aiwale dzina lake.—Yeremiya 23:27.
Maganizo olakwika: Potengera chikhalidwe cha Ayuda, dzina la Mulungu likuyenera kuchotsedwa m’Baibulo.
Zoona zake: N’zoona kuti alembi ena Achiyuda ankakana kutchula dzina la Mulungu. Ngakhale zili choncho, iwo sanachotse dzinali m’Mabaibulo awo. Mwa njira ina iliyonse, Mulungu safuna kuti tizitsatira miyambo ya anthu yomwe ndi yosemphana ndi malamulo ake.—Mateyu 15:1-3.
Maganizo olakwika: Dzina la Mulungu lisamagwiritsidwe ntchito m’Baibulo chifukwa sitikudziwa bwinobwino mmene ankalitchulira m’Chiheberi.
Zoona zake: Maganizo amenewa amasonyeza kuti Mulungu amayembekezera kuti anthu omwe amalankhula zinenero zosiyanasiyana azitchula dzina lake mofanana. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti atumiki a Mulungu amene ankalankhula zinenero zosiyanasiyana m’mbuyomu, ankatchula mayina amwinimwini mosiyanasiyana.
Chitsanzo pa nkhaniyi ndi dzina la woweruza wa ku Isiraeli, Yoswa. Pofuna kutchula dzina lake, Akhristu olankhula Chiheberi munthawi ya atumwi akanatha kutchula dzinali kuti Yehoh·shuʹa, pomwe olankhula Chigiriki akanalitchula kuti I·e·sous. Baibulo limasonyeza mmene dzina la Chiheberi la Yoswa analimasulira m’Chigiriki ndipo umenewu ndi umboni wakuti Akhristu ankatchula mayina amwinimwini mogwirizana ndi mmene anthu ambiri ankatchulira m’chinenero chawo pa nthawiyo.—Machitidwe 7:45; Aheberi 4:8.
Mfundo yomweyi ingagwirenso ntchito pomasulira dzina la Mulungu. Chofunika kwambiri si kutchula dzina la Mulungu ndendende mmene ankalitchulira, koma kuliika m’malo ake oyenerera m’Baibulo.
a Tyndale anagwiritsa ntchito dzina lakuti “Iehouah” pomasulira mabuku 5 oyambambirira a m’Baibulo. Patapita nthawi Chingelezi chinasintha ndipo dzina la Mulungu anayamba kulilemba mogwirizana ndi mmene anthu ankalankhulira pa nthawiyo. Mwachitsanzo, mu 1612, Henry Ainsworth anagwiritsa ntchito dzina lakuti “Iehovah” pomasulira buku lonse la Masalimo. Koma pamene ankakonzanso Baibuloli mu 1639, anagwiritsa ntchito dzina lakuti “Yehova.” Nawonso omasulira Baibulo la American Standard Version, anagwiritsa ntchito dzina lakuti “Yehova” m’malo onse amene dzina la Mulungu linkapezeka m’malemba a Chiheberi.
b Buku lina linati: “Nthawi ina Ukapolo utatha anthu anayamba kulemekeza kwambiri dzina lakuti Yahweh ndipo ankaopa kulitchula, m’malomwake anayamba kugwiritsa ntchito mawu akuti ADONAI kapena ELOHIM m’malo onse amene linkapezeka.”—The New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Volume 14, tsamba 883-884
c Kuti mumve zambiri onani Kabuku Kothandiza Kuphunzira mawu a Mulungu, pamutu wakuti: “Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi.”
d Onani Theological Lexicon of the Old Testament, Volume 2, tsamba 523-524.