Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mtsikana, cholengedwa chamoyo, akuyang’ana gulugufe, cholengedwa chamoyo china

Kodi Munthu Akamwalira Mzimu Wake Umapitirizabe Kukhala Ndi Moyo?

Kodi Munthu Akamwalira Mzimu Wake Umapitirizabe Kukhala Ndi Moyo?

Yankho la m’Baibulo

 M’Malemba Achiheberi, mawu achiheberi akuti ruʹach (luwaki) akupezeka maulendo 260 kuyambira pa Genesis 1:2. Mawuwa amatanthauza “mpweya umene munthu amatulutsa popuma,” koma alinso ndi matanthauzo ena kuwonjezera pamenepo. Matanthauzo onsewa akugwirizana pa mfundo imodzi iyi: Onse amanena za chinthu chosaoneka kwa anthu koma chimene chimasonyeza kuti pali mphamvu inayake imene ikugwira ntchito. Mphamvu yosaoneka imeneyo imatha kuchita zinthu zina zimene zimaoneka.

Adamu, cholengedwa chamoyo, pa nthawi imene ankalengedwa

Sikuti Adamu anapatsidwa moyo koma ‘anakhala wamoyo’

 M’Malemba Achigiriki, mawu achigiriki akuti pneuʹma (penevuma) akupezeka maulendo 334, kuyambira pa Mateyu 1:18, pamene pakupezeka mawu akuti “mzimu woyera.” Mawu amenewa ndi ofanana matanthauzo ndi mawu achiheberi aja akuti ruʹach.

 M’munsimu muli timitu tosiyanasiyana timene tikusonyeza malemba mmene mukupezeka mawu akuti ruʹach ndi pneuʹma.

 Mphepo

Ge 8:1; Eks 10:13; 1Mf 18:45; Yoh 3:8.

 Mzimu woyera, kapena Mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito

Ge 1:2; 41:38; Nu 11:25; Owe 6:34; 1Sa 19:20; 2Mb 24:20; Yes 11:2; Eze 11:5; Zek 4:6; Mt 1:18; 28:19; Mko 1:8; Lu 1:67; 2:27; Yoh 14:26; Mac 1:8; 2:33; Aro 5:5; 8:15, 16; 2Ak 13:14; Aef 3:16; 4:4; 1At 5:19; Tit 3:5; Yuda 20.

 Mphamvu ya moyo

Ge 6:17; Yob 27:3; 34:14; Sl 31:5; 146:4; Mla 3:19; 12:7; Yes 42:5; Lu 8:55; 23:46; Mac 7:59.

 Mulungu ndi mzimu, kapena wauzimu

Yoh 4:24; 2Ak 3:17; 3:18.

 Zolengedwa zauzimu

1Mf 22:21; Eze 3:12; 8:3; Mt 8:16; 10:1; Mko 3:11; 3:30; 1Ak 15:45; Ahe 1:7; 1Pe 3:18.

 Kudzipereka, mtima, ndi maganizo

Ge 45:27; Eks 35:21; Nu 14:24; Yob 17:1; Miy 25:28; Yes 57:15; Da 2:1; Lu 1:17; Yoh 11:33; 13:21; Mac 17:16; 1Ak 16:18; 2Ak 2:13; 7:13; 1At 5:23.

Kodi mzimu umapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira?

 Lemba la Salimo 104:29 limati: “[Inu Yehova] mukachotsa mzimu [ruʹach] wawo, zimafa, ndipo zimabwerera kufumbi.” Komanso lemba la Yakobo 2:26 limanena kuti ‘thupi lopanda mzimu [pneuʹma] limakhala lakufa.’ Choncho pa lemba limeneli, mawu akuti “mzimu” amatanthauza chimene chimachititsa kuti thupi likhale la moyo. Thupi likakhala lopanda mzimu, limakhala lakufa. M’Baibulo, mawu akuti ruʹach amamasuliridwa mosiyanasiyana. Nthawi zina amawamasulira kuti “mzimu” komanso “mpweya wa moyo,” kapena kuti mphamvu ya moyo. Mwachitsanzo, ponena za Chigumula cha nthawi ya Nowa, Mulungu anati: “Ndidzabweretsa chigumula chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo [ruʹach] m’thupi mwake.” (Genesis 6:17; 7:15, 22) Zimenezi zikusonyeza kuti “mzimu” ndi mphamvu yosaoneka (mphamvu ya moyo), imene imachititsa kuti zinthu zikhale ndi moyo.

Chitsanzo chothandiza kumvetsa nkhaniyi

 Thupi limafunikira mzimu kuti likhale ndi moyo, mofanana ndi mmene wailesi imafunikira magetsi kuti igwire ntchito. Taganizirani za wailesi ya mabatire. Mukaika mabatire muwailesi n’kuitsegula, mphamvu yochokera m’mabatirewo imapangitsa kuti wailesiyo iyambe kugwira ntchito. Koma popanda mabatire, wailesiyo imakhala yakufa, kapena kuti siingathe kugwira ntchito. N’chimodzimodzinso ndi wailesi yoyendera magetsi. Ngati mutazula nthambo yake kumagetsi, wailesiyo ingasiye kugwira ntchito. Mofanana ndi zimenezi, mzimu ndi mphamvu imene imapangitsa kuti thupi lathu likhale lamoyo. Ndipo mofanana ndi magetsi, mzimu ndi mphamvu chabe moti suumva kalikonse kapena kuganiza. Koma popanda mzimuwu, kapena kuti mphamvu ya moyo, matupi athu ‘amafa, ndipo timabwerera kufumbi.’—Salimo 104:29.

 Ponena za zimene zimachitika munthu akafa, lemba la Mlaliki 12:7 limati: “Fumbi [thupi la munthuyo] lidzabwerera kunthaka kumene linali, ndipo mzimu udzabwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka.” Mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo, ukatuluka m’thupi, thupilo limafa n’kubwerera kunthaka kumene linachokera. Nayonso mphamvu ya moyo imabwerera kwa mwiniwake amene anaipereka, yemwe ndi Mulungu. (Yobu 34:14, 15; Salmo 36:9) Zimenezi sizikutanthauza kuti mphamvu ya moyo imayendadi ulendo wopita kumwamba ayi. Koma zikutanthauza kuti munthu amene wamwalirayo kuti adzakhalenso ndi moyo m’tsogolo, zikudalira pa zimene Yehova Mulungu angachite. M’mawu ena, tingati moyo wake umakhala m’manja mwa Mulungu. Izi zili choncho chifukwa Mulungu yekha ndi amene ali ndi mphamvu yobwezeretsanso mzimu wa munthuyo kuti akhalenso ndi moyo.

Kodi chiphunzitso chakuti mzimu umapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira chinachokera kuti?

 Baibulo silimaphunzitsa kuti munthu akamwalira chinachake chimapitirizabe kukhala ndi moyo. Anthu anayamba kukhulupirira zimenezi chifukwa cha ziphunzitso zina zakale monga chiphunzitso cha Chigiriki chakale. Mulungu samafuna kuti anthu aziphatikiza ziphunzitso zake ndi ziphunzitso za anthu. Baibulo limatichenjeza kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”—Akolose 2:8.