TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YOBU
Yehova Anamuchotsera Ululu
Pamapeto pake onsewo anakhala chete ndipo n’kutheka kuti pankangomveka phokoso la kamphepo kayeziyezi kochokera kuchipululu cha Arabia. Yobu analibenso mawu oti angalankhule chifukwa anali atatoperatu ndi zomwe anakambirana ndi anzakewo. N’kutheka kuti Yobu ankayang’anitsitsa Elifazi, Bilidadi ndi Zofari mokwiya ndipo ankaoneka ngati akuwauza kuti ‘ngati ali ndi mawu anene.’ Koma anzakewo sankafuna kumuyang’ana n’komwe poona kuti mawu onyoza komanso opweteka omwe analankhula sanaphule kanthu. (Yobu 16:3) Ndipotu Yobu anali wokonzeka kusonyeza kuti akhalabe wokhulupirika.
Yobu ankaona kuti chinthu chomwe watsala nacho ndi kukhulupirika basi. Iye anali atasaukiratu, ana ake 10 anali atamwalira, anzake ankamunyoza komanso anali akudwala. Khungu lake linaderatu chifukwa cha zilonda, anali ndi zipsera thupi lonse ndipo ankatuluka mphutsi. Ndiponso mpweya umene ankatulutsa unali wonyansa. (Yobu 7:5; 19:17; 30:30) Ngakhale zinali choncho, anzakewo anamulankhula zinthu zokhumudwitsa kwambiri. Komabe Yobu anafuna kuwatsimikizira kuti sanali wochimwa ngati mmene iwowo ankanenera. Ndipo mawu omaliza omwe Yobu analankhula anawasowetsa chonena moti anangokhala chete. Komatu Yobu anali akumvabe ululu ndipo ankafunika kuthandizidwa mofulumira.
Yobu ankalephera kuganiza bwinobwino chifukwa cha zomwe zinkamuchitikira. Choncho pankafunika munthu wina woti amulangize komanso amuthandize. Yobu ankafunikanso kulimbikitsidwa komanso kutonthozedwa, zinthu zomwe anzake atatu aja analephera kumuchitira. Kodi nanunso munamvapo kuti mukufunika kulangizidwa komanso kulimbikitsidwa? Kodi munakhumudwitsidwapo ndi anthu amene munkawaona kuti ndi anzanu? Zimene Yehova Mulungu anachita pothandiza mtumiki wake Yobu komanso zimene Yobuyo anachita posonyeza kuti walandira thandizolo, zingakupatseni chiyembekezo ndipo zingakuthandizeni.
Mlangizi Wanzeru Komanso Wokoma Mtima
Nkhani ya Yobu imapitirira mochititsa chidwi. Panali munthu wina yemwe anali wamng’ono pa onsewo dzina lake Elihu. Iye ankangomvetsera zimene anzakewo ankakambirana koma sankasangalala nazo.
Elihu anakwiyira Yobu chifukwa choti Yobuyo analolera kusokonezedwa ndi anzake aja ndipo “ankanena kuti anali wolungama, osati Mulungu.” Komabe Elihu ankamumvera chisoni Yobu. Iye ankaona kuti Yobu akuvutika ndi ululu ndipo akufunika kulangizidwa mwachikondi komanso kulimbikitsidwa. Apa Elihu analephera kuugwira mtima. Iye anali atamva anzake atatuwo akumulankhula Yobu mawu opweteka komanso akukayikira za kukhulupirika kwake. Zinanso zomwe zinamukwiyitsa kwambiri ndi zomwe anthuwo analankhula zosonyeza kuti Mulungu ndi woipa. Zimenezi ndi zomwe zinachititsa kuti Elihu alankhulepo.—Yobu 32:2-4, 18.
Elihu ananena kuti: “Ine ndine wamng’ono ndipo amuna inu ndinu achikulire. N’chifukwa chake ndinabweza mawu anga ndipo ndinaopa kukuuzani zimene ndikudziwa.” Elihu ananenanso kuti: “Si anthu a masiku ambiri okha amene amakhala ndi nzeru, ndipo si okalamba okha amene amadziwa kuweruza.” (Yobu 32:6, 9) Pofuna kusonyeza kuti zimene ananenazi n’zoona, Elihu analankhula mawu ambiri. Iye analankhula zosiyana ndi zomwe Elifazi, Bilidadi ndi Zofari analankhula. Elihu anamutsimikizira Yobu kuti samulankhula zinthu zomwe zingamuwonjezere ululu. Anasonyezanso kuti amalemekeza Yobu pomutchula dzina, mosiyana ndi zomwe anzake atatu ena aja anachita. * Kenako Elihu anauza Yobu mwaulemu kuti: “Tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga.”—Yobu 33:1, 7; 34:7.
Elihu anapereka malangizo osapita m’mbali akuti: “Inu mwanena m’makutu anga, . . . ‘Ndine woyera, wopanda tchimo, ndilibe chondidetsa, ndilibe cholakwa. Mulungu amapeza ponditsutsira.’” Kenako Elihu anafotokoza vuto lomwe Yobu anali nalo, pomufunsa kuti: “Kodi mukuona ngati chimenechi n’chilungamo? Inuyo mwanena kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu.’” Apa Elihu anafuna kutsutsa maganizo olakwika omwe Yobu anali nawo. Ndiyeno anapitiriza kuti: “Pamenepa simunalondole.” (Yobu 33:8-12; 35:2) Elihu ankamvetsa kuti Yobu anakhumudwa chifukwa cha mavuto omwe anakumana nawo ndiponso chifukwa cha chipongwe chomwe anzake aja anamuchitira. Koma iye anachenjeza Yobu kuti: “Samalani kuti mkwiyo usakuchititseni kuwomba m’manja chifukwa cha njiru.”—Yobu 36:18.
Elihu Anafotokoza za Kukoma Mtima Kwa Yehova
Koposa zonse, Elihu ananena kuti Yehova Mulungu salakwitsa zinthu. Anafotokoza mwachidule mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe. . . Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.” (Yobu 34:10, 12) Elihu anathandiza Yobu kumvetsa kuti Yehova ndi wachifundo komanso wachilungamo, pomufotokozera kuti Yehova sanamupatse chilango ngakhale kuti analankhula mopanda ulemu. (Yobu 35:13-15) Ndipo pofuna kusonyeza kuti sankadziwa zonse zomwe zinkachititsa kuti Yobu azivutika, Elihu anasonyeza kudzichepetsa ponena kuti: “Mulungu ndi wokwezeka kuposa mmene tikudziwira.”—Yobu 36:26.
Ngakhale kuti Elihu anapereka malangizo osapita m’mbali, ankalankhula mokoma mtima. Anamufotokozera Yobu za chiyembekezo chosangalatsa chakuti Yehova adzabwezeretsa thanzi lake. Pa nthawiyo Mulungu adzauza mtumiki wake wokhulupirika kuti: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.” Koma Elihu anasonyezanso kukoma mtima m’njira ina. M’malo momangomuuza Yobu zochita, anamupempha kuti ayankhepo. Iye ananena kuti: “Lankhulani chifukwa ine ndakondwera ndi kulungama kwanu.” (Yobu 33:25, 32) Koma Yobu sanayankhe chilichonse. Mwina ankaona kuti palibe chifukwa choti adziikire kumbuyo chifukwa malangizowo anamuthandiza komanso kumulimbikitsa kwambiri. N’kuthekanso kuti analira chifukwa chodzimvera chisoni.
Tingaphunzire zambiri pa zimene amuna okhulupirikawa anachita. Kwa Elihu, tikuphunzira mmene tingaperekere malangizo komanso kulimbikitsa anthu omwe akufunika thandizo. Mnzathu weniweni amayenera kutichenjeza za zinthu zimene tikulakwitsa zomwe zingatigwetsere m’mavuto. (Miyambo 27:6) Ifenso timafunika kumachita zimenezi. Tizilankhula mokoma mtima komanso tizilimbikitsa anzathu ngakhale pamene akulankhula zinthu zolakwika. Ndipo ngati ifenso titafunika kulangizidwa, zimene Yobu anachita zingatithandize kukhala odzichepetsa n’kumvetsera malangizowo m’malo mongowanyalanyalaza. Tonsefe timafunika kulangizidwa komanso kuthandizidwa. Ndiye tikamvera, tikhoza kupulumutsa moyo wathu.—Miyambo 4:13.
“Kuchokera Mumphepo Yamkuntho”
Nthawi zambiri Elihu akamalankhula ankatchula zinthu monga mphepo, mitambo, mabingu ndi mphezi. Iye ananena zokhudza Yehova kuti: “Mvetserani mwatcheru kugunda kwa mawu a Mulungu.” Pasanapite nthawi anatchula za “mphepo yamkuntho.” (Yobu 37:2, 9) Zikuoneka kuti pa nthawi imene Elihu ankalankhula, mphepo inkawomba pang’onopang’ono ndipo kenako mphepoyo inayamba kuwomba mwamphamvu kwambiri. Ndiyeno panachitika zinthu zina zochititsa chidwi. Yehova analankhula.—Yobu 38:1.
Kodi mungamve bwanji Mlengi wachilengedwe chonse atakuitanani kuti akuphunzitseni zinthu zosiyanasiyana zokhudza chilengedwechi?
Tikamawerenga buku la Yobu, timasangalala kuona machaputala omwe muli nkhani zochititsa chidwi zimene Yehova analankhula ndi Yobu. Zinali ngati chimphepo chachilungamo chikusesa mawu opanda pake omwe Elifazi, Bilidadi ndi Zofari analankhula. Komabe Yehova sanalankhule chilichonse ndi amuna atatuwa kwa kanthawi. Cholinga chake chinali kuthandiza Yobu mtumiki wake ngati mmene bambo angalangizire mwana wake wokondedwa.
Yehova ankadziwa kuti Yobu akumva ululu. Ndipo ankamumvera chisoni monga mmene amachitira ndi mwana wake aliyense wokondedwa akamavutika. (Yesaya 63:9; Zekariya 2:8) Ankadziwanso kuti Yobu ankalankhula ‘mawu opanda nzeru,’ zomwe zinkangowonjezera mavuto ake. Choncho Yehova anafunsa Yobu mafunso ambiri omuthandiza kuganiza. Iye anayamba ndi mawu akuti, “Kodi unali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Ndiuze ngati uli womvetsa zinthu.” Pamene Mulungu anayamba kulenga zinthu, “nyenyezi za m’mawa” ndiponso ana onse a Mulungu zinafuula ndi chisangalalo. (Yobu 38:2, 4, 7) Komatu pa zonsezi, Yobu sankadziwa chilichonse.
Yehova anapitiriza kufotokozera Yobu za zinthu zomwe analenga. Zinali ngati Yehova akumuphunzitsa mwachidule zinthu zomwe masiku ano anthu amanena kuti ndi zasayansi. Zinthu zake zinali zokhudza nyenyezi, zamoyo, nthaka komanso mmene zinthu zinapangidwira. Kenako Yehova anafotokoza za nyama zosiyanasiyana zimene zinkapezeka m’dera limene Yobu ankakhala monga mkango, khwangwala, mbuzi za m’mapiri, mbidzi, njati, nthiwatiwa, hatchi, kabawi, chiwombankhanga, mvuwu komanso ng’ona. Kodi mungamve bwanji Mlengi wachilengedwe chonse atakuitanani kuti akuphunzitseni zinthu zosiyanasiyana zokhudza chilengedwechi? *
Anaphunzira Kukhala Wodzichepetsa Komanso Wachikondi
Kodi Yehova anachitiranji zimenezi? Ankafuna kuti Yobu aphunzire kudzichepetsa. Yobu ankadandaula poganiza kuti Yehova ndi amene akumuchitira zinthu mopanda chilungamo. Komatu zimenezi zinkangomuwonjezera ululu ndipo zikanachititsa kuti asokoneze ubwenzi wake ndi Atate wake wachikondi. Ndiyeno Yehova anamufunsa Yobu mobwerezabwereza ngati analipo pamene ankalenga zinthu zodabwitsa padzikoli. Anamufunsanso ngati angakwanitse kudyetsa komanso kusamalira zimene Mulunguyo analenga. Ngati Yobu sankadziwa chilichonse chokhudza chilengedwe, n’chifukwa chiyani ankaimba mlandu Mlengi? Kodi tinganene kuti Yobu ankadziwa zambiri kuposa Yehova?
Yobu sanatsutse zimene Yehova ananena kapena kupeza zifukwa zodziikira kumbuyo
Mawu onse omwe Yehova analankhula ankasonyeza kuti ankamukonda kwambiri Yobu. Zinali ngati Yehova akumuuza kuti: ‘Mwana wanga, ngati ndinalenga chilengedwechi ndipo ndimakwanitsa kuchisamalira, kodi ukuona kuti ndingalephere kukusamalira iweyo? Kodi ukuganiza kuti ndingakutaye, kukulanda ana ako kapenanso kulephera kuteteza moyo wako? Kodi si ineyo amene ndingakubwezere zinthu zonse zomwe unataya komanso kukuchotsera mavuto omwe ukukumana nawowa?’
Pa mafunso amene Yehova anafunsa, Yobu anangoyankhako kawiri kokha. M’malo motsutsa kapena kupeza zifukwa zodziikira kumbuyo, Yobu anazindikira kuti sadziwa zambiri ndipo anapepesa chifukwa cha zinthu zopanda pake zomwe analankhula. (Yobu 40:4, 5; 42:1-6) Pamenepatu Yobu anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Ngakhale kuti anapirira zinthu zambiri, anakhalabe wokhulupirika. Analandira malangizo a Yehova ndipo anawagwiritsa ntchito. Choncho aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wodzichepetsa moti ndikalandira malangizo ndimawagwiritsa ntchito?’ Tonsefe timafunika malangizo. Ndipo tikamawatsatira, timasonyeza kuti tikutsanzira Yobu.
“Inu Simunanene Zoona Za Ine”
Kenako Yehova anayamba kutonthoza Yobu. Iye anauza Elifazi amene anali wamkulu pa anzakewo kuti: “Mkwiyo wanga wayakira iweyo ndi anzako awiriwo chifukwa inu simunanene zoona za ine, monga wachitira Yobu mtumiki wanga.” (Yobu 42:7) Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti zonse zimene amuna atatu aja analankhula ndi zabodza, kapena zonse zomwe Yobu ananena zinali zoona? Ayi ndithu. * Komabe panali kusiyana kwakukulu pakati pa Yobu ndi anzakewo. Yobu anali wosweka mtima, wachisoni komanso wokhumudwa ndi zinthu zomwe anzakewo ankamunamizira. Mpake kuti nthawi zina ankalankhula zinthu zopanda pake. Koma Elifazi ndi anzake awiriwo sanakumanepo ndi mavuto ngati a Yobu. Iwo ankalankhula zinthu zopweteka mwadala chifukwa cha kunyada komanso chifukwa choti chikhulupiriro chawo chinali chochepa. Kuwonjezera pa kulimbana ndi Yobu, amunawa analankhula zinthu zosonyeza kuti Yehova, ndi Mulungu wankhanza komanso woipa kwambiri.
N’zosadabwitsa kuti Yehova analamula kuti amuna atatuwo apereke nsembe pa zomwe anachita. Anauzidwa kuti apereke nsembe ya ng’ombe 7 ndi nkhosa 7. Imeneyitu siinali nkhani yaing’ono. Tikutero chifukwa chakuti m’Chilamulo cha Mose, mkulu wa ansembe ndi amene ankayenera kupereka ng’ombe monga nsembe ngati wachita tchimo lomwe labweretsa mavuto kwa mtundu wonse. (Levitiko 4:3) M’chilamulocho, pa nyama zonse zomwe zinkaperekedwa nsembe, ng’ombe inali yodula kwambiri. Kuwonjezera pamenepa, Yehova ananena kuti alandira nsembe za amuna atatuwo pokhapokha Yobu atawapempherera. * (Yobu 42:8) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa kwambiri Yobu kuona kuti Mulungu amamuganizira ndiponso kuona kuti Yehovayo wachita zinthu mwachilungamo.
“Yobu mtumiki wanga akakupemphererani.”—Yobu 42:8
Yehova sanakayikire kuti Yobu achita zimene wauzidwa, kusonyeza kuti wakhululukira anzakewo ngakhale kuti anamukhumudwitsa kwambiri. Ndipo Yobu anachitadi zomwezo. (Yobu 42:9) Zimene Yobu anachita posonyeza kumvera unali umboni wamphamvu wakuti anali wokhulupirika Yehova. Ndipo zinachititsa kuti Yehova amudalitse kwambiri.
“Wachikondi Chachikulu”
Yehova anasonyeza kuti ndi “wachikondi chachikulu ndi wachifundo” kwa Yobu. (Yakobo 5:11) Iye anachiritsa Yobu. Taganizirani mmene Yobu anamvera atazindikira kuti mnofu wake wasalala “kuposa mmene unalili ali mnyamata” monga mmene Elifazi ananenera. Anthu a m’banja lake komanso anzake ankabwera kwa Yobu kudzamupepesa komanso kudzamupatsa mphatso. Yehova anamupatsanso chuma kuwirikiza kawiri kuposa chomwe anali nacho poyamba. Nanga bwanji za chinthu chopweteka kwambiri, chomwe ndi kumwalira kwa ana ake? Yobu ndi mkazi wake anasangalala kukhalanso ndi ana ena 10. Ndipotu Yehova anatalikitsa moyo wa Yobu modabwitsa moti anakhala ndi moyo kwa zaka zina 140. Yobu anaona mibadwo 4 ya ana ake ndipo nkhaniyi imanena kuti: “Pomalizira pake Yobu anamwalira ali wokalamba ndiponso wokhutira ndi masiku ake.” (Yobu 42:10-17) M’dziko latsopano, Yobu ndi mkazi wake wokondedwa adzakumananso ndi anthu a m’banja lake, kuphatikizapo ana ake 10 omwe anaphedwa ndi Satana.—Yohane 5:28, 29.
N’chifukwa chiyani Yehova anamudalitsa kwambiri Yobu? Baibulo limayankha kuti: “Munamva za kupirira kwa Yobu.” (Yakobo 5:11) Yobu anapirira mavuto ambiri kuposa amene enafe tingakumane nawo. Kuwonjezera pa kupirira mayesero, Yobu anakhalabe wokhulupirika ndipo sanasiye kukonda Yehova. M’malo mosunga zifukwa, iye anasonyeza kuti anali wokonzeka kukhululukira ena ngakhale anthu amene ankamukhumudwitsa mwadala. Yobu ankayembekezerabe kuti zinthu zidzayenda bwino ndipo anakhalabe ndi mtima wosagawanika.—Yobu 27:5.
Aliyense amafunika kupirira zinazake. N’zosakayikitsa kuti Satana amafunitsitsa kutifooketsa ngati mmene anachitira ndi Yobu. Koma tikakhalabe wokhulupirika, wodzichepetsa, wokonzeka kukhululukira ena komanso tikakhala ndi mtima wosagawanika, tikhoza kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wabwino m’tsogolo. (Aheberi 10:36) Satana amanyansidwa kwambiri akaona kuti tikukhalabe okhulupirika ngati Yobu koma Yehova amasangalala nazo kwambiri.
^ ndime 9 Zomwe Elifazi, Bilidadi ndi Zofari analankhula kwa Yobu zinali zambirimbiri moti zikhoza kupanga machaputala 9 a Baibulo. Komabe pa zonsezo, palibepo pomwe anatchula dzina la Yobu posonyeza kumulemekeza.
^ ndime 19 Nthawi zina, Yehova ankaphunzitsa Yobu pogwiritsa ntchito zinthu zodziwikiratu. Koma nthawi zina ankafotokoza zinthu mwandakatulo kapenanso mokuluwika. (Mwachitsanzo onani pa Yobu 41:1, 7, 8, 19-21) Ngakhale zinali choncho, cholinga cha Mulungu chinali choti amuthandize Yobu kuti apitirize kulemekeza komanso kuopa Mlengi wake.
^ ndime 25 Pofuna kusonyeza kuti zina zomwe Elifazi ananena ndi zoona, mtumwi Paulo anagwira mawu a Elifaziyo. (Yobu 5:13; 1 Akorinto 3:19) Zimene Elifazi ankanena zinali zoona ndithu, koma vuto ndi loti anazigwiritsa ntchito molakwika pothandiza Yobu.
^ ndime 26 Palibe pamene anafotokozapo kuti Yobu ankayenera kuperekera nsembe mkazi wake ngati mmene anzakewo anachitira.