Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mungatani Kuti Musamakwiye Mopitirira Malire?

Mungatani Kuti Musamakwiye Mopitirira Malire?

 Tiyerekeze kuti mwamuna kapena mkazi wanu walankhula kapena wachita zinazake zomwe sizinakusangalatseni koma inuyo mukuchita zinthu ngati kuti simunakhumudwe nazo. Kenako mnzanuyo akuzindikira kuti chinachake sichili bwino ndipo akukufunsani kuti adziwe chimene chalakwika. Zimenezi zikukupangitsani kuti mukwiye kwambiri. Zikafika pamenepa, mungatani kuti musamakwiye mopitirira malire?

 Zimene muyenera kudziwa

  •   Kukwiya kukhoza kuwononga thanzi lanu. Ochita kafukufuku anapeza kuti munthu akamangokhalira kukwiya amakhala pangozi yodwala matenda a kuthamanga kwa magazi, matenda a mtima, kuvutika maganizo komanso matenda ena a m’mimba. Nthawi zinanso anthu oterowo, angavutike ndi matenda a kusowa tulo, matenda a pakhungu, nkhawa komanso kufa ziwalo. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Usapse mtima.”​—Salimo 37:8.

  •   Kubisa mmene mukumvera kungakubweretsereninso mavuto. Kumangokhalira kusunga mkwiyo, kuli ngati matenda oopsa osaonekera. Zotsatira zake mungayambe kukayikira mwamuna kapena mkazi wanu komanso kumuganizira zolakwika. Zimenezi zingachititse kuti muzikhala osasangalala ndipo zingasokoneze kwambiri banja lanu.

 Zimene mungachite

  •   Muziona makhalidwe abwino a mkazi kapena mwamuna wanu. Lembani makhalidwe atatu a mnzanuyo omwe amakusangalatsani. Ndiyeno tsiku lina mukadzakwiya chifukwa cha zomwe mkazi kapena mwamuna wanuyo wachita, mudzaganizire makhalidwe munalembawo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamakwiye mopitirira malire.

     Lemba lothandiza: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”​—Akolose 3:15.

  •    Muziyesetsa kukhululukira mnzanuyo. Choyamba, muziganizira chifukwa chomwe chachititsa mnzanuyo kulankhula kapena kuchita zinthuzo. Izi zingakupangitseni kuti mukhale ndi mtima “omverana chisoni.” (1 Petulo 3:8) Kenako dzifunseni kuti, ‘Kodi pali chifukwa chomveka chomwe chachititsa kuti ndikwiye moti mpaka sindingakwanitse kukhululuka?’

     Lemba lothandiza: “Kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa [munthu] kukhala wokongola.”​—Miyambo 19:11.

  •    Muzikhala okoma mtima komanso aulemu pofotokoza mmene mukumvera. Mwachitsanzo, m’malo moloza chala mnzanuyo kuti, “Ndimaona kuti iweyo ulibe nane ntchito chifukwa ukachedwa kufika pakhomo siundiuza kuti uli kuti. Munganene kuti, “Nthawi ikatha usanafikebe pakhomo, ndimakudera nkhawa kwambiri?” Mukamafotokoza mmene mukumvera mofatsa zingakuthandizeni kuti musamakwiye mopitirira malire.

     Lemba lothandiza: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere.”​—Akolose 4:6.

  •    Muzimvetsera mwachidwi. Mukafotokoza za mumtima mwanu, muzipatsanso mpata mnzanuyo kuti afotokoze maganizo ake ndipo musamam’dule mawu. Akamaliza, muziyesa kuganiziranso zomwe wanenazo kuti muone ngati mwamvetsadi. Dziwani kuti kumvetsera zimene mnzanu akunena ndi njira imodzi yokuthandizirani kuti musamakwiye kwambiri.

     Lemba lothandiza: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.”​—Yakobo 1:19.