Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Baibulo limatithandiza kupeza mayankho a mafunso ovuta kwambiri amene tingafunse pa moyo wathu. Ndipo kwa zaka zambirimbiri, mfundo zimene zili m’Baibulo zakhala zikuthandiza anthu kwambiri. M’chigawo chino, mupeza mfundo zotsimikizira kuti Baibulo ndi lothandizadi.—2 Timoteyo 3:16, 17.
Zina Zimene Zilipo
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?
Kodi ineyo ndikuona kuti chimenechi ndi chipembedzodi cholondola?
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?
Kodi ineyo ndikuona kuti chimenechi ndi chipembedzodi cholondola?
Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova
Yambani Kuphunzira Baibulo
Phunzirani Baibulo kwaulere, mochita kukambirana ndi mphunzitsi wanu.
Pemphani Kuti Tidzakuyendereni
Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.
Zokuthandizani Pophunzira Baibulo
Sankhani zinthu zokuthandizani pophunzira Baibulo zimene zingapangitse kuphunzira kukhala kopindulitsa komanso kosangalatsa.
Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
Mtendere Komanso Moyo Wosangalala
Baibulo lathandiza anthu ambirimbiri kupirira mavuto, kuchepetsako nkhawa komanso kuthana ndi mavuto ena ndipo lawathandizanso kuona kuti moyo uli ndi cholinga.
Kukhulupirira Mulungu
Chikhulupiriro n’champhamvu kwambiri ndipo chimathandiza munthu kukhala ndi mtendere wam’maganizo panopa komanso chiyembekezo chodalirika cham’tsogolo.
Anthu Okwatirana Komanso Mabanja
Anthu okwatirana komanso mabanja amakumana ndi mavuto ambiri. Koma malangizo amene amachokera m’Baibulo angathandize kuti anthu a m’banja azigwirizana komanso azisangalala.
Mfundo Zothandiza Achinyamata
Onani mmene Baibulo lingathandizire achinyamata pa mavuto omwe amakumana nawo nthawi zambiri.
Zoti Ana Achite
Gwiritsani ntchito zinthu zosangalatsa zimenezi, nkhani zochokera m’Baibulo komanso makadi a anthu otchulidwa m’Baibulo pophunzitsa ana mfundo za m’Baibulo.
Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Werengani kuti mudziwe mayankho a m’Baibulo a mafunso osiyanasiyana okhudza Mulungu, Yesu, banja, mavuto ndi zinthu zina zambiri.
Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo
Dziwani tanthauzo lenileni la mavesi komanso mawu ena odziwika bwino a m’Baibulo.
Mbiri Komanso Baibulo
Werengani kuti mudziwe zimene zinachitika kuti Baibulo lifikebe mpaka nthawi yathu. Fufuzani umboni wosonyeza kuti ndi lolondola komanso lodalirika.
Baibulo Komanso Sayansi
Kodi Baibulo limagwirizana ndi zimene asayansi amaphunzitsa? Kuyerekezera zimene Baibulo limanena ndi zimene asayansi apeza kungatithandize kupeza yankho la funsoli.