Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 25, 2014
UNITED STATES

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko: A Mboni Anachita Msonkhano Wosaiwalika ku Sitediyamu Yotchedwa MetLife

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko: A Mboni Anachita Msonkhano Wosaiwalika ku Sitediyamu Yotchedwa MetLife

NEW YORK—Kuyambira pa June 20 mpaka 22 ndi pa June 27 mpaka 29, 2014, a Mboni za Yehova anadzazana mu sitediyamu ya MetLife kummawa kwa Rutherford mumzinda wa New Jersey. Iwo ankakamvetsera Msonkhano wawo wa Mayiko womwe unali ndi mutu wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Msonkhano wa pa June 20 mpaka 22 unali wa chingelezi ndipo wa pa June 27 mpaka 29 unali wa Chisipanishi.

Anthu amene anapezeka pamisonkhano yonseyi anakwana 118,000. Padutsa zaka zambiri kuti anthu ochuluka chonchi apezeke pamsonkhano ku New York. Anthu amene anamvera nkhani zina za msonkhanowu m’mizinda ina pogwiritsa ntchito telefoni ndi TV anakwana 407,000 ndipo zimenezi zinapangitsa kuti anthu onse amene anachita nawo msonkhanowu akwane 525,500.

M’nkhani zambiri za pa msonkhanowu ankachita zitsanzo komanso kuonetsa mavidiyo osonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo. Pa tsiku lililonse la msonkhanowu, nkhani yomaliza inkakambidwa ndi munthu wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. A David Splane omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani pa June 20 mpaka pa 22 ndipo a Geoffrey Jackson, omwenso ndi a m’Bungwe Lolamulira anakamba pa June 27 mpaka pa 29.

Panalinso anthu ambiri amene anabatizidwa. Anthu 1,255 anabatizidwa pa misonkhano imene inachitika ku sitediyamu ndipo anthu 2,930 anabatizidwa m’mizinda imene anamvera msonkhanowu patelefoni. Onse pamodzi anakwana 4,185.

Pamisonkhanoyi panali anthu ambiri ochokera m’mayiko ena monga ku Argentina, Australia, Belize, Britain, Chile, Costa Rica, El Salvador, Germany, Greece, Guatemala, Honduras, Italy, Malaysia, Mexico, Nicaragua, Panama, Peru, Spain, ndi Venezuela.

Bambo J. R. Brown omwe amalankhula moimira Mboni za Yehova ananena kuti; “Msonkhano umenewu unatikumbutsa msonkhano winanso wosaiwalika womwe unachitika mu 1958 ku New York. Msonkhano umenewo unachitikira mu sitediyamu ya Yankee ndi pabwalo la Polo ndipo anthu okwana 253,000 anapezeka pa misonkhanoyi. N’zodziwikiratu kuti a Mboni za Yehova, sadzaiwala misonkhano imene yachitika chaka chino mu sitediyamu ya MetLife.”

Mungalankhule ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000