25 JULY, 2017
UKRAINE
Akuluakulu a Boma ku Ukraine Anakaona Malo ku Ofesi ya Mboni za Yehova Patsiku Lapadera
LVIV, Ukraine— Ofesi ya Mboni za Yehova ku Ukraine inasankha tsiku lapadera kuti ilandire alendo ochokera m’madera osiyanasiyana odzaona malo. Tsikuli linali pa 2 May, 2017 ndipo panafika akuluakulu aboma, akatswiri azamaphunziro, abizinezi komanso anthu omwe amakhala moyandikana ndi ofesiyi mumzinda wa Lviv.
Ogwira ntchito pa ofesiyi anaonetsa alendowo zinthu zosiyanasiyana komanso anawaonetsa vidiyo yosonyeza ntchito zimene zimachitika pa ofesiyo. Anawaonetsanso malo amene amasungira zinthu zakale komanso malo ena omwe anakonzera ana. A Ivan Riher, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Ukraine anati: “Kano ndi koyamba kukhala ndi tsiku lapadera lolandira alendo kuchokera mu 2001. Anthu ambiri kuno ku Ukraine amatidziwa chifukwa cha ntchito yathu yolakira khomo ndi khomo kuphunzitsa anthu Baibulo. Koma lero ndi tsiku limene taitana anthu kuti adzaone mmene timagwirira ntchito zathu pa ofesi pano komanso zimene timachita pothandiza anthu a m’dera lathu.”
A Andriy Yurash omwe ndi mkulu wa bungwe loona za zipembedzo mu unduna woona zachikhalidwe ku Ukraine ananena kuti: “Zimene a Mboni za Yehova akuchita ndi zothandiza kwambiri kuti anthu a m’chipembedzo chimenechi komanso anthu ena azigwirizana.”
Chaka chino a Mboni za Yehova anakonzanso tsiku lapadera ngati limeneli ku ofesi yawo ya ku Cameroon komanso ku likulu lawo lapadziko lonse lomwe lili ku Warwick ku New York.
Lankhulani ndi:
International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000
Ukraine: Ivan Riher, +38-032-240-9323