Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

11 AUGUST, 2017
TAIWAN

Pulogalamu Yopereka Ntchito zina Kwa Anthu Okana Usilikali ku Taiwan Ikuyenda Bwino Kwambiri

Pulogalamu Yopereka Ntchito zina Kwa Anthu Okana Usilikali ku Taiwan Ikuyenda Bwino Kwambiri

Mu 2000, dziko la Taiwan linayamba kupereka mwayi woti athu okana usilikali azigwira ntchito zina za boma zosasemphana ndi zimene amakhulupirira. Potsatira pulogalamuyi anthu okana usilikali anapatsidwa mwayi wogwira ntchito m’zipatala, m’malo osungira anthu okalamba komanso m’maofesi ena a boma. Boma la Taiwan likupindula kwambiri ndi pulogalamuyi. Makamaka anthu omwe amakana usilikali ndi amene zikuwayendera bwino chifukwa panopa sakumangidwanso potsatira zomwe amakhulupirira.

Vidiyoyi ikufotokoza zimene boma la Taiwan linachita pokhazikitsa pulogalamuyi. Ikuyankhanso mafunso a akuluakulu a mayiko ena omwe saona kufunika kopereka mwayi woterewu kwa anthu okana usilikali. Onerani vidiyoyi kuti muone mmene pulogalamuyi yathandizira boma la Taiwan komanso anthu a m’dzikoli. A Kou-Enn Lin ndi mkulu wa ofesi yolemba anthu ntchito. A Lin ananena kuti: “Ndikukhulupirira kuti mayiko ena akhoza kuphunzirapo kanthu pa zimene boma lathu lachita.”