DECEMBER 21, 2018
SRI LANKA
Msonkhano Wapadera Woyamba Kuchitikira ku Sri Lanka
A Mboni za Yehova masauzande ambiri ochokera m’mayiko 7 anapita ku Sri Lanka kukachita nawo msonkhano wapadera womwe unali woyamba kuchitikira m’dzikolo. Msonkhano wapaderawu unali ndi mutu wakuti “Limbani Mtima” ndipo unachitika pa 6 mpaka 8 July, 2018 pa Sugathadasa National Sports Complex mumzinda wa Colombo womwe ndi likulu la dzikolo. Chiwerengero chapamwamba cha anthu omwe anapezeka pamsonkhanowu chinali 14,121. Panali zinthu zambiri zapadera zomwe zinachitika pamsonkhanowu monga nkhani zomwe m’bale wa m’Bungwe Lolamulira anakamba, anthu ambiri anabatizidwa kuposa pamisonkhano yonse ya m’mbuyomu, komanso abale ndi alongo anachereza alendo pafupifupi 3,500.
Ntchito yokonzekera msonkhanowu inayamba mu September 2017 mipingo ya ku Sri Lanka itadziwitsidwa kuti msonkhano wapadera udzachitika mu 2018. Kuwonjezera pa zinthu zomwe zinkafunika kuchitika pokonzekera msonkhanowu, sitediyamu nayonso inkafunika kukonzedwa komanso kuyeretsedwa. Ntchito yokonza sitediyamuyo inkaphatikizapo kupenta, kuchotsa zinyalala, kukonza mipando yowonongeka, komanso kukwirira maenje mu msewu. Kutatsala milungu itatu kuti msonkhanowu uyambe, a Mboni ambiri anafika kuti athandize nawo pa ntchito yokonza sitediyamuyo. Mmodzi mwa ogwira ntchito yoonetsetsa kuti pasitediyamuyo pali chitetezo, ananena kuti ogwira ntchito yokonza zinthu pasitediyamuyo zikanawatengera zaka 4 kuti agwire ntchito imene abale ndi alongo anagwira m’kanthawi kochepa.
Abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena anasangalalanso ndi kuona malo osiyanasiyana komanso zinthu zosiyanasiyana zosonyeza chikhalidwe cha ku Sri Lanka. Zinthu zosaiwalika zomwe zinachitika tsiku lina madzulo zinali kuvina magule komanso kuimba nyimbo zachikhalidwe, ndiponso panali gulu la achinyamata a Mboni omwe ankaimba nyimbo za Ufumu.
M’bale Ashley Ferdinands yemwe anaimira ofesi ya nthambi ku Sri Lanka anati: “Msonkhano wapaderawu unalidi mphatso kwa abale ndi alongo a m’dziko lino ndipo tikuona kuti unali mwayi wapadera kulandira alendo ambiri. Tikuyamikira kwambiri abale ndi alongo ambiri omwe anadzipereka kugwira ntchito zosiyanasiyana zomwe zathandiza kuti msonkhanowu uyende bwino. Komanso tikutamanda kwambiri Atate wathu wakumwamba yemwe amapereka mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.”—Yakobo 1:17.
Malo a msonkhanowu anagawidwa m’zigawo za ziyankhulo 4 zomwe ndi Chingelezi (m’chithunzichi), Chisinhala, Chinenero Chamanja cha ku Sri Lanka ndi Chitamiwu.
M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira ankakamba nkhani yomaliza tsiku lililonse.
Anthu 273 anabatizidwa pamsonkhanowu.
Abale anachititsa msonkhano wa atolankhani ku ofesi ya nthambi. Atolankhani oposa 40 anapezeka pamsonkhanowu ndipo kenako anawaonetsa malo osiyanasiyana pa ofesi ya nthambi.
M’bale woyankhula ndi atolankhani pamsonkhanowu akufunsidwa mafunso ndi atolankhani ochokera kunyumba ziwiri zoulutsira nkhani zomwe n’zodziwika bwino ku Sri Lanka.
Mu January 2018, abale ndi alongo oposa 700 anakumana ku Colombo kuti akaphunzire zoyenera kuchita pokonzekera msonkhano.
Abale ndi alongo odzipereka anakonza mipando yambiri yomwe inawonongeka pasitediyamu.
Ku Nyumba za Ufumu zambiri pafupi ndi komwe msonkhanowu unachitikira mumzinda wa Colombo, alendo ochokera m’mayiko ena anali ndi mwayi wodziwana ndi abale ndi alongo a ku Sri Lanka.
Akuvina komanso kuimba nyimbo zosiyanasiyana zosonyeza chikhalidwe cha ku Sri Lanka.
Gulu la a Mboni achinyamata likuimba nyimbo yamutu wakuti: “Yehova Akutipempha Kuti: ‘Mwana Wanga, Khala Wanzeru’”..
Alendo ochokera ku mayiko ena akuphunzira mmene tiyi amapangidwira.
Msonkhanowu utatha, alendo ananyamula zikwangwani zosonyeza kuti amakonda abale ndi alongo a ku Sri Lanka.