Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

RWANDA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Rwanda

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Rwanda

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Rwanda kuyambira mu 1970. Iwo analembetsa kukhala chipembedzo chovomerezeka mu 1992 koma boma linatsimikizira zimenezi mu 2002. A Mboni amadziwika kuti sachita zandale ndipo tingati ali ndi ufulu wochita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo. Iwo sanatenge nawo mbali pa nkhondo yomwe inayambika chifukwa chosiyana mitundu mu 1994 ndipo analolela kuika moyo wawo pangozi kuti apulumutse anthu ena. Komabe, anthu ena amasala a Mboni chifukwa choti sanasinthe maganizo awo ndipo sachita nawo zandale masiku ano.

Akuluakulu ena a sukulu amachotsa sukulu ana a Mboni akakana kuchita nawo miyambo yosonyeza kukonda dziko lawo komanso zochitika zina zachipembedzo. a Boma limafunanso kuti aphunzitsi azichita nawo maphunziro amene amaphatikizapo kuphunzira zausilikali komanso kuimba nyimbo yafuko. Chifukwa cha zimenezi, aphunzitsi ambiri omwe ndi a Mboni anachotsedwa ntchito. Mu 2010, boma la Rwanda linalamula kuti anthu onse ogwira ntchito m’boma achite nawo mwambo wina wolumbira ndipo ankagwiritsa ntchito mbendera ya dzikolo. Chifukwa cha zimenezi, a Mboni za Yehova ambiri omwe ankagwira ntchito m’boma anachotsedwa ntchito.

Ngakhale kuti pali mavuto amenewa, a Mboni za Yehova ku Rwanda akuyamikira chifukwa cha ufulu wopembedza umene ali nawo. Iwo akukhulupirira kuti nthawi ina akuluakulu a boma adzazindikira kuti a Mboni saopseza boma mwanjira iliyonse chifukwa chosachita nawo zandale.

a A Mboni za Yehova amaona kuti kuchita nawo miyambo yosonyeza kukonda kwambiri dziko lako ndi mwambo wachipembedzo komanso kuphwanya lamulo la Mulungu loti tizilambira iye yekha basi. Ngakhale kuti a Mboni sachita nawo miyambo ngati imeneyi, iwo amalemekeza ufulu umene ena ali nawo wochita nawo miyamboyi.