Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Pavel Chemrov

30 DECEMBER 2024
RUSSIA

“Yehova Akuona Zimene Zikundichitikira”

“Yehova Akuona Zimene Zikundichitikira”

Pa 26 December 2024, Khoti la Mzinda wa Nazarovo m’chigawo cha Krasnoyarsk linamanga M’bale Pavel Chemrov ndipo linagamula kuti kwa zaka zitatu, azitsatira malamulo enaake ali panyumba. M’baleyu sakufunika kupita kundende panopa.

Zokhudza M’baleyu

Mofanana ndi M’bale Chemrov, nafenso timalimbikitsidwa podziwa kuti Yehova ‘amationa’ ndipo adzatidalitsa tikamayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa iye.​—Yeremiya 12:3.