15 JULY, 2024
RUSSIA
M’bale Yevgeniy Sokolov Amuzenganso Mlandu Ndipo Amupeza Wolakwa
Pa 29 May 2024, Khoti la m’boma la Zeyskiy m’chigawo cha Amur, linapeza kuti M’bale Yevgeniy Sokolov ndi wolakwa ndipo linagamula kuti kwa zaka zitatu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo. M’baleyu sakufunika kupita kundende panopa.
Umenewu ndi mlandu wachiwiri womwe m’bale Sokolov anaimbidwa. Tikunena pano mlandu woyamba umene ukukhudzanso abale ena 9, ukuyendetsedwa mumzinda wa Voronezh komwe m’baleyu akukhala.
M’bale Sokolov anafotokoza chimene chimamuthandiza kupirira. Iye anati: “Ndikuphunzira kudalira kwambiri Yehova. Anthufe sitingathetse mavuto athu m’njira yabwino ngati mmene Yehova angachitire. Nthawi zonse iye amachita zinthu m’njira yabwino kwambiri komanso mwanzeru.”
Mofanana ndi M’bale Sokolov, tiyeni tipitirize kuuza Yehova kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako,” ndipo tisamakayikire kuti adzatithandiza pa nthawi yomwe tikufunika kuthandizidwa.—Salimo 142:5.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
15 December, 2022
Anatsegulira Yevgeniy mlandu wachiwiri mwiniwake asakudziwa
22 September, 2023
Yevgeniy anadziwa kuti amutsegulira mlandu. Anafunsidwa mafunso ndipo anamupeza ndi mlandu “wokonzekera komanso kuchititsa msonkhano wachipembedzo”
22 April, 2024
Anayamba kumuzenga mlandu
29 May, 2024
Anapezeka wolakwa ndipo anamugamula kuti kwa zaka zitatu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo