Zokhudza Kusunga Chinsinsi

Pofuna kukuthandizani kuti musamavutike kuchita zinthu pawebusaiti yathu, timagwiritsa ntchito ma cookies ndiponso njira zina zamakono zofanana ndi zimenezi. Ma cookies ena amathandiza kuti webusaiti yathu izigwira bwino ntchito ndipo sizingatheke kuwakana. Mukhoza kuvomereza kapena kukana ma cookies ena owonjezera, omwe cholinga chake ndi kungokuthandizani kuti musamavutike kuchita zinthu zina pawebusaiti. Sitidzagulitsa kapena kugwiritsa ntchito mauthenga amenewa pofuna kutsatsa malonda. Kuti mudziwe zambiri, werengani Ndondomeko ya Padziko Lonse ya Mmene Timagwiritsira Ntchito ma Cookies ndi Njira Zina Zamakono. Mukhoza kusintha ma settings nthawi ina iliyonse popita pa Zokhudza Kusunga Chinsinsi.

Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mkuntho wa Noru wachititsa kuti madzi asefukire dera lalikulu ku Philippines

6 OCTOBER, 2022
PHILIPPINES

Mphepo Yamkuntho ya Noru Yawononga ku Philippines

Mphepo Yamkuntho ya Noru Yawononga ku Philippines

Pa 25 September 2022, mphepo yamkuntho ya Noru yomwe anthu a m’dziko la Philippines amaitchulanso kuti Karding, inawomba pazilumba za Polillo m’chigawo cha Quezon. Pambuyo pake, mphepoyi inawombanso m’chigawo cha Aurora. Mphepoyi imathamanga pa liwilo la makilomita 195 pa ola limodzi. Mphepo yamkuntho ya Noru inawononga nyumba zambiri, misewu ndi mabuliji komanso inachititsa kuti madzi anasefukira dera lalikulu.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi

  • Mabanja 180 anasamuka m’nyumba zawo

  • Nyumba 209 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 20 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba 22 zinawonongekeratu

  • Nyumba za Ufumu 7 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Panakhazikitsidwa Makomiti Othandiza Pangozi Zamwadzidzidzi okwana awiri

  • Akulu a m’deralo akulimbikitsa mwauzimu mabanja okhudzidwa komanso kuwapatsa zinthu zofunikira

  • Ntchito zonse zopereka chithandizo, zikugwiridwa potsatira njira zodzitetezera ku COVID-19

Tipitirizabe kupempherera abale athu omwe akhudzidwa ndi mphepoyi pomwe akudalira Yehova kuti awateteze.—Salimo 57:1.