5 AUGUST, 2022
PHILIPPINES
Kumpoto kwa Dziko la Philippines Kwachitika Chivomerezi Choopsa
Pa 27 July 2022, chivomerezi champhamvu zokwana 7.0 chinachitika pachilumba cha Luzon ku Philippines. Dera la Abra ndi lomwe linakhudzidwa kwambiri. Mphamvu ya chivomezichi inafika ku Manila womwe ndi mtunda wamakilomita 400. Akatswiri anapeza kuti chivomerezichi chitachitika, panachitika tizivomerezi tinanso tokwana 2,000.
Mmene Zinakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Palibe m’bale kapena mlongo wathu aliyense amene anafa pa tsokali
Ofalitsa 4 anavulala pang’ono
Mabanja 42 anasamutsidwa
Nyumba 63 zinawonongeka pang’ono
Nyumba imodzi inawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 13 zinawonongeka
Ntchito Yopereka Chithandizo
Panakhazikitsidwa Komiti Yothandiza pa Ngozi Zamwadzidzidzi kuti iyang’anire ntchito yopereka chithandizo
Akulu a m’deralo akuchititsa maulendo aubusa kwa onse omwe anakhudzidwa
Ntchito zonse zopereka chithandizo zikugwiridwa potsatira njira zodzitetezera ku COVID-19
Mwamsanga, ofesi ya nthambi inatumiza chithandizo kwa abale ndi alongo omwe ali m’madera okhudzidwa komanso anawapezera malo okhala ongoyembekezera. Abale ndi alongo a m’maderawa akumathandizana ngakhale kuti nawonso anakhudzidwa ndi chivomerezichi.
Tili ndi chikhulupiriro champhamvu kuti Yehova athandiza abale ndi alongo athu pa nthawi yovutayi.—Salimo 50:15.