NOVEMBER 4, 2015
MEXICO
Boma Linathokoza a Mboni Chifukwa Chophunzitsa Akaidi ku Mexico
Akuluakulu a boma kudera la Baja California, m’dziko la Mexico, anapereka chikalata chothokoza a Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa Baibulo m’ndende. Anthu amene anasaina chikalatachi anali nduna yoona za chitetezo ndiponso nduna yoona zakundende.
M’chikalata chimenechi anati: “Nduna yoona za chitetezo yoimira boma ikuthokoza Mboni za Yehova chifukwa chothandiza anthu a ku Baja California modzipereka kuti azikhala ndi moyo wabwino komanso kuti akaidi azitha kuchita zinthu bwinobwino akadzachoka m’ndende.”
A Mboni za Yehova amayendera ndende za ku Baja California pothandiza akaidi. Kuyambira mu 1991, akhala akuyenderanso ndende ina yamumzinda wa Mexicali chifukwa choti mkaidi wina anawapempha kuti azimuphunzitsa Baibulo. Munthu wina amene amayang’anira malo ena a mumzindawu othandiza akaidi kuti asinthe khalidwe lawo, anauza a Mboni kuti: ‘Mukabwera kudzaphunzitsa akaidi mumawathandiza kuona kuti nawonso ndi anthu. Amaonanso kuti ndi ofunika chifukwa nthawi ikadzakwana, adzatuluka m’ndende n’kumakagwira ntchito zothandiza kuti zinthu ziziyenda bwino m’dzikoli. Ndikuthokoza kwambiri thandizo lanuli.’
Munthu wina wolankhulira Mboni za Yehova ku Mexico anati: “Ntchito yaikulu ya Mboni za Yehova ndi yothandiza anthu, kuphatikizapo akaidi, kuti adziwe zimene Baibulo limaphunzitsa. Mpingo wina wa Mboni za Yehova ku Mexicali unanena kuti anthu osachepera 8 anabatizidwa n’kukhala a Mboni ali m’ndende ya ku Mexicali. Timaona kuti anthu onse ayenera kukhala ndi mwayi wophunzira Baibulo.”
Lankhulani ndi:
Kumayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048