NOVEMBER 7, 2018
JAPAN
A Mboni Anathandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa Ndi Kusefukira Kwa Madzi ku Japan
Mu July 2018 abale ndi alongo athu oposa 47,000 omwe amakhala m’madera a kumadzulo kwa dziko la Japan anakhudzidwa kwambiri ndi kusefukira kwa madzi. Zimenezi zitangochitika, anthu 4,900 ongodzipereka anayamba kuyeretsa komanso kukonza nyumba za a Mboni ndi Nyumba za Ufumu zomwe zinawonongeka.
Abale ndi alongo athu anayeretsa komanso kukonza Nyumba za Ufumu 9 zomwe zinawonongeka ndi madzi osefukirawo, ndipo ntchitoyi inayendetsedwa ndi Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi atatu. Komanso Nyumba ya Ufumu ina ili mkati mokonzedwa. Kuwonjezera pamenepo, nyumba 184 za a Mboni zakonzedwa, ndipo zinanso 11 zikonzedwa chaka chino chisanathe.
Banja la a Taro ndi a Keiko Abe omwe ali ndi ana atatu ndipo amakhala ku Ehime, ndi limodzi mwa mabanja omwe analandira chithandizo. Pambuyo pa masiku atatu m’nyumba ya banjali mutadzadza madzi, abale a m’dera lawo anafika n’kuyamba kukonza nyumbayo, ndipo ntchitoyo inaphatikizapo kukonza pansi pa nyumbayo. Kuwonjezera pamenepo, abale a m’derali anapereka mabedi atsopano ku banjali komanso madesiki oti ana azigwiritsa ntchito.
M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira, yemwe pa nthawiyi anali kale ku Japan, anakamba nkhani yolimbikitsa pamsonkhano wapadera womwe unachitikira mu Nyumba ya Ufumu ku Okayama pa 20 September, 2018. Abale ndi alongo onse omwe anamvetsera nkhaniyi analipo 36,691 ndipo ena mwa abalewa ndi amene anakhudzidwa ndi mphepo zamkuntho komanso zivomezi zomwe zinachitika pa nthawi yomwe madziwa anasefukira. M’bale Jackson anapezanso nthawi yocheza ndi anthu osiyanasiyana omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukirawa n’cholinga chofuna kuwalimbikitsa.
Tonsefe limodzi ndi abale ndi alongo athu a ku Japan timayamikira kuti tili m’gulu la Yehova lomwe limasonyeza chikondi potengera Atate wathu wakumwamba.—2 Akorinto 1:3, 4.