OCTOBER 14, 2014
GEORGIA
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula Mlandu Motsatira Malamulo ku Georgia
Pa October 7, 2014, khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula mlandu mokomera a Mboni za Yehova ku Georgia. Mlanduwu unali wa pakati pa boma la Georgia ndi a Begheluri komanso anthu ena (Begheluri and Others v. Georgia) ndipo unapititsidwa kukhotili zaka zoposa 12 zapitazo. Mlanduwu unkakhudza anthu 99 omwe anakhala akuchitidwa nkhanza m’njira zosiyanasiyana komanso kuopsezedwa maulendo 30. Pa anthu 99 odandaulawo, ndi munthu mmodzi yekha amene sanali wa Mboni za Yehova. Apolisi a m’dzikoli ankachitira nkhanza a Mboni za Yehova m’njira zosiyanasiyana monga kusokoneza misonkhano yawo, kuwachitira nkhanza m’nyumba zawo, m’makhoti komanso m’misewu.
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapeza kuti anthu odandaulawo anakadandaulapo ku boma maulendo pafupifupi 160. Khotili linapezanso kuti apolisi komanso akuluakulu ena a boma ankachita nawo zinthu zankhanzazi. N’zomvetsa chisoni kuti zinthu sizinasinthe ngakhale kuti anthuwo anakadandaula ku boma kambirimbiri. Chifukwa chakuti boma la Georgia silinalange anthu olakwawo, iwo anapitirizabe kuchitira nkhanza Mboni za Yehova.
Mwachitsanzo, pa September 8, 2000 a Mboni za Yehova okwana 700 anasonkhana mumzinda wa Zugdidi kuti achite msonkhano. Koma mwadzidzidzi, pamalowa panafika gulu la apolisi omwe anavala zinthu zobisa nkhope zawo kuti anthu asawazindikire. Apolisiwo anatentha nyumba yomwe amachitira msonkhanowo komanso anamenya anthu pafupifupi 50. Nthawi yomweyo, a Mboniwo anakadandaula ku boma za nkhaniyi. Koma akuluakulu a bomawo anakana kuimba mlandu apolisiwo moti a Mboniwo anangowasiya manja ali m’nkhosi.
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Ladzudzula Boma la Georgia Chifukwa Chosathandiza a Mboni Moyenera
Mu 2002, a Mboni za Yehova amene anachitidwa zinthu zankhanzawo anapititsa nkhaniyi ku Khoti Loona za ufulu wa Anthu ku Ulaya. Iwo anachita izi poona kuti akuluakulu a boma m’dzikoli sanafufuze nkhaniyi mokwanira komanso anthu olakwawo sanalandire chilango.
Pa chigamulo chimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka pa October 7 2014, linanena kuti “akuluakulu a boma la Georgia sankalanga anthu opalamula. Izi zinachititsa kuti anthu a Mboni za Yehova azizunzidwa m’dziko lonselo.” Khotili linanenanso kuti “anthuwo amachitira nkhanza Mboni za Yehova chifukwa cha tsankho.” Linatinso “akuluakulu abomawo anali ndi maganizo atsankho . . . , ndipo n’chifukwa chake sanapereke chilango kwa anthu ochita zachiwawawo.”
“Akuluakulu a boma a ku Georgia sankalanga anthu opalamula, ndipo izi zinachititsa kuti anthu a Mboni za Yehova azizunzidwa m’dziko lonselo.”
— Begheluri and Others v. Georgia, no. 28490/02, 7 October 2014, p. 40, par. 145
Khotili linapeza kuti akuluakulu a boma la Georgia ndi olakwa chifukwa anazunza anthu 47 mwa odandaulawo komanso kuti anthu 88 anawaphwanyira ufulu wawo wolambira. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linauza boma la Georgia kuti “lisiye kuchita nkhanza zoterezi komanso kuti likonze zinthu zomwe zinawonongeka chifukwa chakuti bomali linalekerera zinthu komanso kuti linali ndi mtima watsankho. Khotili linalamulanso boma la Georgia kuti lipereke ndalama za chipukuta misozi zokwana mayulo 45,000 kwa anthu olakwiridwawo.
Zinthu Zina Zayamba Kuyenda Bwino
Kuyambira mu 2004, akuluakulu a boma ku Georgia ayesetsa kukonza zinthu kuti a Mboni za Yehova azikhala mwamtendere m’dzikoli. Komabe, nthawi zina a Mboni za Yehova akumachitidwabe nkhanza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mu 2013, a Mboni za Yehova anachitidwa zinthu zankhanza maulendo 53. Pogamula mlandu wa a Begheluri uja, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lija linauza boma la Georgia kuti lizifufuza mwansanga nkhani zokhudza nkhanza zomwe mzika za m’dzikoli zingachitiridwe. A Mboni za Yehova akukhulupirira kuti boma la Georgia liyesetsa kufufuza nkhaniyi. Akukhulupiriranso kuti bomali lipereka chilango mosakondera kwa anthu onse opezeka olakwa pa mlandu wochitira nkhanza anthu chifukwa cha chipembedzo chawo.