Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Ndinkakonda Kwambiri Karati”

“Ndinkakonda Kwambiri Karati”
  • Chaka Chobadwa: 1962

  • Dziko: United States

  • Poyamba: Ankakonda kwambiri karati

KALE LANGA

 Mnzangayo anavulala kwambiri kusiyana ndi mmene ndinkaganizira. Ndinamumenya mwangozi pamphuno. Ndinadziimba mlandu kwambiri moti ndinayamba kuganiza zosiya karati. N’chifukwa chiyani zimenezi zinandichititsa kuganiza zosiya masewera amene ndinkawakonda kwambiriwa? Ndisanayankhe funso limeneli, ndikufotokozereni kaye zimene zinachitika kuti ndiyambe karati.

 Ndinakulira mumzinda wa Buffalo, ku New York, m’dziko la U.S.A. Banja lathu linali losangalala ndipo tinali Akatolika odzipereka kwambiri. Ndinaphunzirapo m’sukulu zosiyanasiyana za Katolika ndipo ndikapita kutchalitchi ndinkathandizira wansembe. Makolo anga ankafuna kuti ineyo ndi mchemwali wanga tidzakhale ndi tsogolo labwino. Choncho ankandilola kuti ndikaweruka kusukulu ndizichita masewera osiyanasiyana kapena kugwira timaganyu, bola ngati ndikukhoza bwino kusukulu. Zimenezi zinandithandiza kuti ndikhale munthu wodalirika kuyambira ndili wamng’ono.

 Ndili ndi zaka 17, ndinayamba kuphunzira karati. Kwa zaka zambiri ndinkaphunzira masewerawa masiku 6 pamlungu ndipo ndinkachita zimenezi kwa maola atatu patsiku. Mlungu uliwonse, ndinkathera maola ambirimbiri ndikuganizira za njira zosiyanasiyana zomwe ndingamenyere munthu komanso ndinkaonera mavidiyo omwe angandithandize kuwonjezera luso langa. Ndinkasangalala kuyeserera masewerawa nditaphimba kunkhope ndipo ndinkachita zimenezi ngakhale ndikugwiritsa ntchito zida. Ndinkatha kuphwanya matabwa kapena njerwa pongozimenya ndi chibakera chimodzi chokha. Kenako ndinadzakhala katswiri wamasewerawa ndipo ndinawinapo zikho pamipikisano yosiyanasiyana. Ndinkaona kuti karati ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga.

 Ndinkaona kuti ndapeza zonse zomwe ndinkafuna pa moyo wanga. Ndinachita maphunziro akuyunivesite ndipo ndinakhoza bwino kwambiri. Kenako ndinayamba kugwira ntchito pakampani ina yaikulu ngati injiniya wa zamakompyuta. Kampaniyi inkandichitira chilichonse. Ndinalinso ndi nyumba yangayanga ndiponso ndinali ndi chibwenzi. Ngakhale zinthu zinkaoneka ngati zikundiyendera bwino, sindinkasangalala chifukwa ndinali ndi mafunso ambiri omwe sindinkapeza mayankho ake.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Pofuna kupeza mayankho a mafunsowa, ndinayamba kupita kutchalitchi kawiri pamlungu komanso kupemphera kwa Mulungu kuti andithandize. Koma zomwe ndinakambirana ndi mnzanga winawake tsiku lina, zinasintha moyo wanga. Ndinamufunsa kuti: “Kodi unayamba waganizirapo kuti cholinga cha moyo ndi chiyani? Ndikutero chifukwa chakuti padzikoli pali mavuto ambiri komanso pakuchitika zinthu zambiri zopanda chilungamo.” Iye anandiuza kuti nayenso anadzifunsapo mafunso amenewo ndipo anapeza mayankho ogwira mtima kuchokera m’Baibulo. Kenako anandipatsa buku la mutu wakuti, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. a Anandifotokozera kuti wakhala akuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Poyamba sindinkafuna kuliwerenga chifukwa ndinkaona kuti sindiyenera kuwerenga mabuku azipembedzo zina. Komabe, chifukwa choti ndinkafunitsitsa kupeza mayankho a mafunso anga aja ndinayamba kuona kuti ndingachite bwino kuona ngati zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa zili zomveka.

 Ndinadabwa kwambiri kudziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndinaphunzira kuti cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga anthu chinali choti akhale padzikoli m’paradaiso mpaka kalekale ndipo cholinga chimenecho sichinasinthe. (Genesis 1:28) Nditaona kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova likupezeka m’Baibulo langa la King James, ndinadabwa kwambiri chifukwa sindinkalidziwa n’komwe ngakhale kuti m’Pemphero la Ambuye, lomwe ndinaliloweza pamtima, ndinkapemphera kuti liyeretsedwe. (Salimo 83:18; Mateyu 6:9) Komanso ndinamvetsa chifukwa chake Mulungu walola kuti anthu azivutika. Zonse zomwe ndinkaphunzira zinali zomveka moti ndinasangalala kwambiri.

 Sindidzaiwala mmene ndinamvera nditafika koyamba pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Anthu ake anali ochezeka kwambiri ndipo aliyense ankafuna kudziwa dzina langa. Pa tsikulo kunakambidwa nkhani ya onse yokhudza mapemphero amene Mulungu amamva. Nkhani imeneyi inandisangalatsa kwambiri chifukwa ndinkapemphera kuti Mulungu andithandize. Ulendo wina umene ndinakasonkhana ndi a Mboni za Yehova ndi pa nthawi ya Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Pa maulendo awiri onsewa, ndinadabwa kwambiri kuona kuti ngakhale ana ankatsatira m’Mabaibulo awo pamene malemba ankawerengedwa. Poyamba zinkandivuta kupeza malemba m’Baibulo, koma a Mboni za Yehova anandithandiza kudziwa mmene ndingamawapezere mosavuta.

 Pamene ndinkapitiriza kusonkhana, ndinayamba kuona kuti zimene a Mboni za Yehova amaphunzira ndi zabwino kwambiri. Nthawi iliyonse imene ndasonkhana ndinkaphunzira zambiri ndipo ndinkachokako nditalimbikitsidwa komanso ndili wosangalala. Kenako a Mboni anandipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo.

 Ndinaona kuti zomwe a Mboni za Yehova ankachita zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe zinkachitika kutchalitchi kwathu. A Mboni za Yehova ndi anthu ogwirizana komanso ochita zinthu moona mtima ndipo amayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu. Ndinazindikira kuti chikondi chimene amasonyezana ndi chizindikiro cha Akhristu enieni.—Yohane 13:35.

 Nditapitiriza kuphunzira Baibulo ndinasintha zinthu zambiri pa moyo wanga kuti zigwirizane ndi mfundo za m’Baibulo. Komabe, ndinkaona kuti sindingasiye kuchita masewera a karati. Ndinkakonda kuphunzira karati komanso kuchita nawo mipikisano. Nditafotokozera zimenezi munthu amene ankandiphunzitsa Baibulo, iye anandiuza kuti, “Ungopitiriza kuphunzira, sindikukayikira kuti udzasankha mwanzeru.” Zimene anandiuzazi zinandilimbikitsa kwambiri. Pamene ndinkapitiriza kuphunzira m’pamenenso ndinkafunitsitsa kuchita zinthu zomwe zingasangalatse Yehova Mulungu.

 Zimene ndinachita pomenya mwangozi mnzanga amene ndamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi, n’zomwe zinachititsa kuti ndisinthe kwambiri moyo wanga. Ngozi imeneyi inachititsa kuti ndiyambe kuona kuti sizingatheke kuti ndikhale wotsatira wa Khristu wamtendere kwinaku ndikupitiriza kusewera karati. Ndinali nditaphunzira zimene Baibulo linaneneratu pa Yesaya 2:3, 4, zakuti anthu amene amatsatira malangizo ochokera kwa Yehova “sadzaphunziranso nkhondo.” Komanso Yesu ankaphunzitsa anthu kuti asamabwezere, ngakhale pamene ena akuwachitira zinthu zopanda chilungamo. (Mateyu 26:52) Choncho ndinasankha kusiya masewera a karati ngakhale kuti ndinkawakonda kwambiri.

 Kenako ndinayamba kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti, “Ukhale ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.” (1 Timoteyo 4:7) Nthawi yomwe ndinkaigwiritsa ntchito pochita masewera a karati, ndinayamba kuigwiritsa ntchito polimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu komanso kumutumikira. Mkazi yemwe ndinali naye pachibwenzi uja sanagwirizane ndi zimene ndinkaphunzira m’Baibulo, choncho tinasiyana. Pa 24 January, 1987, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Patangopita nthawi yochepa, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse, womwe ndi ntchito yongodzipereka yophunzitsa anthu Baibulo. Kungochokera nthawi imeneyo, ndakhala ndikuchita utumiki wa nthawi zonse ndipo nthawi zina ndimathandizira kulikulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova ku New York, U.S.A.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Panopa ndikukhala moyo wosangalala kwambiri chifukwa ndinadziwa zolondola zokhudza Mulungu. Ndikukhala moyo wabwino kwambiri ndipo ndikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. Ndimakonda kuchita masewera olimbitsa thupi, koma sikuti zimenezi ndi zofunika kwambiri pa moyo wanga. Cholinga changa chachikulu ndi kutumikira Yehova Mulungu.

 Pa nthawi imene ndinkachita masewera a karati, ndinkakhala tcheru ndi anthu amene andiyandikira ndipo ndinkangoganizira mmene ndingadzitetezere ngati winawake atandiukira. Koma panopa ndimakhala tcheru ndi anthu amene andiyandikira n’cholinga choti ndiwathandize. Baibulo landithandiza kuti ndikhale munthu wopatsa komanso kuti ndikhale mwamuna wabwino kwa mkazi wanga wokongola, Brenda.

 Poyamba ndinkakonda kwambiri masewera a karati. Koma m’malo mwa karati, panopa ndimachita zinthu zina zabwino kwambiri. Baibulo ndi limene lingafotokoze bwino zimene ndikutanthauza. Limati: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono, koma kukhala wodzipereka kwa Mulungu n’kopindulitsa m’zonse, chifukwa kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwerawo.”—1 Timoteyo 4:8.

a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma linasiya kusindikizidwa.