Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Warwick Gawo 5 (Kuyambira September 2015 Mpaka February 2016)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Warwick Gawo 5 (Kuyambira September 2015 Mpaka February 2016)

Zithunzi izi zikusonyeza mmene ntchito yomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova yapitira patsogolo komanso mmene antchito ongodzipereka anathandizira ntchito yomangayi kuyambira mu September 2015 mpaka February 2016.

Chithunzi chosonyeza mmene likulu la ku Warwick lizidzaonekera. Kuyambira kumanzere kupita kumanja:

  1. Galaja

  2. Poimika Magalimoto a Alendo

  3. Nyumba Yokonzerako Zinthu Komanso Koimika Magalimoto

  4. Nyumba Yogona B

  5. Nyumba Yogona D

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona A

  8. Maofesi

7 October, 2015​—Ku Warwick

Akunyamula konkire yopangira mlatho ndipo akupita nayo pamalo ena omwe amakhala achinyezi kwambiri. Matayala a galimoto ndi amene anagwiritsidwa ntchito poteteza konkireyi kuti isasweke itangotsitsidwa m’galimoto. Mlathowu umagwiritsidwa ntchito pamalo achinyezi omwe amakhala ovuta kudutsapo.

13 October, 2015​—Maofesi

Denga lomwe adzalapo mtundu wina wake wa zomera zobiriwira zomwe zimakhala ndi masamba ochindikala ndipo zimasintha mtundu zisanasiye kukula m’nyengo yozizira. Pa dengali pali mitundu yosiyanasiyana yokwana 16 ya mtundu umenewu wa zomera. Denga lokhala ndi zomera, zomwe zimathandiza kuchepetsa mphamvu ya madzi a mvula, limachepetsanso ndalama zimene zimaonongeka zolipilira magetsi ndipo zimangofuna kuchotsamo udzu wosafunika kuti zipitirize kukula bwino.

13 October, 2015​—Nyumba Yogona D

Kalipentala akuika kathabwa pakati pa khoma ndi kabati m’khitchini. Pofika kumapeto kwa mwezi wa February 2016, ogwira ntchito m’dipatimenti ya ukalipentala anali ataika makabati opitirira hafu ya makabati onse ofunika m’makhitchini.

16 October, 2015​—Maofesi

Ogwira ntchito zamagetsi akuika nyale zoti usiku ziziwalitsa chizindikiro cha Watch Tower chomwe chili pansanja.

21 October, 2015​—Maofesi

Maofesi, nsanja komanso chipata cha pamalo olandirira alendo zikuwala usiku. Alendo azidzati akaima pa nsanjayi azidzatha kuona mosavuta malowa komanso zinthu zina zomwe zili pafupi.

22 October, 2015​—Ku Warwick

Ogwira ntchito akuthira konkire pamsewu wa magalimoto othandiza pakachitika ngozi. Masaka a chiguduli omwe akuoneka cha ku tsogolowo amathandiza kuti zinthu monga dothi komanso miyala zisamagwe pa nthawi yomanga.

9 November, 2015​—Maofesi

Ogwira ntchito akuika denga loonekera mkati pa malo olandirira alendo. Maofesiwa ali ndi madenga okwana 11 a mtunduwu ndipo amathandiza kuti kuwala kwa dzuwa kuzitha kulowa mkati.

16 November, 2015​—Nyumba Yokonzera Zinthu Komanso Koimika Magalimoto

Wogwira ntchito yowotcherera zinthu akudula paipi yoti akagwiritse ntchito pa chipangizo choziziritsira madzi. Akudula paipiyi pogwiritsa ntchito moto wa gasi.

30 November, 2015​—Maofesi

Kalipentala akuika thabwa loyamba pa windo. Akatsimikiza kuti thabwali silinapendekeke komanso akamanga khoma, adzaikanso thabwa lina pa windoli.

17 December, 2015​—Ku Warwick

M’munsi mwa chithunzichi, katapila akuika matailosi a konkire ndipo tsikuli linali la mvula. Chapakati koma kumanja kwa chithunzichi, katapila akukoka chithabwa chomwe chikusalaza miyala kuti mbali ina isakhale yokwera kuposa inzake. Chakumanzere kuli chilona chomwe chikuteteza dothi kuti lisakokoloke ndi madzi.

24 December, 2015​—Ku Warwick

Ogwira ntchito akukoka mawaya omwe azibweretsa mphamvu za magetsi pa malo onsewa.

5 January, 2016​—Maofesi

Wogwira ntchito akumalizitsa kumanga denga lomwe lili pamwamba pa kanjira komwe kakuchoka ku malo oimika magalimoto a alendo kupita ku maofesi. Dengali lizidzateteza alendo ku mvula komanso chipale chofewa.

5 January, 2016​—Nyumba Yokonzera Zinthu Komanso Koimika Magalimoto

Wogwira ntchito akudina mabatani pamalo oyatsira makina okhala ndi thanki yotenthetsera zinthu. Panopa ku Warwick kuli mathanki 4.

8 February, 2016​—Maofesi

Ogwira ntchito akumangirira mashini oumitsira zovala m’chipinda chochapira. M’mashiniwa angathe kuikamo zovala zolemera makilogalamu 6 mpaka 45. Mashini ochapira adzakhala ku khoma limene likuoneka kumanzere.

8 February, 2016​—Ku Malo Athu a ku Tuxedo

A Gerrit Lösch, omwe ndi membala wa Bungwe Lolamulira akuchititsa phunziro la Nsanja ya Olonda lomwe limachitika pa beteli. Anthu enanso ogwirira ntchito ku Warwick alumikizidwa ndipo akumvetsera pulogalamuyi.

19 February, 2016​—Nyumba Yogona A

Ogwira ntchito m’dipatimenti ina anyamula kalapeti yoti aike mu imodzi mwa nyumba zogona ku Warwick. Makalapeti onse omwe aikidwa m’nyumba za ku Warwick ataphatikizidwa kuti ikhale kalapeti imodzi, kalapetiyo ikhoza kukhala yaikulu mamita 65,000 mbali zonse.

22 February, 2016​—Ku Warwick

Zipepala zovomereza kuti nyumba zogona C ndi D ziyambe kugwira ntchito zinaperekedwa pakati pa September 2015 ndi February 2016. Panopa ogwira ntchito ku Warwick akumagona m’nyumbazi. Msewu wopita ku nyumba zogona anamaliza kuukonza ndipo anaika matailosi a konkire. Zikepi zonse anamalizanso kuzimangirira. Chifukwa chakuti kumalowa si kuzizira kwambiri, ntchito yodzala maluwa ndi kapinga inayambika ngakhale kuti nthawi imene ankafuna kudzayamba inali isanakwane.

24 February, 2016​—Nyumba Yokonzeramo Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Wogwira ntchito wavala zinthu zomuthandiza kuti athe kufikira pamalo pamene akuika zitsulo zimene padzakhale siling’i. Ogwira ntchito m’dipatimentiyi ndi amene amaika zitsulo zoikapo siling’i, kumangirira makoma amatabwa, kupanga pulasitala komanso kuika mkati mwa khoma zinthu zoteteza ku moto.