Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anthu Anasangalala Kwambiri Pamsonkhano wa M’chilankhulo cha Chitagalogi ku Rome

Anthu Anasangalala Kwambiri Pamsonkhano wa M’chilankhulo cha Chitagalogi ku Rome

Pa 24 mpaka 26 July 2015, a Mboni za Yehova ambirimbiri olankhula Chitagalogi anachita msonkhano wapadera mumzinda wa Rome, m’dziko la Italy. Mzindawu uli pa mtunda wa makilomita 10,000 kuchokera ku Philippines, komwe anthu olankhula Chitagalogi amachokera.

Kafukufuku wina akusonyeza kuti panopa anthu oposa 850,000 ochokera ku Philippines akukhala ku Europe. Izi zachititsa kuti ku Europe kukhale timagulu ndiponso mipingo yokwana 60 ya Mboni za Yehova imene imachita misonkhano yawo ndiponso kulalikira m’Chitagalogi.

Pamsonkhano wa masiku atatu womwe unachitikira ku Rome, timagulu ndiponso mipingo yonseyi inasonkhana limodzi kwa nthawi yoyamba ndipo zonse zinkachitika m’chilankhulo chawo. Anthu okwana 3,239 amene anapezekapo anasangalala kwambiri chifukwa M’bale Mark Sanderson, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene ankakamba nkhani yomaliza tsiku lililonse. Kale, m’baleyu anatumikirapo m’dziko la Philippines.

“Zandifika Pamtima”

Koma funso n’kumati, Kodi pali kusiyana kulikonse munthu akachita msonkhano m’chilankhulo chake kapena m’chilankhulo china chimene amamva? Mayi wina, yemwe akulera yekha ana, dzina lake Eva anati: “Ndimamva pang’ono Chingelezi, koma chifukwa cha msonkhano wa m’Chitagalogiwu, panopa mfundo za m’Baibulo zandifika pamtima.” Pofuna kuti akhale ndi ndalama zokwanira zodzayendera kuchokera ku Spain kumene amakhala kupita kumalo a msonkhano ku Italy, mayiyu ndi ana ake awiri anasankha kuti asiye kudya kulesitilanti mlungu uliwonse ndipo ankangochita zimenezi kamodzi kokha pa mwezi. Mayiyu anati: “Tinachita bwino kwambiri chifukwa pamsonkhanowu ndinamva mfundo iliyonse imene inakambidwa.”

Jasmin, yemwe amakhala ku Germany, anapempha kuti abwana ake amupatse tchuthi n’cholinga choti adzapezeke pamsonkhanowu. Koma iye anati: “Nditangotsala pang’ono kuti ndinyamuke, ndinauzidwa kuti ndisapite chifukwa kunali ntchito yambiri. Nditamva zimenezi sindinataye mtima. Ndinapemphera kwa Yehova kenako n’kukalankhula ndi abwana angawo. Tinagwirizana zimene tingachite n’cholinga choti ndipitebe kumsonkhanowo. Zinali zosangalatsa kwambiri kusonkhana limodzi ndi abale ndi alongo ambiri a ku Philippines amene anabwera kuchokera kumayiko osiyanasiyana a ku Europe.”

Anthu ambiri a ku Philippines omwe akukhala ku Europe amasowa zinthu za kwawo komanso amasowana ndi anzawo amene anasamukira kumayiko ena a ku Europe. Koma msonkhanowu unathandiza kuti anthu ambiri a ku Philippines akumanenso ndi anzawo omwe panopa ndi abale ndi alongo awo auzimu. (Mateyu 12:48-50) Munthu wina dzina lake Fabrice anati: “Ndinasangalala kwambiri kuonananso ndi anthu amene ndimadziwana nawo.” Pamene msonkhanowu unkatha, mlongo wina ankanena mobwerezabwereza kuti: “Ndasangalala kwambiri, zinangokhala ngati takumananso ndi achibale athu omwe tinasowana nawo.”