Nthawi Yochoka ku Hotelo ya Bossert
Mu November 2012, a Mboni za Yehova anagulitsa Hotelo ya Bossert. Iwo anapereka makiyi a hoteloyo kwa munthu amene anaigula n’kuchokako moti kuyambira nthawi imeneyo analibenso mphamvu zilizonse pa hoteloyo. Ndalama zimene anapeza atagulitsa hoteloyo azigwiritsa ntchito popititsa patsogolo ntchito yawo yapadziko lonse yophunzitsa anthu Baibulo.
A Mboniwa anagulitsa nyumbayi, yomwe inali ya nsanja 14 yomangidwa ngati nyumba za ku Italy za m’zaka za m’ma 1500 kapena 1600, chifukwa chakuti akusamutsa likulu lawo lomwe panopa lili ku Brooklyn mumzinda wa New York. Iwo akufuna kusamukira ku Warwick mumzinda womwewo wa New York. Pali chiyembekezo choti patenga zaka zingapo kuti asamuke.
Yakhalapo kwa Zaka Zoposa 100
Louis Bossert, yemwe ankachita bizinezi ya matabwa ku New York, ndi amene anamanga hoteloyi m’chaka cha 1909 n’kuipatsa dzina lake lakuti Bossert. Iye anamanga hoteloyi kuti ikhale ndi zipinda zogona anthu apaulendo komanso anthu ofuna kuchita lendi kwa nthawi yaitali. Popeza hoteloyi inadzadza mwachangu moti makasitomala ena ankasowa pokhala, mu 1914, iye anaiwonyezera ndipo inakula kuwirikiza maulendo awiri poyerekeza ndi poyamba.. Kenako anamanga lesitanti pamwamba pa denga la hoteloyo m’chaka cha 1916 ndipo ankaitcha Marine Roof.
M’zaka za m’ma 1980, a Mboni za Yehova anagula nyumbanyi n’kuikonzanso kuti muzikhala anthu ena a Mboni amene amagwira ntchito kulikulu lawo. Iwo anakonza mabafa kuti akhale zipinda zodyera komanso lesitanti yomwe inali pamwamba pa denga kuti ikhale malo ochezera.
Kuyambira chaka cha 2010, kunyumbayi kwakhala kukufikira alendo a Mboni za Yehova ochokera m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi omwe amapita kukaona malo kumalikulu awo.
Munthu amene wagula nyumbayi akufuna kuikonza kuti ikhale hotelo. Panopa nyumbayi, yomwe a Mboni ankaigwiritsanso ntchito ngati situdiyo, ikuoneka bwino kwambiri moti munthu amene waigula savutika kuikonza kuti ikhale hotelo yapamwamba kwambiri.
Kuikongoletsanso
A Mboni za Yehova asanagule hotelo ya Bossert, sinkasamaliridwa kwa zaka zambiri ndithu. Makoma anali akuda kwambiri komanso pulasitala inali itawonongeka kwambiri. Nawonso mawindo anali ataphwasuka. Alendo amene ankadya mu lesitanti imene inali pamwamba pa denga, yotchedwa Marine Roof, anali nkhunda basi. Apa panalibenso mochitira koma kuyamba chintchito chokonza nyumbayi. A Mboni za Yehova ochokera m’madera onse a dziko la United States anadzipereka kugwira ntchito imeneyi yomwe inatha mu 1991.
Pa nthawiyi, a Mboni anachapa komanso kukonza khoma lopaka laimu lakunja kwa nyumbayi. Anaikanso zinthu zatsopano zokongoletsera makoma a pulasitalawo. Anaikanso mawindo atsopano komanso apamwamba kwambiri opangidwa ndi matabwa a m’bawa.
Anakonzanso mkati mwa nyumbayo moti malo olandirira alendo anakongola ngati kuti angomangidwa kumene. Pofuna kukonza makoma amene anawonongeka, anaitanitsa miyala ya kwale kuchokera ku Italy yomwe anaigwiritsira ntchito pomanga nyumbayo. Anakonzanso siling’i yomwe inali itawonongeka ndi madzi.
Zinali zovuta kukonza nsanamira zachitsulo zomwe zinali pachipinda cholandirira alendo kuti zizionekanso ngati mmene zinkaonekera. Poyamba nsanamirazo zinapakidwa pulasitala wa ku Italy yemwe amaoneka wonyezimira komanso wokongola kwambiri ngati mabo. Koma anthu oyamba amene ankagwiritsira ntchito nyumbayi anapenta mobwerezabwereza nsanamirazi. Pa anthu onse a Mboni amene ankagwira ntchito yokonzanso nyumbayi, panalibe aliyense amene akanatha kuika pulasilatala wooneka ngati maboyu pansanamirazi. Zitatero anapita ku laibulale ya payunivesite ina yomwe inali pafupi ndi malowa kukabwereka buku lomwe linali ndi malangizo a kapakidwe ka pulasitala wooneka ngati mabo. Atawerenga malangizowa anagwira ntchito kwa milungu ingapo popaka pulasitalayu ndipo sanamirazo zinakongolanso pafupifupi kufanana ndi mmene zinalili nyumbayo itangomangidwa kumene.
Ntchito yokonzanso nyumbayi inatha mu 1991, ndipo nyumbayi inali yabwino komanso yokongola kwambiri. A Mboni analandira chikalata cha ulemu (kuchokera ku bungwe la Lucy G. Moses Preservation) chifukwa cha ntchito yotamandika imene anagwira pokonzanso nyumbayo.