Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 43

Pemphero Lothokoza

Pemphero Lothokoza

(Salimo 95:2)

  1. 1. Yehova tikufuna kuthokoza

    Kudzera mupemphero lathuli.

    Tizitumikira mofunitsitsa,

    Timadziwa mumatithandiza.

    Ndife anthu obadwa ndi uchimo

    Chonde muzitikhululukira.

    Tikuthokoza munatiwombola

    Ndi dipo la mwana wanu Yesu.

  2. 2. Zikomo chifukwa munatikonda,

    Munatikokeranso kwa inu.

    Tiphunzitseni za inu Mulungu

    Kuti nafe tizikukondani.

    Zikomo chifukwa cha mzimu wanu,

    Timalankhula molimba mtima.

    Tizitumikira modzichepetsa.

    Tikukuthokozani Yehova.