Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 34

Kuchita Zinthu Mokhulupirika

Kuchita Zinthu Mokhulupirika

(Salimo 26)

  1. 1. Mulungu wanga mundiweruze,

    Muone ngati ndimakudalirani.

    Ndifufuzeni ndi kundiyesa.

    Konzani mtima wanga, mundidalitse.

    (KOLASI)

    Koma ine ndatsimikizadi

    Kumachita zinthu mokhulupirika.

  2. 2. Sindicheza ndi anthu oipa.

    Ndimadana ndi onyoza choonadi.

    Chonde musachotse moyo wanga

    Limodzi ndi anthu okonda zoipa.

    (KOLASI)

    Koma ine ndatsimikizadi

    Kumachita zinthu mokhulupirika.

  3. 3. Ndimakonda nyumba yanu M’lungu.

    Ndimasangalala kukulambirani.

    Ndidzayendadi kuguwa lanu

    Pokutamandani mokweza kwambiri.

    (KOLASI)

    Koma ine ndatsimikizadi

    Kumachita zinthu mokhulupirika.

(Onaninso Sal. 25:2.)