Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 14

Tamandani Mfumu Yatsopano Yolamulira Dziko Lapansi

Tamandani Mfumu Yatsopano Yolamulira Dziko Lapansi

(Salimo 2:​12)

  1. 1. Anthu ochokera m’mitundu

    yonse asonkhana. 

    Khristu ndi odzozedwawo

    Akuwasonkhanitsa. 

    Ufumu wa M’lungu wayamba

    Tikupempha ubwere.

    Tonse tikudikirirabe

    Ndipo tikusangalala.

    (KOLASI)

    Tamandani M’lungu, watipatsa Yesu

    Kukhala Mfumu ya mafumu.

    Tizimumvera mogwirizana

    Ndi kumamutamanda.

  2. 2. Titamande Mfumu yathu poimba

    Mwachimwemwe.

    Kalonga Wamtendereyu

    Adzatipulumutsa.

    Tidzasangalala kukhala

    M’dziko mopanda mantha.

    Akufa adzawaukitsa.

    Tidzasangalala ndithu.

    (KOLASI)

    Tamandani M’lungu, watipatsa Yesu

    Kukhala Mfumu ya mafumu.

    Tizimumvera mogwirizana

    Ndi kumamutamanda.