Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 104

Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

(Luka 11:13)

  1. 1. Yehova M’lungu ndinu wamkulu.

    Mumaposa mitima yathu.

    Muzitithandiza pamavuto.

    Mutilimbitse ndi mzimu wanu.

  2. 2. Ndife ochimwa, operewera.

    Nthawi zina timalakwitsa.

    Tikupempha mutipatse mzimu

    Utitsogolere nthawi zonse.

  3. 3. Tikafooka ndi kukhumudwa,

    Mzimu uzitilimbikitsa.

    Mutipatse mphamvu tisagonje.

    Muzitipatsa mzimu woyera.