KHALANI MASO
Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Kapena Kuthandizira Nkhondo?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Monga mmene taonera pa nkhondo imene ikuchitika ku Ukraine, atsogoleri ambiri achipembedzo akulimbikitsa anthu kuti atengepo mbali pa nkhondoyo. Taonani mmene atsogoleri achipembedzo ambali zonse ziwiri akhala akuchitira zimenezi.
Epiphanius I yemwe ndi mkulu wa tchalitchi cha Orthodox ku Kyiv, ananena kuti: “Ulemu waukulu upite kwa asilikali athu amene akuteteza dziko lathu la Ukraine kwa anthu ankhanza. . . Timakukondani ndipo nthawi zonse tikumakupemphererani pamene mukumenya nkhondo imeneyi.”—The Jerusalem Post, March 16, 2022
“Mtsogoleri wa Tchalitchi cha Russian Orthodox, lamlungu lina anakonza mwambo wopempherera asilikali a dziko la Russia ndipo anawalimbikitsa kuti ateteze dziko lawo mmene angathere. Iye anati monga nzika za dzikolo, ndi udindo wawo kuchita zimenezi pamene dziko la Russia likupitirizabe kulimbana ndi dziko la Ukraine.”—Reuters, April 3, 2022
Kodi Akhristu ayenera kutenga nawo mbali pa nkhondo? Kodi Baibulo limanena zotani?
Zimene Baibulo limanena
Baibulo limanena kuti otsatira a Yesu enieni satenga nawo mbali iliyonse pa nkhondo.
“Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”—Mateyu 26:52.
Kodi tingati munthu amene akuvomereza kuti nkhondo izichitika kapenanso amene akumenya nawo nkhondoyo akumvera mawu a Yesu amenewa?
“Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:34, 35.
Kodi tingati munthu amene akuvomereza kuti nkhondo izichitika, akusonyeza chikondi chimene Yesu ananena kuti ophunzira ake adzadziwika nacho?
Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?”
Mmene Akhristu Amaonera Nkhondo Masiku Ano
Kodi ndi zoyenera kuti Akhristu asamatenge nawo mbali pa nkhondo masiku ano? Inde. Baibulo linaneneratu kuti mu nthawi yathu ino, yomwe imatchedwa “masiku otsiriza,” anthu ochokera ku mitundu yonse “sadzaphunziranso nkhondo,” mogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa.—Yesaya. 2:2, 4.
Kuti mudziwe zambiri werengani nkhani za mu Nsanja ya Olonda zokhala ndi mutu wakuti, “Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo?”
Posachedwapa, Yehova a yemwe ndi “Mulungu wamtendere” agwiritsa ntchito boma lake lakumwamba kupulumutsa anthu ku “chipsinjo ndi chiwawa.”—Afilipi 4:9; Salimo 72:14.
Kuti mudziwe mmene adzachitire zimenezi, onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18