KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?
Kuthandiza Anthu Amene Akhudzidwa Ndi Ngozi Zadzidzidzi
FEBRUARY 1, 2021
M’chaka cha 2020 munachitika ngozi zam’chilengedwe zambiri kuphatikizapo mliri wa COVID-19 womwe unakhudza dziko lonse. Kodi a Mboni za Yehova anathandiza bwanji anthu amene anakhudzidwa?
M’chaka chautumiki cha 2020, * Komiti ya Ogwirizanitsa ya Bungwe Lolamulira inavomereza kuti ndalama zokwana madola * 28 miliyoni zigwiritsidwe ntchito pothandizira anthu omwe anakhudzidwa. Ndalamazi zinagwiritsidwa ntchito pothandizira anthu omwe anakhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi zoposa 200, zomwe zikuphatikizapo mliri wa COVID-19, mphepo zamkuntho, kusefukira kwa madzi ku Africa, kusowa kwa chakudya ku Venezuela komanso chilala ku Zimbabwe. Ndalamazi, zomwe anthu anapereka mwa kufuna kwawo, zinagwiritsidwa ntchito pogulira chakudya, madzi, zovala, kulipirira malo okhala, kupezera thandizo lachipatala komanso zinthu zina zogwiritsira ntchito poyeretsa, kukonzera zinthu zowonongeka ndi kumanganso nyumba zomwe zinawonongeka. Tiyeni tione zitsanzo zochepa za ntchito yothandiza anthuyi.
COVID-19. Padziko lonse, mliriwu wakhudza abale ndi alongo athu m’njira zosiyanasiyana. Pofuna kuthandiza abale ndi alongowa, Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi oposa 800 anakhazikitsidwa padziko lonse. Abale a m’makomitiwa ankafufuza zinthu zomwe abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi mliriwu ankafunikira, ndipo mwamsanga ankadziwitsa Komiti ya Ogwirizanitsa kuti idziwe thandizo loyenera lomwe linkafunika.
Kwa chaka chonse, Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi anathandiza anthu ambiri kupeza chakudya, madzi, zinthu zowathandiza kukhala a ukhondo komanso mankhwala. M’madera ena makomitiwa ankagwira ntchito ndi akulu a m’maderawo kuti athandize abale kupeza thandizo kuboma.
Anthu ena omwe si a Mboni, anachita chidwi ndi ntchito yothandiza anthuyi. Mwachitsanzo a Field Simwinga omwe ndi bwanamkubwa wa tauni ya Nakonde ku Zambia anauza abalewo kuti: “Tikuyamikira kwambiri chifukwa cha thandizo la pa nthawi yake lomwe linaperekedwa kwa mabanja omwe anakhudzidwa ndi mliriwu.”
Kusowa kwa Chakudya ku Angola. Mliri wa COVID-19 unachititsa kuti chakudya chikhale chochepa komanso chodula kwambiri ku Angola. Moti abale ndi alongo athu ambiri ankalephera kugula chakudya.
Ofesi ya nthambi ya ku Brazil inapemphedwa kuti ithandize abale athu a ku Angola powatumizira zakudya zosiyanasiyana. Pofuna kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene anthu amapereka, abale ankafufuza mosamala kwambiri njira zogulira komanso zotumizira chakudyachi ndipo ankagula chakudya chambiri nthawi imodzi. Chakudya chomwe ankagula komanso kuchitumiza kwa munthu mmodzi, chinali chokwana madola 22 ndipo chinali cholemera pafupifupi makilogalamu 20. Munthu aliyense ankapatsidwa zinthu monga mpunga, nyemba komanso mafuta ophikira. Pofika pano, chakudya chokwanira anthu 33,544 chomwe ndi cholemera matani 654 chinatumizidwa. Chakudya china chinapezeka m’dzikolo ndipo kuwonjezera ndi chakudya chinatumuzidwachi, anthu oposa 50,000 analandira thandizoli.
Kodi abale omwe analandira thandizoli anamva bwanji? Alexandre, yemwe amakhala kudera lina lakutali ku Angola anati: “Ndimaona kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova amandikonda komanso kuti sindili ndekha. Ndikuona kuti gulu la Yehova limandiganizira kwambiri.” Mayi wina yemwe akulera yekha ana dzina lake Mariza anati: “Yehova anamva pemphero langa ndipo ndimamuthokoza komanso ndimathokoza gulu lake.”
Kuthandiza Anthu Okhudzidwa Ndi Chilala ku Zimbabwe. M’chaka chautumiki cha 2020, m’dziko la Zimbabwe munagwa chilala ndipo chinachititsa kuti anthu mamiliyoni akhudzidwe ndi njala, ndipo a Mboni ambiri a m’dzikolo analibe chakudya chokwanira.
Makomiti 5 Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi anakonzedwa n’cholinga choti athandize kupereka chakudya kwa abale athu. Ofalitsa ambiri anathandiza abale a m’makomitiwa kupakira chakudya ndi zinthu zina komanso ankawabwereka magalimoto. * M’chaka chautumiki cha 2020, madola okwana 691,561 anagwiritsidwa ntchito pogulira chakudya cha anthu oposa 22,700.
M’madera ena, abale ena analibiretu chakudya pa nthawi imene thandizoli linkafika. Chakudyachi chitafika iwo analemekeza Yehova ndipo ena anayamba kuimba nyimbo za Ufumu.
M’dera lina, alongo awiri amasiye anapita ku msonkhano wina womwe unkachitika m’deralo umene unakonzedwa kuti akakambirane za thandizo la chakudya limene bungwe lina lomwe si la boma linkafuna kupereka. Koma pamsonkhanowo panayamba kuchitika zinthu zokhudzana ndi zandale ndipo alongowa anasankha kuti asachite nawo zinthu zina zomwe munthu ankafunika kuchita alandire thandizolo. Pamene ankachoka pamsonkhanowo anthu ena anayamba kuwanyoza n’kumawauza kuti “Musadzabwere kwathu kumadzapempha chakudya.” Koma patangopita mawiki awiri, abale athu anafika m’deralo ndipo anapereka thandizo la chakudya kwa alongo aja. Pa nthawiyo, bungwe lija linali lisanafike n’komwe.
Ntchito yothandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi chilala ku Zimbabwe yathandizanso pa ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira Prisca yemwe amakhala m’mudzi wina waung’ono. Ngakhale kuti panali mavuto ambiri chifukwa cha chilalachi, Lachitatu komanso Lachisanu lililonse, iye ankagwira ntchito yolalikira ngakhalenso mu nyengo yolima. Anthu a m’mudzimo ankamunena kuti: “Uvutitsa banja lako ndi njala chifukwa cha zolalikira zakozo.” Prisca ankawayankha kuti: “Yehova sanasiyepo atumiki ake.” Pasanapite nthawi yaitali, iye analandira thandizo kuchokera ku gulu lathu. Zimenezi zinachititsa chidwi anthu ena omwe amakhala pafupi ndi Prisca, ndipo anamuuza kuti: “Mulungu sanakusiyepo, choncho tikufuna kuphunzira zambiri zokhudza Mulungu ameneyo.” Panopa anthu 7 mwa amenewa amamvetsera misonkhano yampingo yomwe imaulutsidwa pa wailesi.
Pamene mapeto akuyandikira kwambiri, tizikumanabe ndi ngozi zam’chilengedwe. (Mateyu 24:3, 7) Timayamikira kwambiri ndalama zanu zomwe mumapereka pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zopezeka pa donate.jw.org. Ndalamazi zimagwiritsidwa ntchito pothandiza anthu omwe akufunikira thandizo.
^ Chaka chautumiki cha 2020 chinayamba mu September 2019 ndipo chinatha mu August 2020.
^ Madola onse omwe atchulidwa munkhaniyi ndi a ku America.
^ Mliri wa COVID-19 unachititsa kuti anthu asamaloledwe kuyenda, choncho abale anthu ankafunika kupempha chilolezo kuti akapereke chakudya. Pamene ankachita zimenezi, iwo ankayesetsa kudziteteza kuti asatenge matendawa.