Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Kachipangizo Kothandiza Kwambiri

Kachipangizo Kothandiza Kwambiri

SEPTEMBER 1, 2020

 Masiku ano a Mboni za Yehova akulandira mabuku ndi mavidiyo ambiri othandiza pophunzira Baibulo pazipangizo zamakono kuposa kale. Koma kumadera ambiri abale ndi alongo athu amalephera kugwiritsa ntchito intaneti chifukwa ndi yokwera mtengo kwambiri. Enanso amakhala m’madera amene intaneti imadukaduka, imachedwa kwambiri kapenanso kulibiretu.

 Ngakhale zili choncho, abale ndi alongo athu ambiri amatha kupanga dawunilodi mabuku ndi mavidiyo athu popanda kugwiritsa ntchito intaneti. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

 Zimatheka ndi JW Box. JW Box ndi kachipangizo kakang’ono kamene kamaperekedwa kumipingo kumene intaneti ndi yovuta. Kachipangizoka timachita kugula kumakampani ena ndipo kamagwira ntchito ngati intaneti. A m’Dipatimenti ya Makompyuta ku Beteli, amaikamo pulogalamu yawo kuti kachipangizoka kazigwira bwino ntchito. Amaikamonso mabuku ndi mavidiyo omwe amapezeka pa jw.org. Ka JW Box kamodzi amakagula pamtengo wa madola pafupifupi 75.

 Ndiye popeza JW Box imagwira ntchito ngati intaneti, abale ndi alongo pa Nyumba ya Ufumu amatha kulumikiza zipangizo zawo zamakono n’kumapanga dawunilodi mabuku ndi mavidiyo. Ndipo sizifunika kuti munthu akhale ndi chipangizo chotsogola kuti akwanitse kulumikiza. Koma ngati pampingo palibe intaneti, ndiye zimatheka bwanji kuti JW Box izikhala ndi zinthu zimene zatuluka kumene? A ku ofesi ya nthambi amatumiza mafulashi okhala ndi zinthu zatsopano zimene zatuluka pa jw.org ndipo ndi zimene amakaziika mu JW Box. Fulashi iliyonse mtengo wake ndi pafupifupi madola 4.

 Kodi JW Box yathandiza bwanji abale athu? Nathan Adruandra wa ku Democratic Republic of Congo, yemwe ali ndi ana, ananena kuti: “Ndakhala ndikuyesetsa kuti ndipange dawunilodi mavidiyo akuti ‘Inu Yehova, . . . Chikhulupiriro Changa Chili Mwa Inu’ ndi Kumbukirani Mkazi wa Loti, koma sizinkatheka ndipo zinkandikhumudwitsa kwambiri. Panopa ndingathe kupanga dawunilodi mavidiyowa mufoni yanga, zomwe zikuthandiza makolofe kuti tizitha kuphunzitsa bwino ana athu.”

 M’bale wina wa ku Nigeria, yemwe amathandiza mipingo kulumikiza JW Box, ananena kuti: “Abale amaona kuti JW Box ndi mphatso yapadera yochokera kwa Yehova. Iwo ndi osangalala kuti tsopano angathe kupanga dawunilodi mosavuta mabuku komanso mavidiyo omwe amapezeka pa Zinthu Zophunzitsira.”

 Pofika pano tatumiza ma JW Box oposa 1,700 kwa abale athu kumipingo ya ku Africa, Oceania komanso South America. Ndipo tikukonza zotumizanso ena kumipingo ina yambiri. Kodi ndalama zake zimachokera kuti? Zimachokera m’zopereka za Ntchito Yapadziko Lonse, zomwe zambiri zimaperekedwa kudzera pa donate.jw.org. Tikukuyamikirani kwambiri chifukwa chopereka mowolowa manja.