KALE LATHU
Anapereka Zinthu Zawo Zabwino Kwambiri
Pamene nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inatha mu 1945, zinthu zambiri ku Germany zinali zitawonongeka. Mizinda yambiri inali itawonongeka moti sankatha kugwiritsa ntchito masukulu ndi zipatala. Komanso kulikonse kunali mabomba omwe anali asanaphulike. Chakudya chinalinso chochepa kwambiri moti mitengo yake inali yodula. Mwachitsanzo, munthu ankagula magalamu 500 a bata pa ndalama zofanana ndi zimene angapeze pogwira ntchito kwa milungu 6.
Pa anthu amene ankavutika, panali a Mboni za Yehova mahandiredi ambiri omwe anali atakhala m’ndende kwa zaka zingapo chifukwa cha zimene amakhulupirira. Mu 1945, anamasulidwa m’ndende ali ndi zovala zakundende zomwe ankavala basi. A Mboni ena anali atalandidwa nyumba ndi zinthu zawo zina. Ena ankakhala ndi njala kwambiri moti ankakomoka ali kumisonkhano ya Chikhristu.
A Mboni Akumayiko Ena Anathandiza Mwamsanga
A Mboni za Yehova akumayiko ena anayamba mwamsanga kutumiza chithandizo cha chakudya ndi zovala. Abale akulikulu lapadziko lonse ku United States anapempha abale a ku ofesi ya nthambi ku Bern, Switzerland kuti athandize abale ndi alongo a ku Germany. M’bale Nathan H. Knorr wochokera kulikulu anapita ku Europe kukathandiza kuti ntchito yokapereka chithandizo iyende mofulumira.
A Mboni a ku Switzerland anapereka mowolowa manja chakudya, zovala ndi ndalama. Zinthuzi zinkatumizidwa kaye kumzinda wa Bern kumene abale ankaziika m’magulu, kuzilongedza kenako n’kuzitumiza ku Germany. A Mboni akumayiko ena monga ku Sweden, Canada ndi ku United States anaperekanso zinthu zothandiza a Mboni anzawo a ku Germany komanso akumayiko ena ku Europe ndi ku Asia, kumene zinthu zambiri zinali zitawonongeka chifukwa cha nkhondoyo.
Anathandiza Modabwitsa
Patangotha miyezi yochepa, a Mboni akunthambi ya ku Switzerland anali atatumiza zinthu monga khofi, mkaka, shuga, zipatso, masamba komanso zitini za nyama ndi nsomba. Abale anaperekanso ndalama.
Kuwonjezera pa zimenezi, a Mboni a ku Switzerland anatumizanso matani 5 a zovala, kuphatikizapo majasi, zovala za akazi komanso masuti a amuna. Nsanja ya Olonda ya January 15, 1946 inati: “Abale sanapereke zinthu zakutha koma zinthu zawo zabwino kwambiri. Iwo anadzipereka kwambiri kuti athandize abale awo a ku Germany.”
A Mboni a ku Switzerland anaperekanso pafupifupi mapeyala 1,000 a nsapato zomwe abale anaziona kaye kuti atsimikizire ngati zinali zabwino asanazitumize. Abale ndi alongo amene anazilandira ku Wiesbaden, Germany anadabwa kuona kuti nsapatozo zinali zabwino kwambiri komanso zamitundu yosiyanasiyana. Wa Mboni wina analemba kuti: “Kulibe shopu iliyonse ku Germany kumene ungapeze nsapato zosiyanasiyana chonchi.”
Abale anapitiriza kupereka chithandizo mpaka mu August 1948. A Mboni a ku Switzerland anatumiza kwa abale a ku Germany makontena okwana 444 a chithandizo omwe analemera matani 25. Monga tanenera, si a Mboni a ku Switzerland okha amene anathandiza pa ntchitoyi. Koma pa magulu onse amene anathandiza, gulu la ku Switzerland linali laling’ono. Tikutero chifukwa pa nthawiyo kunali a Mboni 1,600 okha ku Switzerland.
“Muzikondana”
Yesu Khristu ananena kuti: “Muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Chifukwa cha chikondi, anthu a Yehovawa anapereka zinthu zawo zabwino kwambiri, osati zimene sankazifuna basi. (2 Akorinto 8:1-4) Kalata yochokera ku Zurich inanena kuti “abale ambiri amene alibe zokwanira koma amene ankafuna kuthandiza, anapereka ndalama komanso matikiti awo ochokera ku boma olandirira zinthu.”
Sizinatenge nthawi kuti zinthu ziyambe kuwayendera bwino anthu a Yehova a ku Germany omwe anali atazunzidwa komanso kuvutika chifukwa cha nkhondo. Ndiye chinthu chimodzi chimene chinawathandiza chinali chithandizo chimene a Mboni anzawo anapereka mwadongosolo komanso mowolowa manja posonyeza chikondi chenicheni.
A Mboni a ku ofesi ya nthambi ku Bern, Switzerland akuika m’magulu zovala zimene zinaperekedwa kuti zipite kwa a Mboni anzawo a ku Germany
Makontena a zinthu zimene zinaperekedwa akuikidwa muthiraki ku ofesi ya nthambi ya ku Bern
Thiraki yodzaza ndi makontena olembedwa kuti “Ntchito Yopereka Chithandizo ya Mboni za Yehova”
Makontena a zinthu zimene zinaperekedwa zikuikidwa pasitima kuti zipite ku Germany