Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Okana Khristu Ndi Ndani?

Kodi Okana Khristu Ndi Ndani?

Filimu ina yoopsa kwambiri yaposachedwapa inali ndi mutu wakuti, Wokana Khristu.

Gulu lina lotchuka la oimba linatulutsa abamu ya mutu wakuti, Katswiri Wokana Khristu.

Wafilosofi wina wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Friedrich Nietzsche, analemba buku la mutu wakuti, Wokana Khristu.

Mafumu a m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500, ankatchula anthu omwe ankatsutsa ulamuliro wawo kuti, “okana Khristu.”

Martin Luther, yemwe ankatsutsa Chikatolika ku Germany, ankaona kuti apapa ndi okana Khristu.

MONGA taonera, mawu akuti, “wokana Khristu” amagwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri. Izi zingatipangitse kudzifunsa kuti, ‘Kodi wokana Khristu ndi ndani? Nanga kodi nkhani imeneyi ikutikhudza bwanji ifeyo?’ Mawuwa amapezekanso m’Baibulo ka 5, ndipo Baibulo lingatithandize kudziwa tanthauzo lake.

BAIBULO LIMATITHANDIZA KUDZIWA KUTI WOKANA KHRISTU NDI NDANI

Pa anthu onse amene analemba Baibulo, mtumwi Yohane yekha ndi amene analemba mawu akuti, “wokana Khristu.” Kodi Yohane anasonyeza kuti mawuwa amatanthauza chiyani? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione zimene iye analemba m’kalata yake yoyamba, yomwenso imadziwika ndi dzina lake. Iye analemba kuti: “Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto, ndipo monga mmene munamvera kuti wokana Khristu akubwera, ngakhale panopa alipo okana Khristu ambiri. Chifukwa cha zimenezi timadziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu . . . Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu? Ameneyu ndiye wokana Khristu, amene amakana Atate ndi Mwana.”—1 Yohane 2:18, 19, 22.

Yohane ankaona kuti okana Khristu ndi anthu onse amene amaphunzitsa zabodza zokhudza Yesu Khristu komanso zimene Khristuyo anaphunzitsa

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yohane ananenazi? Popeza Yohane ananena za “okana Khristu ambiri,” izi zikusonyeza kuti wokana Khristu si munthu mmodzi koma gulu la anthu. Okana Khristu amakhala gulu la anthu kapena mabungwe omwe amafalitsa mabodza onena kuti Yesu si Khristu kapena Mesiya. Ena amachititsa kuti anthu asadziwe bwinobwino kuti pali kusiyana kotani pakati pa Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu. Pomwe ena amanama kuti iwowo ndi Khristu kapena ndi oimira Khristu. Koma anthuwa saphunzitsa mfundo za m’Baibulo, n’chifukwa chake Yohane ananena kuti, “anachoka pakati pathu.” Ndipotu anthu oterewa analiponso pa nthawi imene Yohane ankalemba kalata yake. Yohane analemba kalatayi “pa nthawi yakumapeto,” zomwe mwina zikutanthauza kuti anailemba chakumapeto kwa nthawi ya atumwi.

Yohane analembanso mfundo ina yokhudza okana Khristu. Pa nthawiyi ankachenjeza zokhudza aneneri onyenga. Iye anati: “Kuti tidziwe ngati mawu ali ouziridwa ndiponso ochokera kwa Mulungu, timadziwira izi: Mawuwo amavomereza zoti Yesu Khristu anabwera monga munthu. Koma mawu alionse ouziridwa amene amatsutsa zoti Yesu anabwera monga munthu, amenewo si ochokera kwa Mulungu, ndipo ndi ouziridwa ndi wokana Khristu amene munamva kuti akubwera, ndipo tsopano ali kale m’dziko.” (1 Yohane 4:2, 3) Kenako m’kalata yake yachiwiri anati: “Anthu onyenga ambiri alowa m’dziko, amene amatsutsa zakuti kalero Yesu Khristu anabwera monga munthu. Amene amachita zimenezi ndi wonyenga uja ndiponso wokana Khristu.” (2 Yohane 7) Choncho Yohane ankaona kuti okana Khristu ndi anthu onse amene amaphunzitsa zabodza zokhudza Yesu Khristu komanso zimene Yesuyo anaphunzitsa.

“ANENERI ONYENGA” KOMANSO “MUNTHU WOSAMVERA MALAMULO”

Yesu anachenjeza kuti aneneri onyenga adzabwera “atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa”

Zaka zambiri Yohane asanalembe zokhudza anthu ophunzitsa zabodzawa, Yesu Khristu anauza ophunzira ake kuti: “Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.” (Mateyu 7:15) Komanso mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu a ku Tesalonika kuti: “Wina asakunyengeni pa nkhani imeneyi m’njira iliyonse. Pakuti tsikulo [la Yehova] silidzayamba kufika mpatuko usanachitike, ndiponso asanaonekere munthu wosamvera malamulo, amene ndiye mwana wa chiwonongeko.”—2 Atesalonika 2:3.

Choncho m’nthawi ya atumwi, n’kuti aneneri onyenga komanso anthu ampatuko atayamba kale kuonekera ndipo cholinga chawo chinali kusokoneza mpingo wachikhristu. Anthu onse amene ankafalitsa mabodza onena za Yesu Khristu komanso zomwe iye anaphunzitsa, anali m’gulu la anthu amene Yohane anawatchula kuti, “wokana Khristu.” Paulo anawatchula kuti “mwana wa chiwonongeko” ndipo izi zikusonyeza mmene Yehova amawaonera anthuwa.

SAMALANI KUTI OKANA KHRISTU ASAKUPUSITSENI

Masiku anonso, anthu komanso mabungwe omwe amatsutsa Khristu ndi zomwe iye anaphunzitsa, alipo. Anthuwa amafalitsa dala mabodza n’cholinga chofuna kusokoneza anthu kuti asadziwe zoona zokhudza Yehova Mulungu komanso Mwana wake Yesu Khristu. Tiyenera kusamala kwambiri ndi mabodza amene anthuwa amaphunzitsa. Taonani zitsanzo ziwiri izi.

Kwa zaka zambiri, matchalitchi akhala akulimbikitsa chikhulupiriro cha Utatu chimene chimati Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera amapanga Mulungu mmodzi. Anthu amene amaphunzitsa zimenezi ndi okana Khristu ndipo amapangitsa kuti anthu asadziwe zolondola zokhudza Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu. Zimenezi zimalepheretsa anthu a mitima yabwino kutsanzira Yesu Khristu ndiponso kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.—1 Akorinto 11:1; Yakobo 4:8.

Komanso matchalitchi amalimbikitsa anthu kuti azigwiritsa ntchito Mabaibulo omwe mulibe dzina la Mulungu, lakuti Yehova. Amachita zimenezi ngakhale kuti akudziwa zoti dzina la Mulungu limapezeka ka 7,000 m’mipukutu yakale ya Baibulo. Izi zachititsa kuti anthu ambiri asadziwe zoona zokhudza Mulungu.

Komatu kudziwa dzina la Mulungu n’kofunika kwambiri. Anthu ambiri akadziwa dzina la Mulungu amayamba kukhala naye pa ubwenzi. Izi ndi zimene zinachitikira a Richard atakumana ndi abambo ena a Mboni za Yehova ndi akazi awo. A Richard anati: “Anandiwerengera vesi la m’Baibulo lomwe limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ndinasangalala kwambiri nditamva kuti Mulungu ali ndi dzina chifukwa ndinali ndisanamvepo zimenezi.” A Richard anasintha kwambiri ndipo anayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti azisangalatsa Yehova. A Richard ananenanso kuti: “Kudziwa dzina la Mulungu kwandithandiza kuti Mulungu akhale mnzanga wapamtima.”

Kwa zaka zambiri anthu okana Khristu, akhala akupangitsa kuti anthu ambiri akhale mumdima wadzaoneni. Koma kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, kungatithandize kuti tizindikire okana Khristu komanso kuti tizikana mabodza omwe anthuwa amaphunzitsa.—Yohane 17:17.