Kodi N’zoyenera Kupemphera kwa Oyera Mtima?
ALIYENSE akakhala ndi nkhawa amafuna munthu wina woti amuuze nkhawa zakezo. Nthawi zambiri anthufe timauza nkhawa zathu munthu amene tikudziwa kuti atimvetsa komanso amene anakumanapo ndi zimene zikutidetsa nkhawazo.
Anthu ena amaona kuti mfundo imeneyi imagwiranso ntchito popemphera. M’malo mopemphera kwa Mulungu, yemwe ndi wapamwamba kwambiri, amaona kuti kuli bwino azipemphera kwa oyera mtima. Amakhulupirira kuti oyera mtimawo akhoza kuwamvetsa chifukwa akumanapo ndi mayesero komanso mavuto amene anthu amakumana nawo. Mwachitsanzo, ena akataya chinthu chimene amachiona kuti ndi chofunika kwambiri amapemphera kwa Anthony “Woyera” wa ku Padua ndipo amakhulupirira kuti amathandiza anthu kupeza katundu kapena zinthu zimene zatayika.
Koma kodi Malemba amasonyeza kuti tiyenera kupemphera kwa oyera mtima? Popeza pemphero ndi njira imene timalankhulana ndi Mulungu, tiyenera kudziwa ngati iye amamvadi mapemphero athu komanso ngati amafuna kuti tizipemphera kwa oyera mtima.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Kupemphera kwa oyera mtima kunayamba chifukwa cha zimene Tchalitchi cha Katolika chinkaphunzitsa kuti ngati munthu akupemphera kwa Mulungu, pempherolo lizidzera mwa oyera mtima. Buku lina linanena kuti mfundo yaikulu ya chiphunzitso chimenechi ndi yakuti “munthu ayenera kupemphera kwa oyera mtima kuti akamupemphere kwa Mulungu kuti amuchitire chifundo.” (New Catholic Encyclopedia) Anthu ena amapemphera kwa oyera mtima chifukwa amakhulupirira kuti ndi odalitsika kwa Mulungu. Iwo amaona kuti Mulungu amadalitsa amene amapemphera kwa oyera mtima kusiyana ndi amene amangopemphera okha kwa Mulungu.
Koma kodi n’zimene Baibulo limaphunzitsa? Ena amanena kuti mtumwi Paulo ndi amene anayambitsa zoti anthu azipemphera kwa oyera mtima. Iwo amanena zimenezi potengera zimene Paulo ananena m’kalata imene analembera Akhristu a ku Roma. Iye analemba kuti: “Chotero ndikukudandaulirani abale, kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi mwa chikondi cha mzimu, kuti mulimbikire limodzi ndi ine popemphera kwa Mulungu za ineyo.” (Aroma 15:30) Kodi palembali Paulo ankapempha Akhristu anzake kuti amuchonderere kwa Mulungu? Ayi. Ndipo ngati pakanafunika kuchita zimenezi ndiye kuti iwowo ndi amene ankafunika kupempha Pauloyo kuti awachonderere kwa Mulungu chifukwa iye anali mtumwi wa Khristu. Koma palemba limeneli, Paulo ankalimbikitsa Akhristu kuti azitchula Akhristu anzawo m’mapemphero awo kwa Mulungu. Zimenezi n’zosiyana ndi kupemphera kwa oyera mtima omwe anthu ena amakhulupirira kuti ali kumwamba. N’chifukwa chiyani tikutero?
Mu Uthenga Wabwino umene mtumwi Yohane analemba, muli mawu amene Yesu ananena akuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Iye ananenanso kuti: ‘Chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa adzakupatsani.’ (Yohane 15:16) Yesu sananene kuti tizipemphera kwa iyeyo kuti azikatipemphera kwa Mulungu. M’malo mwake ankatanthauza kuti ngati tikufuna kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tizipemphera kwa Mulungu kudzera mwa Yesu basi.
Pa nthawi imene ophunzira a Yesu anamupempha kuti awaphunzitse kupemphera, iye anayankha kuti: “Mukamapemphera muzinena kuti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.’” (Luka 11:2) Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zonse tikamapemphera tizipemphera kwa Mulungu. Mogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsazi, tiyenera kupemphera kwa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu osati kwa oyera mtima.
Chifukwa chinanso n’chakuti tikamapemphera timakhala tikulambira Mulungu ndipo Baibulo limanena kuti tiyenera kulambira Mulungu yekha basi. (Yohane 4:23, 24; Chivumbulutso 19:9, 10) N’chifukwa chake mapemphero athu ayenera kupita kwa Mulungu yekha.
KODI MUYENERA KUCHITA MANTHA KUPEMPHERA KWA MULUNGU?
Pa ulaliki wa paphiri, Yesu anapereka chitsanzo cha mwana amene akupempha bambo ake chakudya. Iye ananena kuti bambo sangapatse mwana wakeyo mwala m’malo mwa mkate kapena kum’patsa njoka m’malo mwa nsomba. (Mateyu 7:9, 10) Kholo lomwe limakonda mwana wake silingachite zimenezi.
Kuti timvetse mfundoyi, tayerekezerani kuti inuyo ndinu kholo ndipo mwana wanu akufuna kukupemphani chinachake. Monga kholo, mumayesetsa kugwirizana ndi mwana wanuyo ndipo mumamumasukira. Koma chifukwa chochita mantha ndi zimene mungamuyankhe, mwana wanuyo akupempha munthu wina kuti adzakuuzeni zimene iyeyo akufuna. Kodi mungamve bwanji? Kodi mungamve bwanji ngati nthawi zonse mwanayo akafuna kulankhula nanu akumauza munthu wina kuti akuuzeni zimene akufunazo? Kodi zimenezi zingakusangalatseni? N’zodziwikiratu kuti sizingakusangalatseni. Makolo amene amakonda ana awo amafuna kuti anawo azimasuka kulankhula nawo komanso azipempha okha zimene akufuna.
Pogwiritsa ntchito fanizo la mwana amene akupempha chakudya kwa bambo ake, Yesu anauza anthu amene ankawaphunzitsawo kuti: “Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!” (Mateyu 7:11) Apa n’zoonekeratu kuti makolo amafunitsitsa kupatsa ana awo zinthu zabwino. Ngati makolo amachita zimenezi ndiye kuti Yehova amafunitsitsa kwambiri tizimufotokozera tokha nkhawa zathu.
Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye ngakhale titafooka ndi zolakwa zathu. Mulungu sanasankhe anthu kuti azimva mapemphero athu. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.” (Salimo 55:22) Choncho sitiyenera kupemphera kwa oyera mtima poganiza kuti Mulungu samva mapemphero athu.
Mulungu, yemwe ndi Atate wathu, amakonda aliyense payekha. Iye amafuna kutithandiza tikakumana ndi mavuto komanso amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. (Yakobo 4:8) N’zosangalatsa kuti tili ndi mwayi wolankhulana ndi Mulungu wathu komanso Atate wathu, yemwe ndi “Wakumva pemphero.”—Salimo 65:2.