NKHANI YA PACHIKUTO: N’ZOTHEKA KUKHALA NDI MOYO WAPHINDU
Kodi N’zotheka Kukhala ndi Moyo Waphindu?
“Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.”—Salimo 90:10.
MAWU amenewatu ndi oona. Nthawi zambiri, moyo m’dzikoli ndi wodzaza ndi “mavuto ndi zopweteka.” Mwina munadzifunsapo kuti, ‘Kodi n’zotheka kukhala ndi moyo waphindu masiku ano?’
Tiyeni tikambirane zimene zinachitikira mayi wina dzina lake Maria. Poyamba iye anali ndi thanzi labwino koma pano pamene ali ndi zaka 84, sathanso kuchita zinthu payekha. Mtima umafuna koma thanzi lake silimulolanso kuchita zimene ankachita poyamba. Kodi iye angatani kuti aziona kuti moyo wake uli ndi phindu?
Mwina inunso munadzifunsapo ngati moyo wanu uli ndi phindu kapena ayi. N’kutheka kuti ntchito imene mumagwira ndi yotopetsa ndiponso yosasangalatsa. Mwinanso anthu ena sayamikira ntchito yanuyo. Ngakhale zitakhala kuti panopa zinthu zikukuyenderani bwino, mwina mumadera nkhawa zimene zidzakuchitikireni m’tsogolo. Nthawi zinanso mukhoza kumasowa anthu ocheza nawo kapena kukhala ndi nkhawa. Banja lanu lingamakumane ndi mavuto osiyanasiyana monga kukangana. N’kuthekanso kuti wachibale kapena mnzanu amene munkamukonda kwambiri anamwalira. Zoterezi ndi zimene zinachitikiranso André. Bambo ake, omwe iye ankawakonda kwambiri, anadwala mwadzidzidzi n’kumwalira. Imfa imeneyi inakhumudwitsa kwambiri André ndipo zinali zovuta kwambiri kuti aiwale za imfayi.
Kaya tikukumana ndi zotani pa moyo wathu, koma pali funso lofunika kwambiri limene timafuna titadziwa yankho lake. Funso lake ndi lakuti kodi masiku ano n’zotheka kukhala ndi moyo waphindu? Tingapeze yankho la funso limeneli poona moyo wa munthu wina amene anakhalapo ndi moyo padziko lapansi zaka 2,000 zapitazo. Munthu ameneyu ndi Yesu Khristu. Ngakhale kuti iye anakumana ndi mavuto ambirimbiri, anali ndi moyo waphindu. Choncho ifenso tikhoza kukhala ndi moyo waphindu ngati titatsatira chitsanzo chake.