“Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”
“Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—MATEYU 24:14.
Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Luka, yemwe analemba nawo Uthenga Wabwino, ananena kuti Yesu “anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Komanso Yesuyo ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu . . . chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Iye anatumiza ophunzira ake kuti akalalikire uthenga wabwino m’matauni ndi m’midzi ndipo kenako anawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8; Luka 10:1.
Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Ophunzira a Yesu sanachedwe kuyamba kugwira ntchito imene Yesu anawauzayi. “Tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba, anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.” (Machitidwe 5:42) Anthu onse ankagwira nawo ntchito yolalikirayi, osati kungosiyira anthu apadera okha. Wolemba mbiri yakale wina, dzina lake Neander, analemba kuti “Celsus, yemwe anali munthu woyamba kulemba nkhani zotsutsa Chikhristu, ankanyoza Akhristu chifukwa anthu osaphunzira monga owomba nsalu, osoka nsapato komanso ofufuta zikopa ankalalikira nawo uthenga wabwino.” Munthu wina, dzina lake Jean Bernardi, analemba m’buku lake kuti: “[Akhristu] ankafunika kupita kulikonse ndi kukalalikira kwa munthu aliyense. Ankalalikira m’misewu, m’mizinda, m’misika ndiponso m’nyumba za anthu. Ankachita zimenezi kaya alandiridwe kapena ayi. . . . Ndipo ankafunika kukafika kumalekezero a dziko lapansi.”—The Early Centuries of the Church.
Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Wansembe wina wa tchalitchi cha Anglican, dzina lake David Watson, analemba kuti: “Chifukwa china chimene chikuchititsa kuti masiku ano anthu ambiri a m’tchalitchi chathu asamakhale ndi chidwi chotumikira
Mulungu n’chakuti, tchalitchichi sichiona nkhani yolalikira komanso kuphunzitsa kukhala yofunika.” Munthu wina, dzina lake José Luis Pérez Guadalupe, analemba m’buku lina zokhudza anthu a m’tchalitchi cha Evanjeliko, cha Adventist komanso matchalitchi ena. Iye analemba kuti “anthu amenewa samapita kunyumba ndi nyumba.” Koma ponena za a Mboni za Yehova, wansembeyu analemba kuti: “Iwo amalalikira kunyumba ndi nyumba ndipo amayesetsa kufika nyumba iliyonse.”—Why Are the Catholics Leaving?Mfundo yochititsa chidwi komanso yoona ndi imene munthu wina dzina lake Jonathan Turley analemba m’buku lina. Iye anati: “Ukangotchula kuti Mboni za Yehova, anthu ambiri nthawi yomweyo amaganiza za anthu amene amabwera kunyumba zathu mwadzidzidzi n’kumadzatilalikira. Kwa a Mboni za Yehova, kukopa anthu kunyumba ndi nyumba si nkhani yongofuna kuti anthu ambiri ayambe kutsatira chikhulupiriro chawo ayi, koma iwo amaona kuti kuchita zimenezi kumawathandizanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.”—Cato Supreme Court Review, 2001-2002.
[Bokosi patsamba 9]
Kodi Ndani Amasonyeza Kuti Ndi Akhristu Oona?
Mukaganizira mfundo za m’Malemba zimene takambirana mu nkhanizi, kodi inuyo mukuona kuti ndi ndani amene akuchita zinthu zosonyeza kuti ndi Akhristu oona? Ngakhale kuti pali anthu ambiri amene amati ndi Akhristu, kumbukirani mawu amene Yesu anauza otsatira ake. Iye anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.” (Mateyu 7:21) Kudziwa anthu amene akuchita chifuniro cha Atate kapena kuti amene amachita zinthu zosonyeza kuti ndi Akhristu oona, n’kuyamba kupita kumisonkhano yawo, kungakuthandizeni kuti mudzapeze madalitso ambiri mu Ufumu wa Mulungu. Kuti mudziwe zambiri zokhudza madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, funsani a Mboni za Yehova amene anakupatsani magaziniyi.—Luka 4:43.