Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Chiphunzitso cha Utatu N’chochokera M’baibulo?
▪ Chiphunzitso cha Utatu, kapena kuti chiphunzitso choti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, chimafotokozedwa m’njira zosiyanasiyana ndipo imodzi mwa njira zimenezi ndi iyi: “Pali milungu itatu (Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera) ndipo mulungu aliyense ndi wamuyaya komanso wamphamvuyonse. Palibe wamkulu kapena wamng’ono kuposa mnzake chifukwa aliyense pa atatuwa ndi mulungu komabe onse pamodzi amapanga Mulungu mmodzi.” Koma kodi Baibulo limaphunzitsadi zimenezi?
Nthawi zambiri anthu amene amakhulupirira zimenezi amanena kuti amazitenga palemba la Mateyu 28:19. Palembali pali mawu a Yesu akuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” N’zoona kuti lembali likutchula za Atate, Mwana ndi mzimu woyera. Komabe silinanene chilichonse chosonyeza kuti iwo amapanga mulungu mmodzi. Palembali, Yesu ankalamula otsatira ake omwe anali Ayuda kuti aziphunzitsa anthu ndi kuwabatiza m’dzina la Atate, Mwana ndi mzimu woyera. Kodi Ayuda unkakhulupirira zotani pa nkhaniyi?
Pangano la Chilamulo limene Aisiraeli anapatsidwa, lomwe tsopano ndi mbali ya Baibulo, linali ndi mawu akuti: “Usakhale ndi milungu ina iliyonse motsutsana ndi ine.” (Deuteronomo 5:7) Kodi mawu a palembali analankhulidwa ndi anthu angati? Lemba la Deuteronomo 6:4 limanena momveka bwino kuti: “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” Onani kuti lembali silinanene kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Pamene lamuloli linkaperekedwa, n’kuti Aisiraeli atangomasulidwa kumene ku ukapolo ku Iguputo ndipo anthu a kumeneko ankalambira milungu yomwe inkakhala itatuitatu. Chitsanzo cha milungu yotereyi ndi Osirisi, Isisi ndi Horasi. (Onani chithunzi kumanzereku) Choncho, Aisiraeli analamulidwa kuti azilambira Mulungu mmodzi yekha. Kodi n’chifukwa chiyani Aisiraeli anafunika kumvetsa bwino lamulo limeneli? Munthu wina yemwe anali rabi, dzina lake J. H. Hertz, ananena kuti: “Mawu amenewa akunena momveka bwino kuti anthu ayenera kulambira Mulungu mmodzi yekha ndipo akutsutsiratu zolambira milungu yambirimbiri. . . . M’pemphero la Ayuda lotchedwa Shema mulibe mawu akuti utatu omwe zipembedzo zachikhristu zimaphunzitsa chifukwa chiphunzitsochi chimatsutsana ndi mfundo yoti Mulungu ndi mmodzi.” *
Popeza Yesu anali Myuda, iye ankafunikanso kutsatira lamulo limeneli. Yesu atabatizidwa ndipo Mdyerekezi atamuyesa, anayankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’” (Mateyu 4:10; Deuteronomo 6:13) Tingaphunzire zinthu ziwiri kuchokera pa nkhani imeneyi. Choyamba, zikuoneka kuti Satana ankanyengerera Yesu kuti alambire iyeyo m’malo mwa Yehova. Zikanakhala kuti Yesu ndi mbali imodzi ya Mulungu, zimene Satana ankafunazi, zikanakhala zosamveka. Chachiwiri, Yesu anasonyeza momveka bwino kuti pali Mulungu mmodzi yekha amene ayenera kulambiridwa. Iye anachita zimenezi pamene ananena kuti “iye yekha.” Zikanakhala kuti Yesu ndi mbali ya Utatu, akananena kuti “ife.”
Anthu akaphunzira zolondola zokhudza Mulungu, amafuna kumutumikira ndipo amabatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” (Mateyu 28:19) Iwo amadziwa mphamvu zimene Yehova ali nazo komanso udindo umene Yesu Khristu ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Yehova. (Salimo 83:18; Mateyu 28:18) Amazindikiranso kufunika kwa mzimu woyera wa Mulungu, womwe ndi mphamvu imene iye amagwiritsa ntchito.—Genesis 1:2; Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 1:21.
Chiphunzitso cha Utatu chasokoneza anthu kwa zaka zambiri. Komabe, Yesu anathandiza ophunzira ake kudziwa zoona pa nkhaniyi ndiponso anawalimbikitsa kuti azilambira Yehova, yemwe ndi “Mulungu yekhayo amene ali woona.”—Yohane 17:3.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Pemphero lotchedwa Shema, lomwe ndi lochokera pa Deuteronomo 6:4, limasonyeza kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo pempheroli limagwiritsidwa ntchito kwambiri pa nthawi yolambira ku sunagoge.
[Mawu a Chithunzi patsamba 23]
Musée du Louvre, Paris