Zokhudza Kusunga Chinsinsi

Pofuna kukuthandizani kuti musamavutike kuchita zinthu pawebusaiti yathu, timagwiritsa ntchito ma cookies ndiponso njira zina zamakono zofanana ndi zimenezi. Ma cookies ena amathandiza kuti webusaiti yathu izigwira bwino ntchito ndipo sizingatheke kuwakana. Mukhoza kuvomereza kapena kukana ma cookies ena owonjezera, omwe cholinga chake ndi kungokuthandizani kuti musamavutike kuchita zinthu zina pawebusaiti. Sitidzagulitsa kapena kugwiritsa ntchito mauthenga amenewa pofuna kutsatsa malonda. Kuti mudziwe zambiri, werengani Ndondomeko ya Padziko Lonse ya Mmene Timagwiritsira Ntchito ma Cookies ndi Njira Zina Zamakono. Mukhoza kusintha ma settings nthawi ina iliyonse popita pa Zokhudza Kusunga Chinsinsi.

Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza mtsikana wina kuti ayambirenso kutsatira mfundo za m’Baibulo zimene anaphunzira ali mwana? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene mtsikanayu ananena.

“Ndikuona kuti panopa ndili ndi moyo waphindu.”​LISA ANDRÉ

CHAKA CHOBADWA: 1986

DZIKO: LUXEMBOURG

POYAMBA: NDINALI MWANA WOLOWERERA

KALE LANGA: Ndinakulira m’tauni ina yaing’ono yotchedwa Bertrange yomwe ili mumzinda wa Luxembourg. Tauni imeneyi ndi yaukhondo, yotukuka komanso muli chitetezo chokwanira. M’banja mwathu tilimo ana asanu ndipo ndine wamng’ono pa onse. Makolo anga ndi a Mboni za Yehova ndipo anayesetsa kutiphunzitsa ana tonsefe makhalidwe achikhristu.

Nditangopitirira zaka 13 ndinayamba kukayikira ngati zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa zilidi zoona. Poyamba ndinkanyalanyaza maganizo amenewa koma kenako chikhulupiriro changa chinayamba kufooka. Makolo anga anayesetsa kundilangiza koma ine ndinkakana kutsatira malangizo awo. Kenako ndinayamba kumacheza ndi achinyamata amene sankafuna kuuzidwa zochita koma makolo anga sankadziwa kuti ndayamba kucheza ndi anthu oterewa. Ndinkaona kuti anthu amenewa amachita zinthu mwaufulu ndipo ndi zimene nanenso ndinkafuna. Tinkakonda kuchita maphwando, zachiwerewere, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Poyamba zinkandisangalatsa kucheza ndi anthu amenewa chifukwa ndinkaona kuti amasangalala kwambiri ndi moyo.

Komabe zoona n’zakuti kuchita zimenezi sikunkandithandiza kukhala wosangalala. Tinkaona kuti moyo wathu ndi wopanda phindu ndipo aliyense ankangochita zomwe akufuna. Ngakhale ndinkachita zimenezi, ndinkada nkhawa kwambiri ndi zinthu monga kupanda chilungamo komwe kuli ponseponse m’dzikoli. M’kupita kwa nthawi, ndinayamba kumada nkhawa kwambiri n’kufika pomavutika maganizo.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndili ndi zaka 17, tsiku lina ndinkaoneka wankhawa kwambiri. Mayi anga atazindikira kuti sindikusangalala, anandilangiza kuti ndiyambirenso kuphunzira Baibulo. Anandiuza kuti ndifufuze bwinobwino zimene limaphunzitsa ndiyeno ndisankhe ndekha ngati ndikufuna kutsatira zimenezo pa moyo wanga kapena ayi. Tinakambirana momasuka kwambiri za nkhani imeneyi ndipo ichi chinali chiyambi cha kusintha kwa moyo wanga. Ndinavomera kuyamba kuphunzira Baibulo ndi mchemwali wanga, dzina lake Caroline komanso mwamuna wake Akif. Akif sanakulire m’banja la Mboni za Yehova koma anakhala wa Mboni atakula. Chifukwa cha zimene Akif anakumana nazo asanakhale wa Mboni, ndinkaona kuti ndingamasuke kulankhula naye ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri.

Ndinkadziwa kuti wa Mboni sayenera kuchita zimene ndinkachita, koma poyamba ndinkaganiza kuti ndili ndi ufulu wochita chilichonse ndi moyo wanga. Komabe kuchokera pa zimene ndinaphunzira m’Baibulo, ndinazindikira kuti zochita zanga zingakwiyitse kapena kusangalatsa Yehova. (Salimo 78:40, 41; Miyambo 27:11) Ndinazindikiranso kuti khalidwe langa limakhudza anthu ena.

Nditapitiriza kuphunzira Baibulo ndinazindikira kuti pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, ndinaphunzira maulosi ambiri a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa ndendende. Kudziwa zinthu ngati zimenezi kunandithandiza kuti ndisamakayikirenso ziphunzitso za Mboni za Yehova.

Patatha chaka chimodzi nditayambiranso kuphunzira Baibulo, ine ndi makolo anga tinapita kukachezera mchimwene wanga yemwe ankatumikira kumaofesi a Mboni za Yehova m’dziko la Germany. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri nditaona mmene mchimwene wangayu ankasangalalira. Chimwemwe choterocho n’chimene ine ndinkafunitsitsa nditakhala nacho. Ndinachitanso chidwi ndi anthu ena a Mboni amene ankatumikira pamalopa. Anthu amenewa anali osiyana kwambiri ndi anthu osaona mtima komanso ongofuna zosangalatsa amene ndinkacheza nawo. Pasanapite nthawi yaitali, ndinapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima ndipo ndinamulonjeza kuti ndimutumikira moyo wanga wonse. Ndili ndi zaka 19, ndinabatizidwa posonyeza kuti ndinadzipereka kwa Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndikuona kuti tsopano ndili ndi moyo waphindu. Panopa ndimaphunzitsa ena Baibulo kuti adziwe za Yehova ndi zimene walonjeza ndipo kuchita zimenezi kumandisangalatsa kwambiri. Nawonso makolo ndi achibale anga apindula chifukwa panopa sadandaulanso za ine.

Ndimakumbukirabe zoipa zimene ndinkapanga poyamba, koma ndimayesetsa kuti ndisamaziganizire kwambiri. M’malomwake ndimaganizira kwambiri mfundo yoti Yehova ndi wokhululuka komanso amandikonda kwambiri. Ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti mawu a pa Miyambo 10:22 ndi oona. Lemba limeneli limati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.”

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Tinkakonda kuchita maphwando, zachiwerewere, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa”

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Ndimakumbukirabe zoipa zimene ndinkapanga poyamba, koma ndimayesetsa kuti ndisamaziganizire kwambiri”