Phunzitsani Ana Anu
Kodi N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Ankamukonda Dorika?
TONSEFE timafuna kuti anthu ena azitikonda. Kodi nawenso umafuna kukondedwa?— * M’Baibulo muli nkhani ya mayi wina dzina lake Dorika, yemwe anthu ankamukonda kwambiri.
Dorika ankakhala mumzinda wa Yopa womwe unali pafupi ndi nyanja ya Mediterranean. Ndipo kuchokera ku Yopa kupita ku Yerusalemu panali mtunda wamakilomita pafupifupi 56. Dorika anali mmodzi mwa ophunzira a Yesu oyambirira.
Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anthu ankamukonda kwambiri Dorika?— Baibulo limanena kuti Dorika ankachita zinthu zabwino zambiri komanso ankapatsa anthu mphatso zabwino. Iye ankasoka zovala zabwino n’kumapatsa azimayi amasiye, kapena kuti azimayi amene amuna awo anamwalira. Komanso Dorika ankauza ena za Mulungu woona, Yehova ngati mmene Yesu ankachitira.
Kodi ukudziwa zinthu zoipa zimene zinamuchitikira
Dorika?— Iye anadwala kwambiri n’kumwalira. Zimenezi zitachitika anzake aja anakhumudwa kwambiri. Choncho anatuma anthu kuti apite kukaitana mtumwi Petulo ndipo anayenera kuyenda mtunda wamakilomita 16 kuti amupeze. Anthuwa anapempha mtumwi Petulo kuti apite mwamsanga ku Yopa. Petulo atafika ku Yopa, anakwera m’chipinda cham’mwamba kumene Dorika anali. Pa nthawiyi n’kuti azimayi akulira kwinaku akumusonyeza Petulo zovala zomwe Dorika anawasokera.Kenako Petulo anauza anthu onse kuti atuluke m’chipindamo. Petulo komanso atumwi ena anali atachitapo zozizwitsa zina koma anali asanaukitsepo munthu wakufa. Kodi ukuganiza kuti Petulo anatani pamenepa?—
Iye anagwada pafupi ndi pamene panali mtembo wa Dorika ndipo anapemphera kwa Yehova. Kenako anauza Dorika kuti adzuke ndipo anadzukadi. Zitatere, Petulo anamugwira dzanja n’kumuimiritsa. Ndiyeno anaitana azimayi amasiye aja komanso anthu ena kuti adzaone kuti Dorika wauka. Kodi ukuganiza kuti anthuwa anamva bwanji ataona kuti Dorika waukitsidwa?—
Tsopano tiye tione zimene tikuphunzirapo pa nkhani ya kuukitsidwa kwa Dorika. Tikuphunzirapo kuti ukamakonda kuthandiza ena, anthu ambiri azikukonda. Komanso chofunika kwambiri n’chakuti ukamakonda kuthandiza ena, Mulungu azikukonda kwambiri ndipo sadzakuiwala. Iye sadzaiwala zinthu zabwino zimene umachitira ena ndipo adzakupatsa moyo wosatha m’dziko latsopano. M’dziko limeneli zinthu zonse zizidzachitika mwachilungamo ndipo anthu adzakhala osangalala zedi.
Werengani Mavesi awa
^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzera muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.