Kodi Masiku Ano Mulungu Ndi Amene Amachititsa Anthu Kulankhula Malilime?
Kodi Masiku Ano Mulungu Ndi Amene Amachititsa Anthu Kulankhula Malilime?
MUNTHU wina, dzina lake Devon, anati: “Sindikumvetsa. Mlungu uliwonse kutchalitchi kwathu, anthu ambiri amaoneka kuti amalandira mzimu woyera ndipo amayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana. Chikhalirecho ena mwa anthu amenewa amachita makhalidwe oipa kwambiri. Koma ineyo ndimayesetsa kupewa makhalidwe oipa amenewa. Ngakhale zili choncho, kaya ndilimbike bwanji kupemphera kuti ndilandire mphatso imeneyi ya mzimu woyera, sizitheka. Kodi chimachititsa n’chiyani?”
Ndiyeno pali Gabriel. Nayenso amapemphera m’tchalitchi chinachake chimene anthu ake amaoneka kuti amalandira mzimu woyera ndipo amalankhula malilime. Iye anafotokoza kuti: “Chimene chimandisowetsa mtendere kwambiri ndi chakuti, ndikamapemphera, anthu ena amandisokoneza chifukwa amasokosera. Sindimva zimene akunena, komanso ngakhale iwowo sadziwa zimene akulankhula. Palibe aliyense amene amapindula ndi zimene amalankhulazo. Kodi si paja mphatso ya mzimu wa Mulungu imayenera kukhala yothandiza?”
Zimene zinachitikira Devon ndi Gabriel zikutichititsa kufunsa funso lofunika kwambiri lakuti: Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti anthu ena azilankhula malilime, ngati zilili m’matchalitchi ena masiku ano? Kuti tiyankhe funso limeneli, tingachite bwino kuonanso nkhani yokhudza Akhristu amene anapatsidwa mphatso yolankhula malilime mu mpingo wachikhristu woyambirira.
“Anayamba Kulankhula Zinenero Zosiyanasiyana”
M’Baibulo timawerenga za amuna ndi akazi amene analandira mphamvu yolankhula zinenero zina zimene sankazidziwa. Zimenezi zinachitika koyamba pa Pentekosite mu 33 C.E., patangodutsa milungu yochepa kuchokera pamene Yesu Khristu anaphedwa ndi kuukitsidwa. Pa tsikuli ku Yerusalemu, ophunzira a Yesu okwana 120 “anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana.” Alendo ochokera m’mayiko ena “anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense wa iwo anawamva akulankhula m’chinenero chake.”—Machitidwe 1:15; 2:1-6.
Baibulo limanenanso za otsatira Yesu oyambirira amene ankalankhulanso zinenero zina mozizwitsa. Mwachitsanzo mtumwi Paulo atapatsidwa mphamvu ndi mzimu woyera, analankhula zinenero zosiyanasiyana. (Machitidwe 19:6; 1 Akorinto 12:10, 28; 14:18) Koma n’zoonekeratu kuti mphatso iliyonse ya mzimu woyera wa Mulungu ngati imeneyi iyenera kukhala ndi cholinga chinachake chabwino. Ndiye kodi n’chifukwa chiyani anthu ankalankhula malilime m’nthawi ya Akhristu oyambirira?
Chinali Chizindikiro Choti Mulungu Akuwathandiza
M’kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Korinto, amene ena mwa iwo ankalankhula 1 Akorinto 14:22) Choncho, kulankhula malilime komanso kuchita zozizwitsa zina kunali chizindikiro chosonyeza kuti Mulungu ankathandiza mpingo wachikhristu, umene unali utangokhazikitsidwa kumene. Zozizwitsa zimenezo zinali ngati chikwangwani cha pamsewu cholozera kumene anthu ofunafuna choonadi ayenera kupita kuti akapeze anthu osankhidwa ndi Mulungu.
malilime, iye anafotokoza kuti “malilimewo ndi chizindikiro kwa osakhulupirira.” (N’zochititsa chidwi kuti Baibulo silinena kuti Yesu, kapena mneneri wina aliyense amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, ankalankhula mozizwitsa zinenero zimene sanaphunzirepo. Choncho, zikuoneka kuti mphatso yolankhula zinenero zosiyanasiyana imene ophunzira a Yesu analandira nthawi imeneyi inali ndi cholinga chapadera.
Kulankhula Malilime Kunathandiza pa Ntchito Yofalitsa Uthenga Wabwino
Chakumayambiriro kwa utumiki wake, Yesu analangiza ophunzira ake kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa Ayuda anzawo okha. (Mateyu 10:6; 15:24) Chifukwa cha zimenezi, ophunzira a Yesu kawirikawiri sankalalikira kumadera kumene kunali Ayuda ochepa. Koma pasanapite nthawi zimenezi zinasintha.
Mu 33 C.E., Yesu, yemwe pa nthawiyi anali ataukitsidwa, analamula otsatira ake kuti ‘akaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake.’ Iye anawauzanso kuti adzakhala mboni zake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mateyu 28:19; Machitidwe 1:8) Kuti athe kufalitsa uthenga wabwino padziko lonse anafunika kuti azilankhula zinenero zambiri kuwonjezera pa Chiheberi.
Komabe ambiri mwa ophunzira a Yesu oyambirira anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Machitidwe 4:13) Ndiyeno akanatha bwanji kulalikira m’madera akutali olankhula zinenero zachilendo zimene iwo sanamvepo ndiponso zoti sankatha kuzilankhula? Mzimu woyera unathandiza ena mwa anthu amene ankalalikira uthenga wabwino mwakhama kuti azilankhula bwinobwino zinenero zina zimene anali asanaziphunzirepo.
Choncho, tingaone kuti mphatso ya malilime inathandiza mbali ziwiri. Choyamba, inali ngati chizindikiro chosonyeza kuti Mulungu akuthandiza mpingo wachikhristu. Chachiwiri, inathandiza kuti Akhristu a m’nthawi imeneyo athe kulalikira uthenga wabwino kwa anthu olankhula zinenero zina. Kodi kulankhula malilime kumene anthu amachita m’matchalitchi osiyanasiyana masiku ano kukukwaniritsa zolinga zimenezi?
Kodi Kulankhula Malilime Kumene Anthu Amachita Masiku Ano Ndi Chizindikiro Chakuti Mulungu Akuwathandiza?
Tiyerekezere kuti mukufuna kuika chikwangwani chimene chili ndi uthenga wofunika kwambiri kwa anthu a m’dera lanu, kodi mungachiyike pati? Kodi mungachiyike m’nyumba? N’zachidziwikire kuti simungachite zimenezo. Nkhani ya m’Baibulo yonena zimene zinachitika pa tsiku la Pentekosite imati “khamu” la anthu odutsa anaona chizindikiro chosonyeza kuti ophunzira a Yesu ankalankhula malilime mozizwitsa. Zotsatira zake zinali zakuti tsiku limenelo, “anthu pafupifupi 3,000” anawonjezeka mumpingo wachikhristu. (Machitidwe 2:5, 6, 41) Ngati anthu masiku ano amanena kuti amalankhula malilime koma n’kumachitira zimenezo m’kati mwa matchalitchi awo, kodi zingatheke bwanji kuti anthu ena osakhulupirira aone chizindikiro chimenecho?
Mawu a Mulungu amatchula dama ndi ‘ntchito zina za thupi’ pa mndandanda wa zinthu zimene zimatsutsana ndi mzimu woyera. Ndipo amati “anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:17-21) Mukadzaona anthu amene makhalidwe awo ndi okayikitsa akulankhula malilime, dzadzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amenewa si ongofuna kusocheretsa anzawo?’ Funso limeneli ndi lomveka chifukwa Mulungu sapereka mzimu woyera kwa anthu amene amapitirizabe kuchita zinthu zimene Mawu ake amaletsa. Anthu ochita zimenezi ali ngati munthu amene waika chikwangwani cholozera anthu kumalo olakwika.
Kodi Masiku Ano Malilime Akuthandiza Kufalitsa Uthenga Wabwino?
Nanga bwanji za chifukwa china chija chimene anthu ena a m’nthawi ya atumwi ankalankhulira malilime? Kodi kulankhula malilime kumene anthu amachita masiku ano m’matchalitchi osiyanasiyana, kukuthandiza kuti uthenga wabwino ulalikidwe kwa anthu azinenero zina? Kumbukirani kuti anthu amene anali ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E. anali ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndipo ankamva zilankhulo zimene ophunzira
a Yesu analankhula mozizwitsa. Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amalankhula malilime masiku ano nthawi zambiri amalankhula zinthu zoti aliyense sangamve.Zimachita kuonekeratu kuti malilime amene anthu amalankhula masiku ano ndi osiyana kwambiri ndi malilime amene otsatira a Yesu oyambirira ankalankhula chifukwa cha mphatso ya mzimu woyera. Ndipo palibe umboni uliwonse wotsimikizira kuti anthu ena analandira mphatso imeneyi atumwi onse atatha kumwalira. Anthu amene amakonda kuwerenga Baibulo sadabwa ndi zimenezi. Chifukwa ponena za mphatso zochitira zozizwitsa kuphatikizapo kulankhula malilime, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba ulosi wakuti: ‘zidzatha.’ (1 Akorinto 13:8) Ndiyeno kodi munthu angadziwe bwanji anthu amene ali ndi mzimu woyera masiku ano?
Kodi Ndani Akusonyeza Kuti Ali ndi Mzimu Woyera Masiku Ano?
Yesu ankadziwa kuti anthu adzasiya kulankhula malilime patangopita nthawi yochepa kwambiri mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa. Patangotsala nthawi yochepa kuti aphedwe, Yesu anauza ophunzira ake chizindikiro chimene sichidzatha, chodziwikitsa amene akulambira Mulungu m’njira yolondola. Iye anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:35) Ndipotu vesi lija, limene limanena kuti mphatso zochita zozizwitsa zidzatha, limanenanso kuti: “Chikondi sichitha.”—1 Akorinto 13:8.
M’Baibulo, chikondi n’choyambirira pa mndandanda wa “makhalidwe” amene mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa. (Agalatiya 5:22, 23) Choncho anthu amenedi ali ndi mzimu woyera wa Mulungu, umenenso ndi chizindikiro chosonyeza kuti Mulungu akuwathandiza, amakondana mochokera pansi pa mtima. Komanso khalidwe lachitatu limene mzimu umatulutsa ndi mtendere. Choncho anthu amene ali ndi mzimu woyera masiku ano amakhala amtendere. Iwo amayesetsa kupewa makhalidwe oipa monga chidani, kusankhana mitundu ndiponso chiwawa.
Kumbukiraninso mawu a Yesu opezeka pa lemba la Machitidwe 1:8. Iye analosera kuti ophunzira ake adzalandira mphamvu kuti akhale mboni zake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” Yesu anasonyezanso kuti ntchito imeneyi idzapitirira “mpaka mapeto a dziko lapansi.” (Mateyu 28:20, King James Version) Zimenezi zikusonyeza kuti ntchito yolalikirayi, imene ikuchitika padziko lonse, idzakhalabe chizindikiro cha anthu amene alandiradi mphamvu ya mzimu woyera.
Ndiyeno kodi inuyo mukuiona bwanji nkhaniyi? Kodi ndi mpingo uti umene mukuona kuti anthu ake ali ndi mzimu woyera? Kodi ndani masiku ano amene akusonyeza kuti ali ndi chipatso cha mzimu monga chikondi ndi mtendere? Kodi ndani padziko lonse amene amalolera kuzunzidwa ndi maboma chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo? (Yesaya 2:4) Kodi ndi anthu ati amene amayesetsa kupewa ntchito zathupi monga chiwerewere, moti amachotsa munthu mumpingo wawo ngati amachita zimenezi osalapa? (1 Akorinto 5:11-13) Kodi ndi mpingo uti umene umalalikira padziko lonse za uthenga wabwino wonena kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto a anthu?—Mateyu 24:14.
Ofalitsa magazini ino akunena mosakayikira kuti amene akutsogoleredwa ndi mzimu woyera masiku ano, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena ndi Mboni za Yehova. Mungachite bwino kudziwa zimene iwo amaphunzitsa kuti muone ngati akutsogoleredwadi ndi Mulungu.