Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinachititsa Rasi wina kumeta tsitsi ndiponso kusiya kudana ndi azungu? Nanga zinatani kuti mnyamata wokonda ndewu asinthe khalidwe n’kusiya kutolera ndalama za anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo? Tamvani zimene anthu amenewa ananena.

“Ndinasiya ngakhale kudana ndi azungu.”​—HAFENI NGHAMA

ZAKA: 34

DZIKO: ZAMBIA

POYAMBA: ANALI RASI

KALE LANGA: Ndinabadwira ku Zambia kumalo ena a anthu othawa kwawo. Mayi anga anathawa ku Namibia pamene kunali nkhondo ndipo analowa chipani cha South West Africa People’s Organization (SWAPO). Chipani chimenechi chinkamenyana ndi boma la South Africa limene panthawiyo linkalamulira dziko la Namibia.

Ndinakhala malo osiyanasiyana a anthu othawa kwawo mpaka pamene ndinafika zaka 15. Achinyamata amene tinali m’malo amenewa, amene anali m’manja mwa chipani cha SWAPO, tinkaphunzitsidwa kuti tidzakhale m’magulu omenyera ufulu wa dziko lathu. Tinkaphunzitsidwanso kuti tizingoganizira zandale ndiponso kuti tizidana ndi azungu.

Ndili ndi zaka 11, ndinkafuna kulowa tchalitchi china chachikhristu cha ku malo a anthu othawa kwawo kumene ndinkakhala. Tchalitchichi chinali cha anthu ochokera m’zipembedzo zosiyanasiyana, monga Katolika, Lutheran, Angilikani ndi zina zotero. M’busa amene ndinamuuza zimenezi anandilangiza kuti ndisalowe tchalitchi chimenechi. Kuyambira pamenepo, ndinayamba kukayikira zoti kuli Mulungu. Koma chifukwa chokonda kumvera nyimbo za chamba cha rege ndiponso kufunitsitsa kuthetsa mavuto amene anthu akuda a ku Africa kuno amakumana nawo, ndinalowa chipembedzo cha Marasi. Apa n’kuti ndili ndi zaka 15. Ndinayamba kusunga tsitsi, kusuta chamba, ndiponso ndinasiya kudya nyama. Komanso ndinayamba kumenyera ufulu wa anthu akuda. Komabe sindinasiye khalidwe lokonda akazi, kuonera mafilimu olimbikitsa zachiwawa komanso sindinasiye kutukwana.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: M’chaka cha 1995, ndili ndi zaka pafupifupi 20, ndinayamba kuganizira kwambiri za tsogolo langa. Ndinkawerenga mabuku onse a Marasi amene ndinkapeza. Ena mwa mabukuwa ankatchula mavesi a m’Baibulo, koma ankawafotokoza mosamveka bwino. Choncho ndinaganiza zowerenga ndekha Baibulo.

Kenako, mnzanga wina amenenso anali Rasi anandipatsa buku lothandiza kuphunzira Baibulo lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ndinayamba kuphunzira pandekha bukuli pogwiritsa ntchito Baibulo. Patapita nthawi, ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anandithandiza kupitiriza kuphunzira Baibulo.

Zinandivuta kwambiri kusiya fodya ndi kumwa mowa mwauchidakwa komabe pamapeto pake ndinakwanitsa. (2 Akorinto 7:1) Ndinayamba kudzisamalira ndipo ndinameta tsitsi langa. Ndinasiyanso kuonera mafilimu olaula ndi achiwawa ndiponso kutukwana. (Aefeso 5:3, 4) M’kupita kwa nthawi, ndinasiya ngakhale kudana ndi azungu. (Machitidwe 10:34, 35) Kuti ndithe kusintha moyo wanga, ndinasiya kumvera nyimbo zolimbikitsa kusankhana mitundu. Ndinasiyanso kucheza ndi anzanga akale amene akanandichititsa kuti ndiyambirenso moyo wanga wakale.

Nditasintha moyo wanga, ndinayamba kufunafuna kumene kunali Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Nditaipeza, ndinapempha kuti nanenso ndikhale wa Mboni. Kenako, munthu wina anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Patapita nthawi, ndinaganiza zoti ndibatizidwe kuti ndikhale wa Mboni za Yehova koma achibale anga sanasangalale. Mayi anga anandiuza kuti ndisankhe chipembedzo china chilichonse chachikhristu koma osati cha Mboni za Yehova. Amalume anga ena, amene anali ndi udindo waukulu m’boma, ankakhalira kundinena chifukwa cholowa chipembedzo cha Mboni za Yehova.

Komabe, nditaphunzira za mmene Yesu ankakhalira ndi anthu ndiponso kugwiritsa ntchito malangizo ake, ndinkatha kupirira ndikamatsutsidwa ndiponso kunyozedwa. Nditayerekezera zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa ndi zimene Baibulo limanena, ndinatsimikiza kuti ndapeza chipembedzo choona. Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zimatsatira lamulo la m’Baibulo loti tizilalikira ena. (Mateyo 28:19, 20; Machitidwe 15:14) Ndiponso a Mboni salowerera ndale.​—Salmo 146:3, 4; Yohane 15:17, 18.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Kuphunzira ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wanga kwandithandiza pa zinthu zambiri. Mwachitsanzo, kusiya kusuta chamba kwandithandiza kupewa kuwononga ndalama zambiri zomwe ndinkagulira chamba mwezi uliwonse. Komanso ndinasiya kuona zilubwelubwe, bongo wanga ukugwira ntchito bwino ndiponso tsopano ndine wathanzi.

Moyo wanga tsopano uli ndi cholinga ndipo ndili ndi tsogolo labwino. Zimenezi n’zimene ndakhala ndikulakalaka kuyambira ndili wamng’ono. Koma chofunika kwambiri kuposa zonse n’chakuti, tsopano ndimaona kuti ndili pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.​—Yakobe 4:8.

“Ndaphunzira kuugwira mtima.”​—MARTINO PEDRETTI

ZAKA: 43

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: ANKAGULITSA MAKHWALA OSOKONEZA BONGO

KALE LANGA: Banja lathu linkasamukasamuka pamene ndinali wamng’ono. Ndakhalapo m’matawuni ang’onoang’ono, mumzinda waukulu, ndiponso panyumba ya mishoni imene ili kumudzi winawake. Ndimakumbukira zinthu zosangalatsa zimene ndinkachita kumudzi limodzi ndi asuweni ndiponso amalume anga, monga kuwedza nsomba, kusaka nyama ndiponso kusema zinthu zosiyanasiyana.

Bambo anga anali katswiri wankhonya ndipo anayamba kundiphunzitsa nkhonya ndili wamng’ono kwambiri moti ndinkakonda kwambiri ndewu. Nditakwanitsa zaka 13 ndinayamba kumwa mowa kumabala. Ineyo ndi anzanga ena tinkachita kuputa dala anthu ena kuti timenyane nawo. Tinkatha kumenyana ndi gulu la anthu 20 kapena kuposa pamenepa pogwiritsira ntchito mipeni ndi zibonga.

Kuti ndipeze ndalama, ndinkagulitsa mankhwala osokoneza bongo ndiponso katundu amene anthu ogwira ntchito m’madoko ankaba kuntchito kwawo. Ndinkachitanso ganyu yotolera ndalama za anthu ena ogulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo munthu akalephera kupereka ndalamazo, ndinkamuopseza ndi mfuti. Ndinkafuna kuti ndizidzagwira ganyu kwa anthu andale yopha adani awo. Mfundo imene ndinkayendera inali yakuti, Ipha apo ayi udzaphedwa.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Ndili mnyamata ndinamva za Mboni za Yehova. Ndikukumbukira kuti ndili ndi zaka za m’ma 20, ndinafunsa mayi anga ngati ankadziwa ena mwa anthu a Mboni. Patangodutsa masiku awiri, wa Mboni wina, dzina lake Dixon, anabwera kunyumba kwathu. Titakambirana kwakanthawi ndithu, iye anandiitanira kumsonkhano wawo. Ndinapitadi kumsonkhanoko ndipo ndakhala ndikusonkhana ndi Mboni za Yehova kwa zaka zoposa 20 tsopano. Mbonizi zinkagwiritsa ntchito Baibulo poyankha funso lililonse limene ndinkafunsa.

Ndinasangalala kwambiri nditaphunzira kuti Mulungu amakonda munthu wina aliyense, ngakhale amene samumvera. (2 Petulo 3:9) Ndinazindikira kuti iye ndi Atate wachikondi amene angandisamalire ngakhale anthu ena onse atanditaya. Ndipo kuphunzira kuti Mulungu angathe kundikhululukira machimo anga ngati nditasiya kuchita zoipa, kunandilimbikitsa. Mfundo ya pa Aefeso 4:22-24 inandithandiza kwambiri. Mavesi amenewa anandilimbikitsa ‘kuvula umunthu wakale’ ndi “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.”

Panapita nthawi yaitali kuti ndikwanitse kusintha moyo wanga. Ndinkatha kukhala Lolemba mpaka Lachisanu popanda kugwira mankhwala osokoneza bongo aliwonse, koma kumapeto a mlungu ndikakumana ndi anzanga amene ndinkacheza nawo poyamba, ndinkalephera kudziletsa. Ndinadziwa kuti ndiyenera kusamuka kuti nditalikirane ndi anzanga amenewa n’cholinga choti ndithe kusintha moyo wanga, choncho ndinaganiza zosamukira kudziko lina. Pamene ndinkanyamuka, anzanga ena anapempha kuti andiperekeze ndipo ndinawalola. Ulendo wathu uli mkati, iwo anayamba kusuta chamba ndipo anandipatsa kuti nanenso ndisute nawo. Koma ndinakana n’kuwauza kuti ndikufuna kusiya kusuta, ndipo titafika pamalire a dzikoli iwo anabwerera. Patapita nthawi ndinamva kuti nditangosiyana nawo, iwo anakaba pabanki ina moopseza ndi mfuti.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Nditangosiya kucheza ndi anzanga amenewa, ndinaona kuti sizinandivute kusiya makhalidwe oipa. Kenako, mu 1989, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Patapita nthawi, makolo anga ndiponso mlongo wanga, nawonso anaphunzira choonadi n’kukhalanso Mboni za Yehova.

Tsopano ndatha zaka 17 ndili pabanja ndipo ndili ndi ana okongola atatu. Ndaphunzira kuugwira mtima, ngakhale wina atachita kundiyamba. Ndaphunzira kukonda anthu a “fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chivumbulutso 7:9) Ndimaona kuti mawu a Yesu akuti: “Ngati mukhala m’mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga, mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani,” akwaniritsidwa ine.​—Yohane 8:31, 32.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Kuti ndithe kusintha moyo wanga, ndinasiya kumvera nyimbo zolimbikitsa kusankhana mitundu

[Mawu Otsindika patsamba 20]

Tinkatha kumenyana ndi gulu la anthu 20 kapena kuposa pamenepa pogwiritsira ntchito mipeni ndi zibonga