Anakhalabe Wokhulupirika Panthawi Yovuta
Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Anakhalabe Wokhulupirika Panthawi Yovuta
PANTHAWI ina Yesu akuphunzitsa anthu m’sunagoge ku Kaperenao, Petulo anawayang’anitsitsa mwachidwi. Petulo anali wochokera m’tawuni imeneyi ndipo ankachitira bizinesi yake ya nsomba m’tawuni yomweyi, kufupi ndi gombe la nyanja ya Galileya. Anzake ambiri, abale ake komanso anthu amene ankachita nawo malonda ankakhalanso komweko. N’zosakayikitsa kuti panthawiyi, Petulo anasangalala ndipo ankayembekezera kuti anthu a m’tawuni yakwawo asangalalanso kwambiri kuphunzira za Ufumu wa Mulungu kuchokera kwa Mphunzitsi waluso kwambiri ameneyu. Koma zimene zinachitika zinali zosiyana ndi zimene iye ankayembekezera.
Panthawiyi, anthu ambiri anali atasiya kumvetsera ndipo ena anayamba kung’ung’udza chifukwa chosagwirizana ndi zimene Yesu ankaphunzitsa. Koma zimene Petulo anakhumudwa nazo kwambiri ndi zimene ena mwa ophunzira a Yesu anachita. Nkhope zawo zinayamba kusonyeza kuti asiya kusangalala ndi zimene Yesu akuphunzitsa ndipo alibe chidwi chophunzira zinthu zatsopano ndiponso choonadi kuchokera kwa Yesu. Ankaoneka kuti asokonezeka ndiponso akwiya. Ena anayamba kulankhula mokweza kuti zimene Yesu ananena zinali zozunguza. Iwo sanafunenso kumvetsera, choncho anatuluka m’sunagogemo ndipo anasiyiratu kutsatira Yesu.
Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri kwa Petulo ndi atumwi anzake. Iye sanamvetse tanthauzo la zimene Yesu anaphunzitsa patsikuli. N’zosakayikitsa kuti Petulo ankadziwa kuti popanda kumvetsetsa tanthauzo la mawuwa munthu akhoza kukhumudwa. Ndiye kodi iye anatani? Aka sikanali koyamba kuti chikhulupiriro chake mwa Yesu chiyesedwe komanso sikanali komaliza. Tiyeni tione mmene chikhulupiriro cha Petulo chinamuthandizira kuthana ndi mavuto amenewa ndiponso kuti apitirizebe kukhala wokhulupirika.
Anakhalabe Wokhulupirika Ena Atasiya Kutsatira Yesu
Nthawi zambiri, Petulo ankadabwa ndi zimene Yesu anali kuchita. Kawirikawiri Yesu ankachita ndiponso kulankhula zinthu zosiyana ndi zimene anthu ankayembekezera. Mwachitsanzo, dzulo lake Yesu anali atadyetsa anthu ambirimbiri mozizwitsa. Chifukwa cha zimenezi, anthuwo ankafuna kumulonga ufumu. Koma iye anachita zinthu zimene zinadabwitsa anthu ambiri chifukwa anachoka pamalowa ndipo anauza ophunzira ake kuti akwere boti kupita ku Kaperenao. Ophunzirawo akuyendetsa boti usiku wa tsiku limeneli panyanja ya Galileya, Yesu anachitanso chinthu china chomwe chinawadabwitsa kwambiri. Iwo anamuona iye akubwera poteropo akuyenda koma osamira ngakhale kuti panyanjapo panali mafunde. Zimenezi zinathandiza kwambiri Petulo kudziwa kufunika kokhala ndi chikhulupiriro. *
M’mawa mwake, iwo anazindikira kuti khamu la anthu lija linkawatsatira. Koma zikuoneka kuti
ankawatsatira ndi cholinga chakuti Yesu awapatsenso chakudya china mozizwitsa, osati ndi cholinga chakuti awaphunzitse zinthu zauzimu. Motero, Yesu anawadzudzula chifukwa cha mtima wawo wokonda zinthu zakuthupi. Atafika m’sunagoge ku Kaperenao, Yesu anapitiriza nkhani ya chakudya ija, ndipo anawauza zinthu zimene sankayembekezera. Cholinga chake chinali choti awaphunzitse mfundo yovuta kumva koma yofunika kwambiri.Yesu ankafuna kuti anthuwa asamangomutsatira n’cholinga choti awapatse chakudya. Koma ankafunanso kuti iwo adziwe kuti iye anatumidwa ndi Mulungu n’cholinga choti adzawafere kuti iwo apeze moyo wosatha. Choncho Yesu anawauza fanizo lofotokoza kuti iye ali ngati mana, kapena kuti chakudya chochekera kumwamba chomwe anthu ankadya m’nthawi ya Mose. Anthu ena atasonyeza kuti sakugwirizana ndi zimene ananenazi, iye anafotokoza fanizo lomveka bwino kuti anthu ayenera kudya thupi lake ndi kumwa magazi ake kuti apeze moyo. Atanena zimenezi, ena mwa anthuwo anakwiya kwambiri ndipo anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza; ndani angamvetsere zimenezi?” Ndipo, ambiri mwa ophunzira a Yesu anaganiza zosiya kuyenda naye. *—Yohane 6:48-60, 66.
Koma kodi Petulo anachita chiyani? Iyenso ayenera kuti anasokonezeka maganizo ndi zimene Yesu ananenazi. Panthawiyi iye sankadziwa kuti Yesu ayenera kufa kaye kuti akwaniritse cholinga cha Mulungu. Koma kodi Petulo anatengeka n’kusiya kutsatira Yesu monga anachitira ophunzira omwe anasintha maganizo aja? Ayi. Pali chinachake chimene chinachititsa Petulo kuti asatsatire maganizo a anzakewo. Kodi chinthu chimenechi chinali chiyani?
Yesu anayang’ana atumwi ake n’kuwafunsa kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” (Yohane 6:67) Funsoli linali la atumwi ake onse 12 koma ndi Petulo yekha amene anayankha. Petulo anachita zimenezi mwina chifukwa choti anali wamkulu kwambiri pagulu lonselo. Kaya Petulo ankachita zimenezi pa chifukwa chiti, koma mfundo ndi yakuti iye anali wokonda kulankhula ndipo kawirikawiri iye sankaopa kulankhula zimene zinali m’maganizo mwake. Zikuoneka kuti zimene zinali m’maganizo mwake ndi mawu abwino komanso osaiwalika akuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”—Yohane 6:68.
Mawu amenewa ndi ogwira mtima kwambiri. Petulo ankakhulupirira kwambiri Yesu ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti akhale wokhulupirika kwa iye. Petulo anadziwa kuti palibenso Mpulumutsi wina kupatulapo Yesu ndi kuti zimene Yesu ankaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu n’zothandiza kuti anthu apulumuke. Petulo ankadziwanso kuti ngakhale kuti panali zinthu zimene sankazimvetsa, panalibe kwina kumene akanapita kuti apeze moyo wosatha ndiponso kuti Mulungu apitirize kumukonda.
Kodi inunso muli ndi maganizo ofanana ndi a Petulo? N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri masiku ano amanena kuti amakonda Yesu koma akakumana ndi mayesero amalephera kukhala okhulupirika kwa iye. Ngati tikufunadi kukhala okhulupirika kwa Yesu tiyenera kuona mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa mofanana ndi mmene Petulo ankazionera. Tiyenera kuphunzira, kumvetsa ndiponso kutsatira mfundozo ngakhale zitakhala kuti n’zosiyana ndi zimene timayembekezera komanso zimene tingakonde. Tidzapeze moyo wosatha umene Yesu analonjeza, pokhapokha ngati tili okhulupirika.
Anakhalabe Wokhulupirika Atadzudzulidwa
Zimenezi zitachitika, Yesu ndi atumwi ake komanso ophunzira ake ena anayamba ulendo wautali wolowera chakumpoto. Iwo akuyenda, anayamba kuona phiri la Herimoni chakumpoto kwenikweni kwa Dziko Lolonjezedwa. Nthawi zina, munthu akakhala kunyanja ya Galileya, ankatha kuona phirili, lomwe nthawi zambiri linkakutidwa ndi chipale chofewa. Paulendowu, iwo anadutsa njira yodzera m’midzi ya pafupi ndi Kaisareya wa Filipi ndipo phirilo linkaoneka lalitali pomwe ankaliyandikira. * Podutsa m’dera lokongolali, ankaona mbali yaikulu ya chigawo chakum’mwera kwa Dziko Lolonjezedwa. Kenako, Yesu anafunsa otsatira ake funso lofunika kwambiri.
Panthawiyi Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthuwa akumati ine ndine ndani?” Tingathe kuona Petulo m’maganizo mwathu akumuyang’anitsitsa Yesu, n’kuganizira za kukoma mtima komanso nzeru za Mbuye wakeyo. Yesu ankafunitsitsa kudziwa zimene anthu ankaganiza kuchokera pa zimene anaona ndi kumva za iye. Ophunzirawo anayankha funsoli pobwereza zina mwa zinthu zolakwika zimene anthu ambiri ankanena zokhudza Yesu. Koma Yesu ankafuna kudziwa ngati ophunzira akewo nawonso anali ndi maganizo olakwika amenewa. Choncho, iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?”—Luka 9:18-22.
Apanso Petulo sanachedwe kuyankha. Iye anayankha momveka komanso molimba mtima zinthu zimenenso zinali m’maganizo a anthu ambiri amene ankamutsatira. Iye anati: “Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” Yesu ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi Petulo chifukwa cha yankho lake ndipo anamuyamikira. Iye anauza Petulo kuti ndi Yehova Mulungu, osati munthu, amene anam’thandiza kudziwa mfundo ya choonadi imeneyi. Apa Petulo anathandizidwa kudziwa imodzi mwa mfundo zofunika kwambiri za choonadi yokhudza Mesiya, kapena kuti Khristu, amene analonjezedwa kuyambira kale kwambiri.—Mateyo 16:16, 17.
Khristu ameneyu ndi amene aneneri analosera kalekale kuti ndi mwala umene amisiri omanga nyumba adzaukana. (Salmo 118:22; Luka 20:17) Yesu ankaganizira ulosi umenewu pamene ananena kuti Yehova adzakhazikitsa mpingo pamwala umenewu kapena kuti thanthwe, lomwe Petulo anali atangolitchula kumene. * Kenako Yesu anapereka kwa Petulo udindo wofunika kwambiri pampingo. Zimenezi sizinatanthauze kuti Petulo ndi wapamwamba kuposa atumwi ena, monga mmene anthu ena amaganizira, koma anangokhala ndi udindo basi. Iye anapatsa Petulo “makiyi a ufumu.” (Mateyo 16:19) Zimenezi zinatanthauza kuti Petulo adzatsegula khomo lakuti magulu atatu a anthu alowe mu Ufumu wa Mulungu. Maguluwa anali Ayuda, Asamariya ndipo kenako anthu akunja.
Komabe, nthawi ina Yesu ananena kuti amene apatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunidwa kwa Luka 12:48) Yesu anapitiriza kuuza ophunzira ake mfundo zofunika kwambiri za choonadi zokhudza iyeyo monga Mesiya, kuphatikizapo kuti iye anali atatsala pang’ono kuzunzidwa ndi kuphedwa ku Yerusalemu. Koma Petulo atamva zimenezi anakhumudwa kwambiri ndipo anatengera Yesu pambali n’kumudzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye; musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.”—Mateyo 16:21, 22.
iwo, ndipo mawu amenewa ndi oona tikaganizira za Petulo. (Yesu atamva zimenezi anatembenuka n’kuyang’ana atumwi ena omwe mwina analinso ndi maganizo ngati a Petulo. Kenako anati: “Ndichokere, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mateyo 16:23; Maliko 8:32, 33) Petulo ayenera kuti anadabwa ndi yankho la Yesu chifukwa iye ananena zimenezi pomufunira zabwino. Koma zimene Yesu ananenazi n’zothandizanso kwa ife chifukwa n’zosavuta kuyamba kutsatira maganizo athu m’malo motsatira zimene Mulungu akufuna. Ngakhale titakhala ndi maganizo ofuna kuthandiza ena, tikamatsatira maganizo athu, tingakhale tikupititsa patsogolo zolinga za Satana mosadziwa. Kodi Petulo atadzudzulidwa anatani?
Petulo ankadziwa kuti Yesu sankatanthauza kuti iyeyo ndi Satana Mdyerekezi weniweni. Ndipotu, zimene Yesu ananena kwa Petulo sizinali zofanana ndendende ndi zimene anauza Satana nthawi ina m’mbuyomo. Tikutero chifukwa polankhula ndi Satana, Yesu anati: “Choka Satana!” pamene polankhula ndi Petulo anati: “Ndichokere, Satana!” (Mateyo 4:10) Apa Yesu anasonyeza kuti sakudana ndi Petulo, mtumwi yemwe iye ankaona kuti ali ndi makhalidwe ambiri abwino. Iye anangofuna kumudzudzula kuti asiye kuganiza molakwika. Apa mfundo ndi yakuti Petulo anafunika kukhala wotsatira wa Yesu wothandiza kwambiri, osati wokhala patsogolo n’kumapunthwitsa Mbuye wake.
Kodi Petulo anatsutsana ndi Yesu, n’kukwiya kapena kusiyiratu kulankhula naye? Ayi. Iye analandira uphungu modzichepetsa. Mwa kuchita zimenezi, Petulo anasonyeza kuti ndi wokhulupirika. Anthu onse amene amatsatira Khristu nthawi zina amafunika kudzudzulidwa. Tikalandira uphunguwo modzichepetsa n’kuphunzira pa zimene tinalakwitsazo, ubwenzi wathu ndi Yesu Khristu ndiponso Atate wake, Yehova Mulungu, umalimba.—Miyambo 4:13.
Anadalitsidwa Chifukwa cha Kukhulupirika
Panthawi imeneyi, Yesu analankhulanso mawu ena odabwitsa. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira panowa amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga mfumu.” (Mateyo 16:28) N’zosakayikitsa kuti Petulo anali ndi chidwi chofuna kudziwa tanthauzo la mawu amenewa. Mwina Petulo anaganiza kuti iye sadzalandira nawo madalitsowa chifukwa chakuti anali atangodzudzulidwa kumene ndi Yesu.
Komabe, patapita mlungu umodzi, Yesu anatenga Yakobe, Yohane, ndi Petulo n’kukwera nawo “m’phiri lalitali.” Phirili mwina linali la Herimoni, lomwe linali pafupi ndi pamene iwo anali. Zikuoneka kuti unali usiku chifukwa atumwi atatuwo anali ndi tulo. Koma Yesu atayamba kupemphera, panachitika chinachake chimene chinachotsa tulo tonse timene atumwiwo anali nato.—Mateyo 17:1; Luka 9:28, 29, 32.
Yesu anayamba kusandulika iwo akuona. Khope yake inayamba kuwala mpaka inayamba kuoneka ngati dzuwa. Zovala zakenso zinayamba kunyezimira kwambiri. Kenako pafupi ndi Yesu panaoneka anthu awiri, mmodzi wooneka ngati Mose ndipo winayo ngati Eliya. Iwo ankakambirana naye za “kuchoka kwake kumene iye anayenera kudzakwaniritsa mu Yerusalemu.” Zimenezi zikutanthauza kuti ankakambirana za kufa ndi kuuka kwake. Choncho, zinali zoonekeratu kuti Petulo analakwitsa kudzudzula Yesu kuti sakuyenera kudzakumana ndi mavuto ngati amenewa.—Luka 9:30, 31.
Ataona masomphenya amenewa Petulo anafunitsitsa kuchitapo kanthu. Zinkaoneka ngati Mose ndi Eliya akutsanzikana ndi Yesu. Motero, Petulo anati: “Mlangizi, ndi bwino ife tizikhala pano, choncho timange mahema atatu, limodzi lanu, limodzi la Mose ndi lina la Eliya.” Komabe, Petulo sanafunike kumangira mahema anthu awiri oimira atumiki Mulungu amenewa omwe anali atafa kale. Pamene Petulo sankadziwa chimene akunena. Komabe, kodi simukuchita chidwi ndi changu chake komanso mtima wofuna kuthandiza ena?—Luka 9:33.
Petulo, Yakobe ndi Yohane adalitsidwanso usiku Luka 9:34-36.
umenewu chifukwa panabwera mtambo womwe unakuta phiri lonselo. Mumtambowo, munamveka mawu a Yehova Mulungu akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, amene ndinam’sankha. Mumvereni iye.” Kenako masomphenyawo anatha ndipo atumwiwo anatsala okhaokha ndi Yesu paphiripo.—Masomphenya amenewa anali dalitso kwambiri kwa Petulo komanso ndi dalitso kwa ifeyo. Patapita zaka zambiri Petulo analemba za mwayi wapadera umene anali nawo usiku umenewu wokhala mmodzi wa anthu amene ‘anaona ndi maso ulemerero’ wa Yesu. Anakhala ngati aona Yesu ali Mfumu kumwamba. Masomphenya amenewa anali umboni wakuti maulosi a m’Mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa ndipo analimbitsa chikhulupiriro cha Petulo komanso anamuthandiza kuti apirire mayesero amene anali kutsogolo kwake. (2 Petulo 1:16-19) Masomphenya amenewa angatithandizenso ngati titapitirizabe kukhala okhulupirika kwa Mbuye wathu, Yesu Khristu, yemwe Yehova wamuika. Angatithandizenso tikamaphunzira zinthu kwa iye, kutsatira uphungu wake, ndiponso kutsatira mapazi ake modzichepetsa tsiku ndi tsiku.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira,” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2009.
^ ndime 9 Umboni wakuti anthuwa anasintha maganizo awo umaoneka tikayerekezera zimene iwo ananena panthawiyi ndi zimene ananena dzulo lake pamene ananena mosangalala kuti iye ndi mneneri wa Mulungu.—Yohane 6:14.
^ ndime 15 Kuchokera kugombe la nyanja ya Galileya, gululi linayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 45. Pagombe pomwe ananyamukira, panali pokwera mamita 210. Koma atayenda ulendowu kudutsa m’dera lokongola kwambiri kupita chakumtunda, anafika pamalo okwera mamita 350.
^ ndime 18 Onani bokosi lakuti “Kodi Thanthwe Limene Yesu Anatchula Anali Ndani?” patsamba 28.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]
Kodi Thanthwe Limene Yesu Anatchula Anali Ndani?
Yesu anauza mtumwi Petulo kuti: “Ndikukuuza kuti, Iwe ndiwe Petulo, ndipo pathanthwe ili ndidzamangapo mpingo wanga.” (Mateyo 16:18) Anthu ambiri amaganiza kuti pamenepa Yesu ankatanthauza kuti Petulo ndiye maziko a mpingo wachikhristu. Tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa kuti Yesu ponena zimenezi ankatanthauza kuti Petulo ndi woposa atumwi ena ndipo amati iye anali papa woyamba. N’chifukwa chake mkati mwa tchalitchi cha Saint Peter ku Rome, mawu a Yesu amenewa analembedwa ndi zilembo zikuluzikulu za Chilatini, zoposa msinkhu wa munthu.
Kodi Yesu anatanthauza kuti Petulo ndiye thanthwe limene Yesu adzamangepo mpingo wake? Ayi. Taganizirani mfundo zitatu zotsimikizira kuti Yesu sankatanthauza kuti Petulo ndiye thanthwe. Mfundo yoyamba ndi yakuti, panthawi imene Yesu amalankhula mawu amenewa n’kuti atumwi enanso ali pomwepo ndipo iwo sanaganize zimenezi. Ngati Yesu ankatanthauza kuti Petulo ndiye wamkulu kuposa ena onsewo, n’chifukwa chiyani pambuyo pake iwo ankatsutsana nkhani yakuti wamkulu ndani? (Maliko 9:33-35; Luka 22:24-26) Mfundo yachiwiri ndi yakuti, mtumwi Paulo anadzalemba kuti thanthwe ndi Yesu Khristu osati Petulo. (1 Akorinto 3:11; 10:4) Mfundo yachitatu ndi yakuti, patapita zaka zambiri Petulo ananena zinthu zosonyeza kuti iye sankadziona kuti ndi thanthwe. M’malo mwake iye analemba kuti Yesu ndiye “mwala wa pangodya” umene Mulungu anausankha.—1 Petulo 2:4-8.
Komabe, ena amanena kuti popeza kuti dzina la Petulo limatanthauza kuti “Mwala,” ndiye kuti thanthwe limene Yesu ankanena ndi Petulo. Ngakhale zili choncho, tanthauzo la dzina la Petulo si lofanana ndi mawu akuti “thanthwe.” Dzina la Petulo kwenikweni limatanthauza “chidutswa cha mwala,” ndipo ndi dzina lonena za chinthu chachimuna, pamene mawu amene anamasuliridwa kuti “thanthwe” amanena za chinthu chachikazi. Ndiye kodi Yesu ankatanthauza chiyani? M’mawu ena, tingati iye ankauza Petulo kuti: “Iwe, amene ndimakutchula kuti Petulo, kapena kuti Mwala, wadziwa ‘thanthwe,’ limene ndi Khristu, yemwe adzakhala maziko a mpingo wachikhristu.” Petulo anali ndi mwayi waukulu kwambiri chifukwa anathandiza kuti Yesu anene mfundo ya choonadi yofunika kwambiri imeneyi.
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Petulo anakhalabe wokhulupirika ngakhale pamene anadzudzulidwa ndi Yesu
[Chithunzi patsamba 26]
Chifukwa cha kukhulupirika kwake, Petulo anaona masomphenya ofunika kwambiri