Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Bodza Lachinayi: Pali Milungu Itatu mwa Mulungu Mmodzi

Bodza Lachinayi: Pali Milungu Itatu mwa Mulungu Mmodzi

Kodi bodzali linayamba bwanji?

Buku linalake lachikatolika limati: “Titafufuza mokwanira tingathe kuona kuti chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi chinayambika chakumapeto kwa zaka za m’ma 300 C.E. Ndipo zimenezi n’zoona . . . chifukwa zaka za m’ma 300 C.E. zisanathe, Akhristu anali asanayambe kukhulupirira kuti pali ‘milungu itatu mwa Mulungu mmodzi.’”​—New Catholic Encyclopedia (1967), Voliyumu 14, tsamba 299.

Buku lina limanena kuti: “Pamsonkhano wa ku Nesiya, umene unachitika pa May 20, 325 [C.E.], Kositantini ndi amene ankatsogolera zokambiranazo. Iye anatchula . . . mfundo yaikulu yosonyeza kugwirizana kwa Khristu ndi Mulungu potsatira zimene anthu anagwirizana pamsonkhanowo, ‘zakuti Yesu ndi wofanana ndi Atate.’. . . Chifukwa choopa mfumuyo, mabishopu onse, kupatulapo awiri okha, anasainira mfundoyo ndipo ambiri anachita zimenezi ngakhale kuti zinali zosiyana ndi zimene ankakhulupirira.”​—Encyclopædia Britannica (1970), Voliyumu 6, tsamba 386.

Kodi Baibulo limati chiyani?

Limanena kuti: “[Sitefano], pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu. Ndipo ananena kuti: ‘Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka, ndipo Mwana wa munthu ali chiimirire kudzanja lamanja la Mulungu.’”​—Machitidwe 7:55, 56.

Kodi lembali likusonyeza chiyani? Sitefano atadzazidwa ndi mzimu woyera anaona Yesu “ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu.” Choncho Yesu ataukitsidwa kupita kumwamba, sanakakhale Mulungu, koma anali munthu wauzimu payekha. Ndipo m’masomphenya akewa, Sitefano sanaone munthu wachitatu ataima pafupi ndi Mulungu. Wansembe wina wachikatolika, dzina lake Marie-Émile Boismard, anayesetsa kufufuza malemba ogwirizana ndi chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, ndipo analemba kuti: “M’Chipangano Chatsopano . . . mulibe mawu osonyeza kuti pali anthu atatu mwa Mulungu mmodzi.”​—À l’aube du christianisme​—La naissance des dogmes (Ziphunzitso Zimene Zinayambika Chikhristu Chitangoyamba Kumene).

Kositantini ankalimbikitsa chiphunzitsochi pofuna kuthetsa kusiyana maganizo kumene kunalipo mumpingo m’zaka za m’ma 300 C.E. Komabe, chiphunzitsochi chinayambitsa funso lina lakuti: Kodi Mariya amene anabereka Yesu, anali “Amayi a Mulungu”?

Yerekezani ndi mavesi awa: Mateyo 26:39; Yohane 14:28; 1 Akorinto 15:27, 28; Akolose 1:15, 16

ZOONA N’ZAKUTI:

Chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi chinayamba chakumapeto kwa zaka za m’ma 300 C.E.