Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzitetezeni ku Mizimu Yoipa

Dzitetezeni ku Mizimu Yoipa

Dzitetezeni ku Mizimu Yoipa

JAMES anakulira m’dera linalake la kumidzi pachilumba cha Malaita, ku Solomon Islands. Kuyambira ali mwana, iye anaphunzitsidwa kuti azilemekeza mizimu. Iye anati: “Sindinkapempha mizimu kuti izivulaza anthu ena, koma ndinkaona kuti sindingakhale ndi moyo wosangalala popanda kudalira mizimuyo kuti izinditeteza.”

Monga mmene zilili ndi anthu a m’madera ambiri, anthu a ku Solomon Islands amakhulupirira kuti mizimu imathandiza ndiponso kuvulaza anthu. Komabe anthu ambiri a ku zilumbazi amaona kuti mizimu ndi yabwino osati yoopsa.

Anthu amakhulupirira mizimu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, panthawi imene James anali mwana, azimayi a m’mudzi mwawo ankati akangomva kulira kwa mbalame yotchedwa nkhwenzule, ankauza ana awo kuti athawire m’nyumba. Iwo ankachita zimenezi chifukwa ankakhulupirira kuti mbalameyi ikangolira, ndiye kuti munthu winawake akumana ndi zoopsa.

Anthu ena a ku zilumbazi ankaika mwala wansangalabwi pamwamba pa mafelemu a nyumba zawo. James nayenso ankachita nawo zimenezi chifukwa chokhulupirira kuti mwalawu ungamuteteze ku mizimu. Ndipo akakhala kuntchito, iye ankatolera nyenyeswa zonse za chakudya chamasana, n’kuziika m’kapepala kuti akazitaye nthawi ina. Iye ankachita zimenezi poopa kuti munthu wina wochita zamatsenga angatenge nyenyeswazo n’kukazichitira mankhwala kuti iye adwale.

N’kutheka kuti anthu am’dera lanu sachita zimene tafotokozazi, koma mofanana ndi James, inunso mumaona kuti muyenera kutsatira miyambo inayake kuti mudziteteze ku mizimu yoipa. Mwina mumakhulupirira kuti mukapanda kuchita nawo miyambo imeneyi, mizimuyo ikhoza kukuvulazani.

Ngati mumakhulupirira Baibulo, muyenera kuti mungakonde kudziwa mayankho a mafunso otsatirawa: (1) Kodi mizimu yoipa ndi yoopsa motani? (2) Kodi mungayambe kukhulupirira mizimu chifukwa chotsatira miyambo inayake yamakolo? (3) Kodi mungatani kuti mudziteteze ku mizimu yoipa n’kukhala osangalala?

Kuopsa kwa Mizimu Yoipa

Baibulo limasonyeza kuti anthu akufa sasanduka n’kukhala mizimu yoipa, chifukwa limati: “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Choncho, angelo omwe anagalukira Mulungu n’kugwirizana ndi Satana posocheretsa anthu ndi amene anakhala mizimu yoipa.​—Chivumbulutso 12:9.

Malemba amanena momveka bwino kuti anthufe tifunika kutetezedwa ku mizimu yoipa. Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Efeso kuti: “Sitikulimbana ndi anthu a thupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi . . . makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba.” Ndipo mtumwi Petulo anafotokoza kuti Satana Mdyerekezi yemwe ndi mkulu wa mizimu yoipa ali ngati “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.”​—Aefeso 6:12; 1 Petulo 5:8.

Satana amasocheretsa anthu powanamiza ndiponso powalimbikitsa kuchita zinthu zosasangalatsa Mulungu. Baibulo limati Satana “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” (2 Akorinto 11:14) Iye amadzionetsa ngati mngelo wabwino, pamene zolinga zake n’zoipa. Iye amachititsa khungu maganizo a anthu kuti asamuzindikire ndiponso kuti asadziwe choonadi chokhudza Mulungu. (2 Akorinto 4:4) Kodi cholinga chake posocheretsa anthu n’chotani?

Satana amafuna kuti azilambiridwa, ndipo amafuna kuti anthu azichita zimenezi kaya modziwa kapena ayi. Panthawi imene Yesu, Mwana wa Mulungu, anali padziko lapansi, Satana anamuuza kuti ‘agwade pansi ndi kumulambira.’ Koma Yesu anayankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira.’” (Mateyo 4:9, 10) Yesu anakana kuchita chilichonse chosonyeza kuti iye akulambira Satana.

Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa zolengedwa zonse zauzimu, motero sangalole kuti mizimu yoipa izivutitsa anthu amene amamumvera. (Salmo 83:18; Aroma 16:20) Komabe kuti tisangalatse Mulungu ngati mmene Yesu anachitira, tiyenera kupewa kulambira Satana ndi ziwanda zake. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kuzindikira miyambo yonse imene cholinga chake n’kulambira mizimu yoipa. Komano kodi tingachite bwanji zimenezi?

Zindikirani Miyambo Imene Sikondweretsa Mulungu

Yehova Mulungu anachenjeza Aisiraeli kuti asatengere miyambo ya anthu amitundu yoyandikana nawo. Iye anati: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga, kapena wotsirika.” Ponena za anthu ochita zimenezi, Baibulo limati: “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”​—Deuteronomo 18:10-12.

Choncho, mukamaganizira za miyambo yofala m’dera lanu, dzifunseni kuti: Kodi mwambowu umalimbikitsa zamizimu kapena kukhulupirira zamatsenga? Kodi mwambowu umalimbikitsa anthu kutsirika, kugwiritsa ntchito zithumwa kapena kulodzana? Kodi pamwambowu anthu amalemekeza mizimu m’malo molemekeza Yehova kapena Yesu, yemwe ndi womuimira wake?​—Aroma 14:11; Afilipi 2:9, 10.

M’pofunika kwambiri kuti mupewe mwambo uliwonse umene umalimbikitsa kulambira mizimu. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Sizingatheke kuti muzimwa chikho cha Yehova komanso chikho cha ziwanda.” Iye anachenjeza kuti anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu komanso mizimu ‘amaputa nsanje ya Yehova.’ (1 Akorinto 10:20-22) Yehova amafuna kuti tikhale odzipereka kwa iye ndi mtima wonse ndipo ndi iye yekha amene tiyenera kumulambira.​—Eksodo 20:4, 5.

Muyeneranso kudzifunsa kuti: Kodi mwambowu amalimbikitsa maganizo akuti munthu sakhala ndi mlandu ngakhale atachita zosayenera? Mwachitsanzo, m’madera ambiri anthu amaona kuti chigololo kapena kugonana anthu asanakwatirane sikoyenera. Ndiponso Baibulo limaletsa makhalidwe amenewa. (1 Akorinto 6:9, 10) Komabe, m’madera ena a kuzilumba za nyanja ya Pacific, anthu angaone kuti makhalidwe amenewa siolakwika ngati mtsikana atanena kuti “amupatsa tsamba laliwisi,” * kutanthauza kuti mizimu yamuuza kuti agonane ndi mwamuna.

Koma Baibulo limanena kuti aliyense amakhala ndi mlandu chifukwa cha zochita zake. (Aroma 14:12; Agalatiya 6:7) Mwachitsanzo, Hava ananena kuti Satana ndi amene anamuchititsa kuti asamvere Mulungu. Iye anati: “Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.” Komabe Yehova anaimba mlandu Hava chifukwa cha zimene anachitazo. (Genesis 3:13, 16, 19) Ifenso tikamachita zoipa, Yehova adzatiimba mlandu.​—Aheberi 4:13.

Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?

Ngati mukufuna kusangalatsa Mulungu komanso kuchita zinthu zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, muyenera kupeweratu zinthu zogwirizana ndi Satana ndiponso mizimu yoipa. M’nthawi ya atumwi, anthu oona mtima omwe ankakhala ku Efeso anasonyeza chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Pofuna kudziteteza ku mizimu yoipa, iwo anasonkhanitsa mabuku awo onse a zamatsenga ndi “kuwatentha pamaso pa onse.”​—Machitidwe 19:19.

Komabe anthuwa asanaotche mabukuwo “anali kubwera kudzaulula ndi kufotokoza poyera zochita zawo.” (Machitidwe 19:18) Anthuwa atakhudzidwa mtima ndi uthenga wa Paulo wonena za Khristu, anawotcha mabuku awo a zamatsenga komanso anasiya kuchita nawo miyambo yolambira mizimu yoipa.

Zingakhale zovuta kusiya kukhulupirira mizimu ndipo zimenezi ndi zimene zinachitikira James yemwe tam’tchula kale uja. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo ankasangalala ndi zomwe ankaphunzirazo. Komabe James sanasiyiretu zamizimu. Ngakhale kuti iye ankakhulupirira malonjezo a Yehova, ankaona kuti akufunikabe kukhulupirira zamizimu kuti akhale wotetezeka.

Kodi n’chiyani chimene chinam’thandiza kuti asinthe? Iye anati: “Ndinapemphera kwa Yehova kuti azinditeteza komanso kuti andithandize kuti ndizim’khulupirira. Ndipo panthawiyi ndinasiyiratu kuchita zamizimu.” Kodi James atasiya zimenezi anakumana ndi mavuto alionse? Ayi, chifukwa iye anena kuti: “Zimenezi zandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova ndiponso kuti ndikhale naye paubwenzi wolimba.” Ndipotu pazaka 7 zapitazi, James wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse pofuna kuthandiza anthu kuti adziwe zimene Baibulo limaphunzitsa.

Inunso mungachite bwino kutengera chitsanzo cha James. Unikani bwinobwino miyambo imene anthu a m’dera lanu amachita ndipo gwiritsani ntchito “luntha la kulingalira” kuti mudziwe ngati ili yogwirizana ndi “chifuniro cha Mulungu.” (Aroma 12:1, 2) Kenako tsimikizani mtima kupewa miyambo yogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Mukamachita zimenezi n’zosakayikitsa kuti Yehova ‘adzakulandirani.’ (2 Akorinto 6:16-18) Monga mmene anachitira James, inunso mungagwirizane ndi mawu a m’Baibulo akuti: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.”​—Miyambo 18:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Mawu amenewa amanena za mwambo winawake umene anthu amagwiritsa ntchito tsamba linalake kapena chakudya pochitira munthu wina zamatsenga. Iwo amatenga chakudya kapena tsambalo n’kupatsa mtsikana kuti iye azikopa amuna. Komabe zimenezi n’zosiyana ndi zimene zingachitike ngati mtsikana wachita kupatsidwa mankhwala ogonetsa tulo iye asakudziwa, kenako n’kumugwiririra. Zikatero, ndiye kuti mtsikanayo amakhala wosalakwa.

[Chithunzi patsamba 19]

Nkhwenzule

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of Dr. Bakshi Jehangir

[Chithunzi patsamba 19]

Mtsikana akutola nyenyeswa za chakudya kuti anthu ena asazitole ndi kukazichitira mankhwala