Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Yekha ndi Amene Angapulumutse Dzikoli

Mulungu Yekha ndi Amene Angapulumutse Dzikoli

Mulungu Yekha ndi Amene Angapulumutse Dzikoli

“MWALA WOKONGOLA WAMTENGO WAPATALI KWAMBIRI, WOKHALA NDI MWINA MWA BULUU NDI MWINA MOYERA.” Umu ndi mmene Edgar Mitchell anaonera dzikoli ali m’mlengalenga.

Mulungu anagwira ntchito yaikulu pokonza dzikoli kuti anthu akhalemo. Zimene Mulungu analenga zinapangitsa angelo kufuula “ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Ifenso tingakhale achimwemwe tikadziwa zinthu zodabwitsa za m’dziko lathuli. M’dzikoli muli zinthu zambiri zosamvetsetseka zimene zimathandiza kuti zinthu zithe kukhala ndi moyo. Chimodzi mwa izo ndi mmene zomera zimapangira chakudya chawo pogwiritsa ntchito dzuwa, mpweya woipa ndiponso madzi. Zimenezi zikamachitika, zomerazi zimatulutsa mpweya wabwino umene umatithandiza kuti tikhale ndi moyo.

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anapatsa anthu udindo wosamalira dzikoli. (Genesis 1:28; 2:15) Komabe, kuti zinthu m’dzikoli zikhalebe mmene zinalili poyamba, anthu anafunika kukhala ndi maganizo abwino. Iwo anafunika kukonda dziko lawo ndiponso kukhala ndi mtima wofuna kukonza dzikoli kuti likhalebe lokongola. Komabe, popeza kuti anthu analengedwa ndi ufulu wosankha zochita, iwo akanatha kuwononga dzikoli. Ndipo zimenezi n’zimene akuchita. Padzikoli pali mavuto ambiri chifukwa cha kusasamala ndiponso dyera la anthu.

Mavuto ena amene tingawatchule ndi awa: (1) Dzikoli likulephera kugwiritsa ntchito bwino mpweya woipa chifukwa chodula mitengo mosasamala ndipo zimenezi zikuchititsa kuti kunja kuzizizira kapena kuzitentha kwambiri. (2) Kugwiritsa ntchito kwambiri mankhwala ophera tizilombo kwawononga tizilombo tina timene timathandiza m’chilengedwechi pa zinthu monga kunyamula mungu kuti zomera zina zibereke. (3) Kupha nsomba mosakaza ndiponso kuipitsa madzi m’nyanja ndi m’mitsinje kwachepetsa kwambiri nsomba. (4) Kugwiritsa ntchito mowononga zinthu zachilengedwe kukuchititsa kuti zinthu zambiri zimene zikanagwira ntchito m’tsogolo zithe ndipo akuti n’zimene zikupangitsa kuti dzikoli lizitentha kwambiri. Akatswiri ena akuti kuchepa kwa madzi oundana m’nyanja ya Arctic ndi Antarctic ndi umboni wakuti dzikoli likutentha kwambiri.

Popeza masoka achilengedwe akuwonjezeka, anthu ena amanena kuti dzikoli likubwezera, n’chifukwa chake pali mavuto aakulu. Mulungu anatipatsa dzikoli kuti tizikhalamo kwaulere. (Genesis 1:26-29) Komabe, mmene zinthu zilili m’dzikoli masiku ano zikusonyeza kuti anthu ambiri alibe mtima wofuna kukonza dzikoli kuti likhalebe lokongola. Anthu angotanganidwa ndi zochita zawo zadyera. Tingati anthu amenewa si abwino kukhala m’dzikoli, popeza ‘awononga dziko lapansi,’ monga linaloserera Baibulo pa Chivumbulutso 11:18.

Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, amene analenga zamoyo zonse za m’dzikoli, wanena kuti ikudza nthawi imene ‘adzachotse’ anthu oipa m’dzikoli. (Zefaniya 1:14; Chivumbulutso 19:11-15) Anthu asanawonongeretu dzikoli, Mulungu awachotsa ndipo achita zimenezi mwamsanga kwambiri kuposa mmene tikuganizira. * (Mateyo 24:44) Ndithudi, ndi Mulungu yekha amene angapulumutse dzikoli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mumve zambiri, onani kabuku kakuti Dikirani! kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.