NKHANI YOPHUNZIRA 9
NYIMBO NA. 51 Tadzipereka kwa Mulungu
Musachedwe Kubatizidwa
“Ukuchedweranji? Nyamuka ubatizidwe.”—MAC. 22:16.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona mmene zitsanzo za anthu monga Asamariya, Saulo wa ku Tariso, Koneliyo ndi Akorinto, zingakulimbikitsireni kuti muchite khama n’kubatizidwa.
1. Kodi ndi zifukwa zina ziti zomwe ziyenera kukuchititsani kubatizidwa?
KODI mumakonda Yehova Mulungu yemwe amakupatsani mphatso iliyonse yabwino, kuphatikizapo moyo? Kodi mumafuna kumusonyeza kuti mumamukonda? Njira yabwino imene mungachitire zimenezo ndi kudzipereka kwa iye n’kusonyeza kwa ena kuti munadzipereka pobatizidwa m’madzi. Mukachita zimenezo mumasonyeza kuti mwalowa m’banja la Yehova. Zotsatira zake n’zakuti Yehova yemwe ndi Atate wanu komanso mnzanu, adzakutsogolerani komanso kukusamalirani chifukwa ndinu wake. (Sal. 73:24; Yes. 43:1, 2) Kudzipereka komanso kubatizidwa kumakupatsaninso mwayi wokhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.—1 Pet. 3:21.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Kodi pali chinachake chomwe chikukulepheretsani kubatizidwa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Pali anthu enanso ambiri omwe ankafunika kusintha khalidwe ndi kaganizidwe kawo kuti ayenerere kubatizidwa. Panopa amatumikira Yehova mwakhama komanso mosangalala. Kodi mungaphunzire chiyani kwa anthu ena omwe anabatizidwa m’nthawi ya atumwi? Tiyeni tikambirane mavuto amene anakumana nawo komanso zimene tingaphunzire pa chitsanzo chawo.
ASAMARIYA ANABATIZIDWA
3. Kodi Asamariya ena ankafunika kusintha zinthu ziti kuti abatizidwe?
3 Asamariya a m’nthawi ya Yesu anali kagulu kachipembedzo komwe kankapezeka ku Sekemu ndi ku Samariya, mizinda yomwe inali kumpoto kwa Yudeya. Asanabatizidwe, iwo ankafunika kuphunzira zambiri zokhudza Mawu a Mulungu. Iwo ankangokhulupirira mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo, oyambira pa Genesis mpaka Deuteronomo komanso mwina buku la Yoswa. Komabe Asamariya ankayembekezera kubwera kwa Mesiya mogwirizana ndi lonjezo la Mulungu lopezeka pa Deuteronomo 18:18, 19. (Yoh. 4:25) Kuti abatizidwe ankafunika kuvomereza kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa. “Asamariya ambiri” anachitadi zimenezo. (Yoh. 4:39) Asamariya ena ankafunika kulimbana ndi tsankho lomwe linali pakati pa mtundu wawo ndi Ayuda.—Luka 9:52-54.
4. Mogwirizana ndi Machitidwe 8:5, 6, 14, kodi Asamariya ena anatani Filipo atawalalikira?
4 Kodi n’chiyani chinathandiza Asamariya kuti abatizidwe? Filipo yemwe anali mlaliki atawalalikira “za Khristu,” Asamariya ena ‘analandira mawu a Mulungu.’ (Werengani Machitidwe 8:5, 6, 14.) Iwo sanakane kumvetsera uthenga wake ngakhale kuti iye anali Myuda. Mwina ankakumbukira mavesi ena a mu Pentatuke omwe amasonyeza kuti Mulungu alibe tsankho. (Deut. 10:17-19) Iwo “ankamvetsera zimene Filipo ankanena” zokhudza Khristu ndipo ankaona umboni wosonyeza kuti iye anatumidwa ndi Mulungu. Filipo ankachitanso zizindikiro zambiri monga kuchiritsa odwala komanso kutulutsa ziwanda.—Mac. 8:7.
5. Kodi tikuphunzira chiyani kwa a Samariya?
5 Asamariya akanatha kukana kumvetsera chifukwa cha tsankho kapenanso chifukwa chakuti zimene Filipo ankawauza zinali zachilendo. Koma sanalole kuti zimenezi zichitike. Iwo atatsimikiza kuti zimene Filipo ankaphunzitsa ndi choonadi, sanazengereze kubatizidwa. Baibulo limafotokoza kuti: “Koma iwo atakhulupirira Filipo, amene ankalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso wonena za dzina la Yesu Khristu, ankabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.” (Mac. 8:12) Kodi inunso mumatsimikizira kuti Mawu a Mulungu ndi choonadi, komanso kuti a Mboni za Yehova alibe tsankho ndipo amasonyezana chikondi chenicheni chomwe ndi chizindikiro cha Akhristu oona? (Yoh. 13:35) Ngati ndi choncho, chitanipo kanthu mwamsanga kuti mubatizidwe ndipo musamakayikire kuti Yehova adzakudalitsani.
6. Kodi chitsanzo cha Ruben chingakuthandizeni bwanji?
6 Ruben, wa ku Germany, anabadwira m’banja la Mboni. Komabe ali wamng’ono iye ankakayikira ngati kuli Mulungu. Ndiye kodi anatani kuti athetse kukayikirako? Iye atazindikira kuti sankadziwa zambiri pa nkhaniyi, anakonza zoti achitepo kanthu. Iye anati: “Pophunzira pandekha, ndinkafunika kufufuza kuti ndidziwe zoona. Ndinaphunzira mobwerezabwereza nkhani yonena kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.” Iye anawerenga buku la Chingelezi lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Buku limeneli linamuthandiza kwambiri Ruben. Iye anadziuza kuti, ‘Yehova alipodi ndipo ndi weniweni.’ Ndipo atapita kukaona likulu lathu, Ruben anayamba kuyamikira kwambiri ubale wathu wapadziko lonse. Atabwerera ku Germany, iye anabatizidwa ali ndi zaka 17. Ngati mukukayikira zinazake zimene mwaphunzira, muzifufuza m’mabuku athu. ‘Kudziwa zinthu molondola’ kungakuthandizeni kuti musamakayikire. (Aef. 4:13, 14) Komanso mukamamva malipoti okhudza chikondi ndi mgwirizano, zomwe zilipo pakati pa anthu a Yehova m’mayiko osiyanasiyana, ndiponso kuona umboni wa zimenezi mumpingo wanu, mudzayamba kukonda kwambiri abale anu padziko lonse.
SAULO WA KU TARISO ANABATIZIDWA
7. Kodi Saulo ankafunika kusintha maganizo olakwika ati omwe anali nawo?
7 Taganizirani chitsanzo cha Saulo wa ku Tariso. Iye anaphunzira kwambiri malamulo a Chiyuda ndipo anali wotchuka. (Agal. 1:13, 14; Afil. 3:5) Pa nthawiyo Ayuda ambiri ankakhulupirira kuti Akhristu ndi ampatuko, choncho Saulo ankazunza kwambiri Akhristu. Pochita zimenezi, iye ankaganiza kuti akuchita chifuniro cha Mulungu. (Mac. 8:3; 9:1, 2; 26:9-11) Choncho kuti akhulupirire Yesu n’kubatizidwa kukhala Mkhristu, Saulo ankafunika kukonzekera kuti nayenso adzazunzidwa.
8. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Saulo kuti abatizidwe? (b) Mogwirizana ndi Machitidwe 22:12-16, kodi Hananiya anathandiza bwanji Saulo? (Onaninso chithunzi.)
8 Kodi n’chiyani chinathandiza Saulo kuti abatizidwe? Yesu atalankhula ndi Saulo kuchokera kumwamba, Saulo anasiya kuona. (Mac. 9:3-9) Kwa masiku atatu iye sankadya ndipo ayenera kuti ankaganizira zimene zinamuchitikirazo. Apa Saulo anali atatsimikiza kuti Yesu ndi Mesiya ndipo kuti otsatira ake ndi amene anali m’chipembedzo choona. Saulo ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri chifukwa chovomereza kuti Sitefano aphedwe. (Mac. 22:20) Pambuyo pa masiku atatu, wophunzira wina dzina lake Hananiya anabwera kwa Saulo n’kumuthandiza kuti ayambirenso kuwona ndiponso anamulimbikitsa kuti abatizidwe mwamsanga. (Werengani Machitidwe 22:12-16.) Modzichepetsa Saulo anamvera zimene Hananiya anamuuza ndipo anabatizidwa.—Mac. 9:17, 18.
9. Kodi mungaphunzire chiyani kwa Saulo?
9 Tingaphunzire zambiri kuchokera kwa Saulo. Iye akanatha kulola kuti kunyada kapena kuopa anthu kumulepheretse kubatizidwa. Koma iye sanalole kuti zimenezi zichitike. Modzichepetsa, Saulo anasintha moyo wake n’kukhala Mkhristu. (Mac. 26:14, 19) Iye ankafunitsitsa kukhala Mkhristu ngakhale kuti ankadziwa kuti adzazunzidwa. (Mac. 9:15, 16; 20:22, 23) Atabatizidwa, iye anapitiriza kudalira Yehova kuti azimuthandiza kupirira mayesero osiyanasiyana. (2 Akor. 4:7-10) Inunso mukabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova, muzikumana ndi mayesero omwe angayese chikhulupiriro chanu. Koma Yehova ndi Khristu adzakuthandizani kuti mupitirizebe kukhala okhulupirika.—Afil. 4:13.
10. Kodi chitsanzo cha Anna chingakuthandizeni bwanji?
10 Anna anakulira m’banja la Chikadishi ku Eastern Europe. Mayi ake atabatizidwa, Anna anapempha bambo ake kuti nayenso aziphunzira Baibulo ndipo anayamba kuphunzira ali ndi zaka 9. Anna ankakhala ndi achibale ake ndipo iwo atamva kuti iye wayamba kuphunzira Baibulo anayamba kumutsutsa. Iwo ankaona kuti n’zochititsa manyazi munthu kusiya chipembedzo cha makolo ake. Anna atakwanitsa zaka 12 anapempha chilolezo kwa bambo ake kuti abatizidwe. Iwo anamufunsa ngati anasankha yekha kuchita zimenezo kapena ngati munthu wina anachita kumukakamiza. Iye anayankha kuti, “Ndasankha ndekha chifukwa ndimakonda Yehova.” Bambo akewo anamulola kuti akabatizidwe. Atabatizidwa, achibale ake a Anna anapitiriza kumunyoza komanso kumuchitira zinthu zina zankhanza. Mmodzi wa achibale akewo anamuuza kuti: “Zikanakhala bwino ukanamachita makhalidwe ena oipa kapena kusuta kusiyana ndi kukhala wa Mboni za Yehova.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza Anna kuti apirire? Iye anati, “Yehova ankandipatsa mphamvu, ndipo mayi anga ndi bambo ankandithandiza kwambiri.” Nthawi zonse Yehova akamuthandiza pa moyo wake, Anna amalemba mmene iye wamuthandizira. Nthawi ndi nthawi amabwerera pa zimene analembazo kuti asamaiwale mmene Yehova anamuthandizira. Inunso ngati mukuopa kutsutsidwa, muzikumbukira kuti Yehova adzakuthandizani.—Aheb. 13:6.
KONELIYO ANABATIZIDWA
11. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikanalepheretsa Koneliyo kubatizidwa?
11 Tingaphunzirenso mfundo zofunika pa chitsanzo cha Koneliyo. Iye anali mtsogoleri wa gulu la asilikali a Chiroma okwana 100. (Mac. 10:1, mawu a m’munsi.) Choncho iye ayenera kuti anali wotchuka m’dera lawo komanso pakati pa asilikali. Komanso “ankapatsa anthu mphatso zachifundo zambiri.” (Mac. 10:2) Yehova anatumiza mtumwi Petulo kuti akamulalikire uthenga wabwino. Kodi udindo umene Koneliyo anali nawo unamulepheretsa kubatizidwa?
12. Kodi n’chiyani chinathandiza Koneliyo kuti abatizidwe?
12 Kodi n’chiyani chinathandiza Koneliyo kuti abatizidwe? Timawerenga kuti iye “ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse.” Komanso Koneliyo ankapemphera mochonderera Mulungu nthawi zonse. (Mac. 10:2) Petulo atalalikira uthenga wabwino kwa Koneliyo, iye ndi banja lake anakhulupirira Khristu ndipo nthawi yomweyo anabatizidwa. (Mac. 10:47, 48) Koneliyo sanazengereze kusintha zilizonse zomwe ankafunikira n’cholinga choti azilambira Yehova limodzi ndi banja lake.—Yos. 24:15; Mac. 10:24, 33.
13. Kodi mungaphunzire chiyani kwa Koneliyo?
13 Mofanana ndi Saulo, udindo wa Koneliyo ukanatha kumulepheretsa kuti akhale Mkhristu. Koma iye sanalole kuti zimenezi zichitike. Kodi inunso mukufunika kusintha zinthu zina pa moyo wanu kuti mubatizidwe? Ngati ndi choncho, dziwani kuti Yehova adzakuthandizani. Iye adzadalitsa zimene mukuyesetsa kuchita kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wanu.
14. Kodi chitsanzo cha Tsuyoshi chingakuthandizeni bwanji?
14 Tsuyoshi, wa ku Japan, ankafunika kusintha ntchito yomwe ankagwira n’cholinga choti abatizidwe. Iye anali wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu pasukulu yotchedwa Ikenobo yomwe inkaphunzitsa anthu kukonza maluwa. Mphunzitsi wamkuluyo akalephera kukapezeka pamaliro enaake, Tsuyoshi ndi amene ankakamuimira pochita miyambo ya Chibuda. Koma Tsuyoshi ataphunzira choonadi chokhudza imfa, anadziwa kuti sangabatizidwe ngati atapitiriza kuchita miyambo imeneyi. Iye anasankha kuti asamachitenso miyambo ya Chibudayi. (2 Akor. 6:15, 16) Tsuyoshi anakambirana nkhaniyi ndi mphunzitsi wamkulu uja. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Mphunzitsi wamkuluyo anavomera kuti Tsuyoshi akhoza kupitiriza kumagwira ntchito yake popanda kuchita nawo miyamboyo. Tsuyoshi anabatizidwa patangotha pafupifupi chaka chimodzi kuchokera pamene anayamba kuphunzira Baibulo. a Ngati inunso mukufunika kusintha zinthu zina pa nkhani ya ntchito imene mumagwira kuti muzisangalatsa Mulungu, dziwani kuti Yehova adzakupatsani inuyo ndi banja lanu zimene mukufunikira.—Sal. 127:2; Mat. 6:33.
AKORINTO ANABATIZIDWA
15. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikanalepheretsa anthu a ku Korinto kubatizidwa?
15 Anthu a mumzinda wa Korinto ankadziwika kuti anali okonda chuma komanso a makhalidwe oipa. Anthu ambiri akumeneko ankachita zinthu zomwe Mulungu sankasangalala nazo. N’zoonekeratu kuti zimenezi zikanachititsa kuti zikhale zovuta kwa anthu amene asankha kuti ayambe kutumikira Yehova. Komabe mtumwi Paulo atabwera mumzindawu n’kulalikira uthenga wabwino wonena za Khristu, “anthu ambiri a ku Korinto, amene anamva uthenga wabwino, anayamba kukhulupirira n’kubatizidwa.” (Mac. 18:7-11) Kenako Ambuye Yesu Khristu anaonekera kwa Paulo m’masomphenya n’kumuuza kuti: “Ndili ndi anthu ambiri mumzindawu.” Choncho Paulo anapitiriza kulalikira mumzindawu kwa chaka ndi hafu.
16. Kodi n’chiyani chomwe chinathandiza anthu ena a ku Korinto kulimbana ndi zinthu zomwe zikanawalepheretsa kubatizidwa? (2 Akorinto 10:4, 5)
16 Kodi n’chiyani chinathandiza anthu a ku Korinto kuti abatizidwe? (Werengani 2 Akorinto 10:4, 5.) Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera womwe ndi wamphamvu, zinawathandiza kuti asinthe kwambiri zinthu pa moyo wawo. (Aheb. 4:12) Anasiya makhalidwe oipa monga kuledzera, kuba komanso kugonana kwa pakati pa amuna ndiponso akazi okhaokha.—1 Akor. 6:9-11. b
17. Kodi mungaphunzire chiyani kwa anthu a ku Korinto?
17 Onani kuti ngakhale kuti anthu ena a ku Korinto analowerera kwambiri m’makhalidwe oipa, iwo sanaone kuti n’zovuta kuti asinthe n’kukhala Akhristu. Iwo anayesetsa kuchita khama kuti apitirizebe kuyenda panjira yopanikiza yomwe ndi yopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:13, 14) Kodi inunso mukulimbana ndi khalidwe linalake loipa lomwe lingakulepheretseni kubatizidwa? Dziwani kuti simuyenera kugonja. Muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera kuti ukuthandizeni kuti musamalakelake zinthu zoipa.
18. Kodi chitsanzo cha Monika chingakuthandizeni bwanji?
18 Monika, wa ku Georgia, anachita khama kuti asiye kulankhula mawu oipa komanso kumvetsera ndi kuonera zosangalatsa zosayenera n’cholinga choti abatizidwe. Iye anati: “Ndisanabatizidwe ndinapeza mphamvu zomwe ndinkafunikira kuti ndisinthe popemphera kwa Yehova. Yehova ankadziwa kuti ndimafuna kuchita zinthu zoyenera, choncho nthawi zonse ankandithandiza komanso kunditsogolera.” Monika anabatizidwa ali ndi zaka 16. Kodi pali makhalidwe ena oipa amene inunso muyenera kuwasiya kuti muzitumikira Yehova movomerezeka? Pitirizani kumupempha kuti akupatseni mphamvu zoti musinthe. Yehova amapereka mowolowa manja mzimu wake woyera.—Yoh. 3:34
CHIKHULUPIRIRO CHANU CHINGASUNTHE MAPIRI
19. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto okhala ngati mapiri? (Onaninso chithunzi.)
19 Musamakayikire kuti Yehova amakukondani ndipo amafuna kuti mukhale m’banja lake. Izitu zili choncho ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto omwe angakulepheretseni kubatizidwa. Pa nthawi ina Yesu anauza kagulu ka ophunzira ake kuti: “Ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhale chosatheka kwa inu.” (Mat. 17:20) Anthu amene anamva zimenezi anali atakhala ndi Yesu kwa zaka zochepa chabe, choncho chikhulupiriro chawo chinali chikukulabe. Koma Yesu anawatsimikizira kuti ngati atakhala ndi chikhulupiriro chokwanira, Yehova adzawathandiza kulimbana ndi mavuto okhala ngati mapiri. Ndipotu Yehova angakuthandizeni inunso kuchita zimenezi.
20. Kodi zitsanzo za Akhristu akale komanso amasiku ano zomwe zatchulidwa munkhaniyi zakulimbikitsani bwanji?
20 Ngati mwazindikira kuti pali mavuto ena omwe akukulepheretsani kubatizidwa, yesetsani kuti muwathetse mofulumira. Zitsanzo za Akhristu akale komanso amasiku ano zingakupatseni mphamvu. Zitsanzo zawo zikulimbikitseni komanso kukuthandizani kuti mudzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa. Mukachita zimenezi mudzakhala kuti mwasankha bwino kwambiri.
NYIMBO NA. 38 Adzakulimbitsa
a Mbiri ya moyo ya M’bale Tsuyoshi Fujii, imapezeka mu Galamukani! ya August 8, 2005, tsamba 28-31.
b Onani pa jw.org vidiyo yakuti ‘N’chifukwa Chiyani Mukuzengereza Kubatizidwa?’
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abale ndi alongo akulandira mosangalala anthu omwe angobatizidwa kumene.