Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

He Loved People

He Loved People

“Zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.”—MIY. 8:31.

1, 2. Kodi Yesu ankachita zotani posonyeza kuti amakonda kwambiri anthu?

YEHOVA anasonyeza nzeru zake zakuya pamene analenga mwana wake woyamba. Pofotokoza za mwanayo, Baibulo limamutchula kuti nzeru ndipo iye anali “mmisiri waluso” pamene ankagwira ntchito yolenga ndi Atate wake. Ayenera kuti anasangalala pamene Atate wake ankalenga kumwamba ndiponso ‘kukhazikitsa maziko a dziko lapansi.’ Koma ‘zinthu zimene zinali kumusangalatsa kwambiri zinali zokhudza ana a anthu.’ (Miy. 8:22-31) Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anayamba kukonda anthu kuyambira kale kwambiri ali kumwamba.

2 Yesu anasonyeza kuti amakonda kwambiri Atate wake ndiponso anthu. Iye “anasiya zonse zimene anali nazo” ndipo anakhala wofanana ndi anthu n’cholinga choti apereke “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Afil. 2:5-8; Mat. 20:28) Yesu ali padzikoli, Mulungu anamupatsa mphamvu kuti azichita zozizwitsa zomwe zinkasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu. Zimene ankachitazi zinkasonyeza zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolomu padziko lonse.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

3 Yesu atabwera padzikoli anagwiranso ntchito ‘yolengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 4:43) Iye ankadziwa kuti Ufumuwu udzathandiza kuyeretsa dzina la Atate wake ndiponso kuthetsa mavuto onse a anthu. Polalikira, ankachita zodabwitsa zambiri zosonyeza kuti amakonda anthu. Zimene Yesu ankachita zimatithandiza kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Tiyeni tikambirane zozizwitsa 4 za Yesu.

ANALI NDI MPHAMVU YOCHIRITSA

4. Fotokozani zimene zinachitika Yesu atakumana ndi munthu wodwala khate.

4 Pa nthawi ina, Yesu anapita kukalalikira ku Galileya. Zimene anaona mumzinda wina wa kumeneku zinali zomvetsa chisoni kwambiri. (Maliko 1:39, 40) Anakumana ndi munthu amene ankadwala khate. Luka anasonyeza kuti matendawo anali atafika poipa chifukwa analemba kuti munthuyo anali “wakhate thupi lonse.” (Luka 5:12) Wodwalayo ataona Yesu, “anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kum’pempha, kuti: ‘Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.’” Munthuyo ankadziwa kuti Yesu ali ndi mphamvu yomuchiritsa koma ankafuna kudziwa ngati akufunitsitsa kuchita zimenezi. Kodi Yesu anamuyankha bwanji? Kodi anamva bwanji mumtima ataona wodwalayo? Kodi anali ndi mtima ngati wa Afarisi omwe sankamvera chisoni anthu odwala matenda oopsawo? Nanga mukanakhala inuyo mukanatani?

5. Pochiritsa munthu wakhate, n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti “Ndikufuna”?

5 Zikuoneka kuti munthuyo sanatsatire Chilamulo cha Mose chimene chinkanena kuti azifuula kuti: “Wodetsedwa, wodetsedwa!” Yesu sanamudzudzule pa nkhani imeneyi. M’malomwake, ankadera nkhawa munthuyo ndipo ankafuna kumuthandiza. (Lev. 13:43-46) Sitikudziwa kuti Yesu ankaganiza zotani pa nthawiyo koma tikudziwa mmene ankamvera mumtima mwake. Iye anamumvera chisoni kwambiri moti anamuchiritsa m’njira yodabwitsa. Anatambasula dzanja lake n’kumukhudza kenako anamulankhula motsimikiza, koma mokoma mtima kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo khate la munthuyo linatha. (Luka 5:13) Mphamvu zimene Mulungu anapatsa Yesu zinamuthandiza kuchita zimenezi ndiponso kusonyeza kuti amakonda kwambiri anthu.—Luka 5:17.

6. (a) N’chiyani chikukuchititsani chidwi mukaganizira mmene Yesu ankachiritsira anthu? (b) Kodi zodabwitsa zimene anachitazi zikusonyeza chiyani?

6 Yesu anatha kuchita zodabwitsa zambirimbiri chifukwa cha mphamvu yochokera kwa Mulungu. Sikuti anachiritsa akhate okha. Anachiritsa anthu odwala matenda alionse komanso olumala. Baibulo limanena kuti: ‘Khamu la anthu linadabwa kuona osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso akhungu akuona, ndipo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.’ (Mat. 15:31) Yesu ankachiritsa anthu onsewa popanda kupempha anthu abwinobwino kuti apereke ziwalo kwa odwalawo. Anthuwo ankachira nthawi yomweyo ndipo ena ankawachiritsa ali kutali. (Yoh. 4:46-54) Kodi zodabwitsa zimene Yesu anachitazi zikusonyeza chiyani? Zikusonyeza kuti Yesu, yemwe akulamulira kumwamba, ali ndi mphamvu zochiritsa komanso mtima wofuna kuchita zimenezi. Tikaganizira zimene Yesu ankachitira anthu sitikayikira kuti m’dziko latsopano ulosi wa m’Baibulo udzakwaniritsidwa. Paja Baibulo limati: “[Yesu] adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka.” (Sal. 72:13) Yesu adzachiritsadi anthu onse ovutika chifukwa chakuti ali ndi mtima wofuna kuwathandiza.

“NYAMUKA, NYAMULA MACHIRA AKOWA NDI KUYAMBA KUYENDA”

7, 8. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu akumane ndi munthu wolumala?

7 Patapita miyezi ingapo kuchokera pamene anachiritsa munthu wakhateyo, Yesu anapita kukalalikira ku Yudeya. Iye ayenera kuti anathandiza anthu masauzande ambiri chifukwa chakuti anawalalikira ndiponso kuwasonyeza chikondi. Yesu ankafunitsitsa kulengeza uthenga wabwino kwa osauka, kulalikira za kumasulidwa kwa akapolo ndiponso kumanga zilonda za anthu osweka mtima.—Yes. 61:1, 2; Luka 4:18-21.

8 Pa mwezi wa Nisani, Yesu anapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa Pasika. Anthu ambirimbiri ankakhala ku Yerusalemu pa nthawi imeneyi. Ndiyeno Yesu anafika kudziwe lotchedwa Betesida, lomwe linali chakumpoto kwa kachisi. Kumeneko, anakumana ndi munthu wolumala.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani anthu ankapita kudziwe la Betesida? (b) Kodi Yesu anakatani kudziweli? (c) Kodi nkhaniyi ikusonyeza chiyani? (Onani chithunzi patsamba 8.)

9 Anthu ambirimbiri odwala ndiponso olumala ankapita ku Betesida. Iwo ankachita zimenezi chifukwa chokhulupirira kuti akalowa m’dziweli madzi akuwinduka angachiritsidwe. Anthu pamalowa ayenera kuti anali ankhawa komanso ankasowa mtengo woti agwire. Popeza Yesu anali wangwiro, n’chifukwa chiyani anapita kumeneko? Anapita chifukwa chomvera chisoni anthuwo. Iye anayandikira munthu wolumala uja yemwe anali atadwala zaka zambiri kuposa zaka zimene Yesu anakhala padziko lapansi.—Werengani Yohane 5:5-9.

10 Yesu anafunsa munthuyo ngati akufuna kuchira. Munthuyo anayankha kuti ankafuna kuchira koma analibe munthu womuthandiza kulowa m’dziwelo. Iye ayenera kuti ankamvetsa chisoni pamene ankanena zimenezi. Kenako Yesu anamuuza kuti achite zinthu zooneka ngati zosatheka. Anati anyamule machira ake azipita. Munthuyo anachitadi zimenezi ndipo anayamba kuyenda. Zimenezi zikusonyeza bwino kuti Yesu amakondadi anthu ndipo adzawathandiza m’dziko latsopano. Nkhaniyi ikusonyezanso kuti Yesu ankafufuza anthu ovutika. Ifenso tikamalalikira tiyenera kufufuza anthu omwe akudandaula chifukwa cha mavuto a m’dzikoli.

“NDANI WAGWIRA MALAYA ANGAWA?”

11. Kodi lemba la Maliko 5:25-34 likusonyeza bwanji kuti Yesu amaganizira kwambiri anthu odwala?

11 Werengani Maliko 5:25-34. Mayi wina ankadwala matenda ochititsa manyazi kwa zaka 12. Matendawa ankamulepheretsa kuchita zambiri ndipo zinkamuvuta kutumikira Mulungu bwinobwino. ‘Madokotala ambiri anam’chititsa kumva zopweteka zambiri ndipo mayiyo anawononga chuma chake chonse’ pofuna kuchira koma matendawo ankangokula. Koma tsiku lina anaganiza zoyandikira Yesu kuti achire. Iye analowa pa chigulu cha anthu n’kugwira malaya a Yesu. (Lev. 15:19, 25) Yesu anazindikira kuti mphamvu zatuluka m’thupi lake ndipo anafuna kudziwa amene anamugwira. ‘Mayiyo anachita mantha ndipo anayamba kunjenjemera kenako anafika pafupi n’kugwada pamaso pake ndikumuuza zonse.’ Yesu anazindikira kuti Yehova ndi amene wachiritsa mayiyo ndipo anamulankhula mwachifundo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”

Zozizwitsa za Yesu zimasonyeza kuti iye amatikonda kwambiri ndipo akufunitsitsa kuthetsa mavuto athu (Onani ndime 11 ndi 12)

12. (a) Kodi taphunzira kuti Yesu ndi munthu wotani? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

12 Satana amafuna kuti tiziganiza zoti ndife osafunika ndipo palibe amene amatikonda. Koma Yesu amakonda kwambiri anthu ndipo amamvera chisoni amene akudwala. Zozizwitsa zake zimatitsimikizira zimenezi. Apa n’zoonekeratu kuti tili ndi Mfumu ndiponso Mkulu wa Ansembe wachifundo kwambiri. (Aheb. 4:15) N’zovuta kumvetsa bwinobwino anthu amene akhala akudwala kwa nthawi yaitali ngati ifeyo sitinadwalepo choncho. Koma tizikumbukira kuti Yesu ankamvera chifundo anthu odwala ngakhale kuti iye sanadwalepo. Choncho tiyeni tiziyesetsa kutsatira chitsanzo chake.—1 Pet. 3:8.

“YESU ANAGWETSA MISOZI”

13. Kodi nkhani ya Lazaro imasonyeza kuti Yesu ndi wotani?

13 Yesu ankamva chisoni kwambiri akaona anthu akuvutika. Mwachitsanzo, iye ataona anthu akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro, “anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.” Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti amuukitsa pasanapite nthawi yaitali. (Werengani Yohane 11:33-36.) Yesu sanachite manyazi kulira pa gulu. Kulira kwake kunathandiza anthu kudziwa kuti ankakonda kwambiri Lazaro ndi azibale ake. Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa poukitsa mnzakeyo.—Yoh. 11:43, 44.

14, 15. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amafunitsitsa kuthetsa mavuto a anthu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu oti ‘manda achikumbutso’?

14 Baibulo limanena kuti Yesu ndi “chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo.” (Aheb. 1:3) Choncho, zozizwitsa za Yesu zimasonyeza kuti iye ndiponso Atate wake amafunitsitsa kuthetsa imfa komanso mavuto onse a anthu. Posachedwapa, Yehova ndi Yesu adzaukitsa anthu ambirimbiri. Paja Yesu ananena kuti “idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa.—Yoh. 5:28, 29.

15 Onani kuti Yesu anagwiritsa ntchito mawu oti ‘manda achikumbutso.’ Mawuwa akusonyeza kuti Mulungu amatha kukumbukira anthu amene anamwalira. Popeza iye ndi amene analenga zinthu zonse, sangavutike kukumbukira khalidwe ndiponso chinthu chilichonse chokhudza anzathu amene anamwalira. (Yes. 40:26) Mulungu akhoza kukumbukira zonsezi ndipo iye ndi Mwana wake amafunitsitsa kuwaukitsa. Nkhani ya Lazaro komanso ya anthu ena otchulidwa m’Baibulo amene anaukitsidwa zimasonyeza kuti m’dziko latsopano anthu ambirimbiri adzaukitsidwa.

MUDZAONA ZOZIZWITSA ZA YESU

16. Kodi Akhristu okhulupirika adzakhala ndi mwayi woona chiyani m’tsogolo?

16 Tikapitiriza kukhala okhulupirika tidzapulumuka pa chisautso chachikulu ndipo chimenechi chidzakhala chozizwitsa chachikulu kwambiri. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha padzachitika zinthu zodabwitsa zambiri monga kuchiritsa anthu onse. (Yes. 33:24; 35:5, 6; Chiv. 21:4) Tidzaonanso anthu akutaya zinthu monga magalasi, ndodo zoyendera ndiponso njinga za olumala. Yehova adzathandiza anthu opulumuka pa Aramagedo kuti akhale athanzi. Adzachita zimenezi n’cholinga choti anthuwo azigwira ntchito mwachangu kuti asinthe dziko lathuli kukhala paradaiso.—Sal. 115:16.

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anachita zozizwitsa? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zonse zimene mungathe kuti mudzakhale m’dziko latsopano la Mulungu?

17 Zozizwitsa zimene Yesu anachita m’mbuyomu zimathandiza a “khamu lalikulu” kuti asamakayikire zoti adzachiritsidwa m’tsogolo. (Chiv. 7:9) Zimene anachitazo zimasonyeza kuti Mwana wa Mulungu ndi wachifundo ndipo amakonda kwambiri anthu. (Yoh. 10:11; 15:12, 13) Chifundo cha Yesu chimasonyezanso kuti Yehova amakonda mtumiki wake aliyense payekha.—Yoh. 5:19.

18 Anthu akuvutika koopsa ndipo ambiri akufa. (Aroma 8:22) Tikuyembekezera kwambiri dziko latsopano pamene anthu onse adzachiritsidwa. Lemba la Malaki 4:2 limatitsimikizira kuti ‘tidzadumphadumpha ngati ana a ng’ombe onenepa.’ Tidzatero chifukwa chosangalala kwambiri kuti tamasulidwa n’kukhala angwiro. Tiyeni tsopano tizichita zonse zimene tingathe kuti tidzakhale m’dziko latsopano. Tizichita zimenezi chifukwa choyamikira kwambiri Yehova ndiponso kukhulupirira malonjezo ake. Timalimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti Yesu anachita zozizwitsa pofuna kusonyeza zimene adzachite posachedwapa akamadzalamulira dziko lonse lapansi.