Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Musafulumire Kugwedezeka pa Maganizo Anu”

“Musafulumire Kugwedezeka pa Maganizo Anu”

“Abale, . . . musafulumire kugwedezeka pa maganizo anu.”—2 ATES. 2:1, 2.

1, 2. N’chifukwa chiyani chinyengo chili ponseponse masiku ano, ndipo nkhani zabodza zikhoza kupezeka kuti? (Onani chithunzi pamwambapa.)

MASIKU ano chinyengo ndi utambwali zili ponseponse. Koma izi n’zosadabwitsa. Pajatu Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti Satana Mdyerekezi ndi katswiri pochita chinyengo, ndipo ndi wolamulira wa dzikoli. (1 Tim. 2:14; 1 Yoh. 5:19) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, mkwiyo wa Satana ukuwonjezeka chifukwa akudziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chiv. 12:12) Choncho m’pake kuti masiku ano anthu amene atengera makhalidwe a Satana akuchitanso kwambiri zachinyengo, ndipo nthawi zambiri amachitira atumiki a Mulungu.

2 Nthawi zina, mawailesi ndi manyuzipepala amafalitsa nkhani zabodza zokhudza atumiki a Yehova ndi zikhulupiriro zawo. Ndipo zinthu zabodzazi zimapezekanso pa Intaneti. Mabodzawa amasokoneza anthu ena kapenanso kuwakwiyitsa chifukwa amangowakhulupirira.

3. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisapusitsidwe?

3 Mawu a Mulungu ndi “opindulitsa pa . . . kuwongola zinthu,” choncho akhoza kutithandiza kuti tisapusitsidwe ndi chinyengo cha mdani wathuyu. (2 Tim. 3:16) Makalata a mtumwi Paulo amasonyeza kuti Akhristu ena a ku Tesalonika anasocheretsedwa ndi nkhani zabodza. Iye anawalimbikitsa kuti ‘asafulumire kugwedezeka pa maganizo awo.’ (2 Ates. 2:1, 2) Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Paulo analangiza Akhristuwo? Nanga tingagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa?

MACHENJEZO A PA NTHAWI YAKE

4. (a) Kodi Akhristu a ku Tesalonika anachenjezedwa bwanji za “tsiku la Yehova”? (b) Kodi ifeyo timachenjezedwa bwanji?

4 M’kalata yake yoyamba yopita ku mpingo wa Tesalonika,  Paulo ananena za “tsiku la Yehova.” Iye sanafune kuti abale akewo lidzawapeze ali mumdima ndiponso osakonzekera. Iye anawauza kuti iwo ndi “ana a kuwala” choncho anafunika ‘kukhalabe maso ndiponso oganiza bwino.’ (Werengani 1 Atesalonika 5:1-6.) Panopa, tikuyembekezera kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga. Chimenechi chidzakhala chiyambi cha tsiku lalikulu la Yehova. Koma chosangalatsa n’chakuti mosiyana ndi kale, tikumvetsa bwino mmene Yehova adzakwaniritsire cholinga chake. Kudzera mumpingo, timapatsidwa machenjezo a pa nthawi yake kuti tikhale oganiza bwino. Kuganizira machenjezo amenewa kungatithandize kuti tizitumikira Mulungu ‘pogwiritsa ntchito luntha la kuganiza.’—Aroma 12:1.

Paulo analembera Akhristu makalata okhala ndi machenjezo a pa nthawi yake (Onani ndime 4 ndi 5)

5, 6. (a) Kodi Paulo anafotokoza zotani m’kalata yake yachiwiri yopita kwa Atesalonika? (b) Kodi posachedwapa Mulungu achita chiyani kudzera mwa Yesu? (c) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

5 Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Paulo analemba kalata yoyamba yopita kwa Atesalonika, anawalemberanso kalata yachiwiri. M’kalata yachiwiriyi ananena za nthawi ya chisautso pamene Ambuye Yesu adzapereka chiweruzo kwa “anthu osadziwa Mulungu ndi kwa anthu osamvera uthenga wabwino.” (2 Ates. 1:6-8) Pa 2 Atesalonika 2:1, 2 (Werengani.), Paulo anasonyeza kuti anthu ena anatengeka kwambiri ndi nkhani ya tsiku la Yehova moti ankaganiza kuti lifika nthawi yomweyo. Akhristu oyambirirawa sankadziwa zambiri zokhudza mmene Yehova adzakwaniritsire cholinga chake. Ponena za ulosi, Paulo ananena kuti: “Pakuti tikudziwa moperewera ndipo tikunenera mopereweranso. Koma chokwanira chikadzafika, choperewerachi chidzatha.” (1 Akor. 13:9, 10) Koma malangizo ochokera kwa Mulungu amene Paulo, mtumwi Petulo komanso abale ena odzozedwa analemba akanawathandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba.

6 Kuti awongole zinthu, Paulo anafotokoza kuti tsiku la Yehova lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu komanso “munthu wosamvera malamulo” adzaonekera. * Kenako  idzafika nthawi yoti Ambuye Yesu ‘awononge’ anthu onse amene apusitsidwa ndi adani a Mulungu. Mtumwiyu ananena kuti anthuwo adzawonongedwa chifukwa chakuti “sanasonyeze kuti akulakalaka choonadi.” (2 Ates. 2:3, 8-10) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonda kwambiri choonadi? Kodi ndimaphunzira magaziniyi ndi mabuku athu ena kuti ndimvetse bwino mmene gulu la Yehova likufotokozera mfundo za m’Baibulo masiku ano?’

MUZISANKHA MWANZERU ANTHU OCHEZA NAWO

7, 8. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanasocheretsa Akhristu oyambirira? (b) Kodi Akhristu ayenera kusamala kwambiri ndi chiyani masiku ano?

7 Komatu Akhristu akhoza kusocheretsedwa ndi zinthu zina kuwonjezera pa anthu ampatuko ndiponso zinthu zimene iwo amaphunzitsa. Paja Paulo analembera Timoteyo kuti “kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” Ndiyeno ananenanso kuti “pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.” (1 Tim. 6:10) Ena akhoza kusocheretsedwa ndi “ntchito za thupi.”—Agal. 5:19-21.

8 Komabe tingamvetse chifukwa chake Paulo anachenjeza mwamphamvu Akhristu a ku Tesalonika kuti asamale ndi anthu amene anawatchula kuti “atumwi onama.” Ena mwa iwo ankalankhula “zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” (2 Akor. 11:4, 13; Mac. 20:30) Pa nthawi ina, Yesu anayamikira mpingo wa ku Efeso chifukwa chakuti ‘sunkalekerera anthu oipa.’ Akhristu a ku Efeso ‘ankayesa’ anthuwa n’kupeza kuti sanali atumwi enieni koma onama. (Chiv. 2:2) Chochititsa chidwi n’chakuti m’kalata yake yachiwiri yopita kwa Atesalonika, Paulo anapereka malangizo akuti: “Tsopano tikukulangizani abale m’dzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe m’bale aliyense woyenda mosalongosoka.” Kenako anatchula mwachindunji za Akhristu amene ‘sankafuna kugwira ntchito.’ (2 Ates. 3:6, 10) Ngati ananena kuti anthu amenewa ndi oyenda mosalongosoka, kuli bwanji anthu amene akuyambitsa mpatuko. Akhristu anayenera kupewa anthu oterewa chifukwa anali oopsa. Nafenso masiku ano tiyenera kuwapewa.—Miy. 13:20.

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ngati anthu atayamba kulankhula maganizo awoawo kapena mawu otsutsa gulu la Yehova?

9 Panopa chisautso chachikulu ndiponso mapeto a dziko loipali zili pafupi kwambiri. Choncho machenjezo ochokera kwa Mulungu amene Akhristu oyambirira anapatsidwa ndi ofunika kwambiri masiku ano. Sitikufuna kuti tiphonye cholinga cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kulephera kulandira moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padziko lapansi. (2 Akor. 6:1) Tiyenera kusamala kwambiri ngati anthu ena amene amabwera kumisonkhano akufuna kutikopa polankhula maganizo awoawo kapena mawu otsutsa gulu la Yehova.—2 Ates. 3:13-15.

“GWIRANI MWAMPHAMVU MIYAMBO”

10. Kodi Akhristu a ku Tesalonika analimbikitsidwa kuti asasiye miyambo iti?

10 Paulo analimbikitsa abale a ku Tesalonika kuti ‘akhale olimba’ ndipo asasiye “miyambo” imene anaphunzitsidwa. (Werengani 2 Atesalonika 2:15.) Kodi Atesalonikawo anaphunzitsidwa “miyambo” iti? Miyamboyi inali ziphunzitso za Yesu ndiponso zimene Mulungu anauzira Paulo ndi anthu ena kuti alembe. Zambiri mwa zinthu zimenezi zinadzalembedwa m’mabuku a m’Baibulo. Choncho Paulo sankanena za miyambo imene chipembedzo chonyenga chinkaphunzitsa. Iye anayamikira abale a ku Korinto ponena kuti: “Mukundikumbukira m’zinthu zonse, ndipo mukusunga miyambo monga mmene ndinaiperekera  kwa inu.” (1 Akor. 11:2) Miyambo imeneyi inali yodalirika chifukwa chakuti inachokera kwa Mulungu.

11. Kodi chimachitika n’chiyani anthu ena akauzidwa zinthu zabodza?

11 M’kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo anasonyeza kuti munthu angafooke n’kusiya chikhulupiriro m’njira ziwiri. (Werengani Aheberi 2:1; 3:12.) Iye ananena kuti munthu akhoza ‘kutengeka pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro’ kapena akhoza ‘kungochoka.’ Nthawi zina, boti limatha kutengeka ndi mafunde n’kumasuntha mosaonekera bwinobwino, ndiyeno mwapang’onopang’ono limapezeka kuti lili kutali. Koma nthawi zina boti limatha kusuntha chifukwa chakuti mwiniwake akulikankhira kwakuya. Zinthu ziwirizi zikusonyeza zimene zimachitika ndi anthu amene apusitsidwa n’kuyamba kusiya kukhulupirira kwambiri choonadi.

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatisokoneze potumikira Mulungu?

12 N’kutheka kuti izi n’zimene zinachitikira Akhristu ena a ku Tesalonika. Zimenezi zikhoza kuchitikiranso Akhristu masiku ano. Pali zinthu zambiri zimene zingatiwonongere nthawi. Mwachitsanzo, anthu amawononga maola ambiri pa masewera, potumizirana mauthenga pa foni ndi pa Intaneti kapena pochita zosangalatsa zina. Zinthu zimenezi zikhoza kusokoneza Mkhristu. Akhoza kusiya kuchita khama popemphera kuchokera pansi pa mtima, kuphunzira Mawu a Mulungu, kupezeka pa misonkhano ndiponso kulalikira. Kodi tingatani kuti tisafulumire kugwedezeka pa maganizo athu?

N’CHIYANI CHINGATITETEZE KUTI TISAGWEDEZEKE?

13. (a) Mogwirizana ndi ulosi, kodi anthu ambiri masiku ano ali ndi maganizo otani? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti chikhulupiriro chathu chisafooke?

13 Chinthu chofunika kwambiri n’kukumbukira kuti tili “m’masiku otsiriza” komanso kudziwa kuopsa kocheza ndi anthu amene savomereza mfundo imeneyi. Ponena za masiku otsiriza ano, mtumwi Petulo ananena kuti: “Kudzakhala onyodola amene azidzatsatira zilakolako zawo, amene azidzati: ‘Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.’” (2 Pet. 3:3, 4) Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kuliphunzira kungatithandize kuti tisaiwale mfundo yakuti tili “m’masiku otsiriza.” Mpatuko umene unaloseredwa uja unayambika kalekale ndipo ulipobe. “Munthu wosamvera malamulo” adakalipo ndipo akupitiriza kutsutsa atumiki a Mulungu. Choncho tiyenera kukhalabe tcheru podziwa kuti tsiku la Yehova layandikira kwambiri.—Zef. 1:7.

Kukonzekera bwino ndiponso kuchita khama mu utumiki zingatithandize kuti tisafulumire kugwedezeka pa maganizo athu (Onani ndime 14 ndi 15)

14. Kodi kuchita khama potumikira Mulungu kungatiteteze bwanji?

14 Anthu ambiri aona kuti kuchita khama pa ntchito yolalikira kumawathandiza kuti akhale tcheru ndiponso asagwedezeke pa maganizo awo. Yesu Khristu, yemwe ndi Mutu wa mpingo, anauza ophunzira ake kuti aziphunzitsa anthu a mitundu yonse ndiponso kuwathandiza kusunga zinthu zonse zimene iye anawalamula. Yesuyo anapereka malangizowa podziwa kuti kugwira ntchitoyi kungawateteze. (Mat. 28:19, 20) Choncho kuti timvere malangizowa, tiyenera kuchita khama pa ntchito yolalikira. Abale a ku Tesalonika sakanangokhutira ndi kugwira ntchitoyi mwamwambo chabe kapena mosaikirapo mtima. Kumbukirani mawu amene Paulo anawauza akuti: “Musazimitse moto wa mzimu. Musanyoze mawu aulosi.” (1 Ates. 5:19, 20) Kunena zoona maulosi amene timaphunzira ndiponso kuuza anthu ena ndi osangalatsa kwambiri.

15. Kodi ndi zinthu zofunika ziti zimene tingakambirane pa Kulambira kwa Pabanja?

 15 Choncho tiyenera kuthandiza banja lathu kukhala ndi luso lophunzitsa mu utumiki. Abale ndi alongo ambiri aona kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito nthawi ina ya Kulambira kwa Pabanja kuti akambirane zimene angachite mu utumiki. Mwina mungakambirane mmene mungachitire maulendo obwereza. Mwachitsanzo, kodi mudzakambirane naye zotani munthuyo? Kodi iye angachite chidwi ndi nkhani ziti? Kodi mukhoza kumupeza pa tsiku liti ndiponso nthawi yanji? Anthu ena amakonda kugwiritsa ntchito nthawi ina ya Kulambira kwa Pabanja kuti akonzekere misonkhano ya mpingo. Kodi mungachite chiyani kuti mudzathe kuyankha bwino pa misonkhanoyo? Kuyankha bwino pa misonkhano kungalimbitse chikhulupiriro chanu ndiponso kukuthandizani kuti musagwedezeke pa maganizo anu. (Sal. 35:18) Kuchita Kulambira kwa Pabanja kungakuthandizeni kuti musapusitsidwe kapena kukhala ndi mtima wokayikakayika.

16. N’chiyani chimathandiza Akhristu odzozedwa kuti akhalebe oganiza bwino?

16 Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akuthandiza anthu ake kumvetsa bwino ulosi wa m’Baibulo. Izi zimatithandiza kuti tisamakayikire zimene watilonjeza. Odzozedwa akuyembekezera kukakhala limodzi ndi Khristu kumwamba. Chiyembekezo chimenechi chimawathandiza kukhalabe oganiza bwino. Tinganene kuti mawu a Paulo amene analembera Atesalonika akufotokozanso za iwowo. Paulo anati: “Tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale okondedwa ndi Yehova. Tiyenera kutero chifukwa Mulungu anakusankhani . . . mwa kukuyeretsani ndi mzimu, ndiponso mwa chikhulupiriro chanu m’choonadi.”—2 Ates. 2:13.

17. Kodi inuyo mwalimbikitsidwa ndi mawu ati pa 2 Atesalonika 3:1-5?

17 Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi ayeneranso kuyesetsa kuti asafulumire kugwedezeka pa maganizo awo. Ngati mukuyembekezera kudzakhala padzikoli, muyenera kutsatira malangizo achikondi amene Paulo analembera odzozedwa anzake a ku Tesalonika. (Werengani 2 Atesalonika 3:1-5.) Tonsefe tiyenera kuyamikira kwambiri malangizowa. M’makalata opita kwa Atesalonika muli machenjezo amene angatithandize kuti tisapusitsidwe kapena kukhala ndi maganizo athuathu pa zinthu zimene sizinafotokozedwe m’Malemba. Popeza kuti mapeto ayandikira kwambiri, Akhristufe tiyenera kuyamikira kwambiri machenjezo amenewa.

^ ndime 6 Pa Machitidwe 20:29, 30, Paulo ananena kuti mumpingo wachikhristu mudzapezeka anthu ena amene “adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” Izi n’zimene zinachitikadi patapita nthawi chifukwa anthu mumpingo anayamba kugawikana m’magulu awiri. Ena anali atsogoleri pomwe ena anali anthu wamba. Pofika zaka za m’ma 200 C.E., “munthu wosamvera malamulo” anali ataonekera monga atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi achikhristu.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 1990, tsamba 10 mpaka 14.