Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Philippines

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Philippines

ZAKA 10 zapitazo, Gregorio ndi mkazi wake Marilou, omwe ali ndi zaka za m’ma 30, ankachita upainiya mumzinda wa Manila komanso ankagwira ntchito yolembedwa. Sizinali zophweka koma ankakwanitsa kuchita zimenezi. Ndiyeno Marilou anakwezedwa pa ntchito yake n’kukhala manijala wa banki. Iye anati: “Tinali pa ntchito zabwino ndipo moyo wathu unali wawofuwofu.” Iwo ankapezadi ndalama zambiri moti anaganiza zomangitsa chinyumba chakum’mawa kwa mzindawu pa mtunda wa makilomita 19. Anapeza anthu omanga n’kugwirizana kuti aziwalipira mwezi uliwonse kwa zaka 10.

“NDINKAONA KUTI NDIKUBERA YEHOVA”

Marilou anati: “Ntchito yanga yatsopano inkafuna nthawi komanso mphamvu zanga zambiri moti kusonkhana ndiponso kulalikira sizinkandisangalatsanso. Ndinkaona kuti ndikubera Yehova chifukwa chakuti sindinkachitanso zimene ndinamulonjeza podzipereka kwa iye.” Gregorio ndi Marilou sankasangalala ndi zimenezi choncho tsiku lina anakambirana n’kuona kuti sakuchita bwino pa moyo wawo. Gregorio anati: “Tinkafuna kusintha zinthu koma sitinkadziwa mmene tingachitire zimenezi. Popeza tilibe udindo wolera ana, tinakambirana zimene  tingasinthe kuti tizichita zambiri potumikira Yehova ndipo tinapemphera kwa Mulungu kuti atithandize.”

Pa nthawiyo, nkhani zambiri zimene anamvetsera zinali zokhudza kukatumikira kudera kumene kulibe ofalitsa okwanira. Gregorio anati: “Tinaona kuti Yehova ankayankha pemphero lathu kudzera m’nkhanizi.” Iwo anapemphanso Yehova kuti awalimbitse mtima kuti asankhe zochita mwanzeru. Koma vuto lawo linali chinyumba chimene ankamanga chija. Iwo anali atapereka kale ndalama za zaka zitatu. Kodi anatani? Marilou anati: “Tinkadziwa kuti tikauza omanga nyumbawo kuti asiye, tiluza ndalama zonse zimene tinapereka, zomwe zinali zambiri. Koma tinaona kuti tiyenera kusankha pakati pa kuika patsogolo zofuna za Yehova kapena zofuna zathu.” Potengera chitsanzo cha mtumwi Paulo, anasiya kumanga nyumbayo, anasiya ntchito ndiponso anagulitsa zinthu zambiri. Kenako anasamukira kumudzi wakutali womwe uli pachilumba cha Palawan ndipo uli pa mtunda wa makilomita 480 kum’mwera kwa Manila.—Afil. 3:8.

‘ANAPHUNZIRA CHINSINSI’

Gregorio ndi Marilou asanasamuke, anayamba kukonzekera kukhala moyo wosalira zambiri. Koma sankadziwa kuti moyo wawo ukakhala wotani mpaka pamene anafika kumaloko. Marilou anati: “Tinadabwa kwambiri chifukwa kunalibe magetsi komanso zinthu zina zamakono. Mwachitsanzo, kwathu tinkaphika pamagetsi, koma tsopano tinkafunika kudula nkhuni n’kukoleza moto kuti tiphike. Kunalibe masitolo akuluakulu, malesitanti ndi zinthu zina zimene ndinkazipeza mosavuta m’tauni.” Koma Gregorio ndi Marilou ankadzikumbutsa chifukwa chake anasamuka, ndipo pasanapite nthawi anazolowera moyo wa kumeneko. Marilou anati: “Panopa ndimasangalala kuona chilengedwe chokongola monga kuwala kwa nyenyezi usiku. Koma chosangalatsa kwambiri n’kuona anthu akusangalala pamene tikuwalalikira. Chifukwa chotumikira kuno, ‘taphunzira chinsinsi’ chokhala okhutira.”—Afil. 4:12.

“Palibe chosangalatsa kwambiri kuposa kuona anthu atsopano akubwera mumpingo wachikhristu. Panopa tikuona kuti moyo wathu uli ndi cholinga chenicheni kuposa kale.”—Gregorio ndi Marilou

Gregorio anati: “Pamene tinkafika kuno, kunali abale ndi alongo 4 okha. Iwo anasangalala kwambiri nditayamba kukamba nkhani ya onse mlungu uliwonse ndiponso kuimba gitala poimba nyimbo za Ufumu.” M’chaka chimodzi chokha, banjali linaona kagulu kameneka kakukula n’kukhala mpingo wa ofalitsa 24. Gregorio anati: “Abale ndi alongo mumpingowu amasonyeza kuti amatikonda ndipo zimenezi zimatikhudza kwambiri mumtima.” Tsopano papita zaka 6 akutumikira m’dera limeneli, ndipo ananena kuti: “Palibe chosangalatsa kwambiri kuposa kuona anthu atsopano akubwera mumpingo wachikhristu. Panopa tikuona kuti moyo wathu uli ndi cholinga chenicheni kuposa kale.”

‘NDALAWA N’KUONA KUTI YEHOVA NDI WABWINO’

M’dziko la Philippines abale ndi alongo pafupifupi 3,000 asamukira kumadera kumene kulibe ofalitsa  okwanira. Pafupifupi 500 mwa iwo ndi alongo osakwatiwa. Mlongo wina wosakwatiwa amene wasamuka ndi Karen.

Karen

Karen ndi wa zaka zoposa 20 ndipo anakulira m’tauni ya Baggao m’dera la Cagayan. Iye ali wamng’ono, ankafunitsitsa kuchita zambiri potumikira Mulungu. Karen anati: “Ndinkadziwa kuti nthawi imene yatsala yafupika ndipo anthu ambiri akufunikira kumva uthenga wa Ufumu, choncho ndinkafunitsitsa kukatumikira kumene kulibe ofalitsa okwanira.” Ngakhale kuti ena a m’banja lake ankamulimbikitsa kuchita maphunziro apamwamba m’malo mosamukira kudera lakutali, iye ankapempha Yehova kuti amuthandize kusankha mwanzeru. Karen ankalankhulanso ndi anthu amene anali kutumikira kudera lakutali. Ndiyeno, ali ndi zaka 18 anasamukira kudera lina la pa mtunda wa makilomita 64 kuchokera kwawo.

Gawo la mpingo waung’ono kumene Karen anakatumikira lili m’mphepete mwa nyanja ya Pacific ndipo lili ndi mapiri ambiri. Karen anati: “Kuti tikafike kumpingo watsopanowu kuchokera kwathu, tinayenda ulendo wa masiku atatu. Tinakwera n’kutsetsereka mapiri komanso kuwoloka mitsinje nthawi 30.” Iye ananenanso kuti: “Nthawi zina ndimayenda maola 6 kuti ndikafike kwa anthu ena amene ndikuphunzira nawo Baibulo. Ndimagona kunyumba kwawo kenako n’kuyendanso maola 6 tsiku lotsatira pobwerera kunyumba.” Kodi iye akungowononga nthawi yake? Karen anavomereza kuti nthawi zina miyendo yake imamuwawa, koma kenako anasekerera kwambiri n’kunena kuti: “Pa nthawi ina ndinali ndi maphunziro a Baibulo okwana 18, choncho ndinganene kuti ‘ndalawa n’kuona kuti Yehova ndi wabwino.’”—Sal. 34:8.

“NDAPHUNZIRA KUDALIRA YEHOVA”

Sukhi

Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Sukhi, amene ali ndi zaka zoposa 40, anasamukira ku Philippines kuchokera ku United States. N’chifukwa chiyani anasankha kuchita zimenezi? Mu 2011 anapita ku msonkhano wadera kumene anamva banja lina likufotokoza zimene linachita kuti lisamukire ku Mexico. Banjali linagulitsa katundu wawo wambiri n’kusamukira m’dzikoli kuti likathandize pa ntchito yolalikira. Mlongoyu anati: “Zimene banjali linanena zinandithandiza kuti ndiyambe kuganizira zolinga zatsopano.” Sukhi, yemwe ndi mmwenye, atamva kuti pakufunika ofalitsa ambiri oti akalalikire anthu olankhula Chipunjabi ku Philippines, anaganiza zopitako. Kodi anakumana ndi vuto lililonse?

Sukhi anati: “Kusankha zinthu zoti ndigulitse ndi zoti ndisunge kunali kovuta kuposa mmene ndinkaganizira. Komanso ndinkakhala ndekha motakasuka kwa zaka 13, koma kenako ndinayamba kukhala ndi achibale anga. Zinali zovuta, komabe zinandithandiza kukonzekera kukhala moyo wosalira zambiri.” Kodi atasamukira ku Philippines anakumana  ndi mavuto otani? Iye anati: “Vuto langa lalikulu linali kuopa tizilombo komanso kulakalaka kunyumba. Koma ndinaphunzira kudalira kwambiri Yehova kuposa kale.” Kodi anasankha bwino kusamukira kumeneko? Akumwetulira, Sukhi anati: “Yehova akutiuza kuti, ‘Ndiyeseni kuti muone ngati sindidzakukhuthulirani madalitso.’ Ndimaona kuti mawu amenewa ndi oona pamene munthu yemwe ndakumana naye mu utumiki wandifunsa kuti, ‘Kodi mudzabweranso liti? Ndili ndi mafunso ambirimbiri.’ Ndimasangalala kwambiri kuthandiza anthu amene akumva njala ya Mawu a Mulungu.” (Mal. 3:10) Sukhi ananenanso kuti: “Kunena zoona, chinthu chovuta kwambiri chinali kusankha zosamuka. Koma nditasankha kusamuka, zinali zosangalatsa kwambiri kuona mmene Yehova anandithandizira.”

“SINDINAOPENSO”

M’bale wina wazaka zoposa 35 dzina lake Sime, yemwe ali ndi banja, anasamuka ku Philippines kupita kudziko lina la ku Middle East kuti akagwire ntchito yabwino. Ali kudzikolo, analimbikitsidwa ndi woyang’anira dera ndiponso nkhani imene m’bale wina wa m’Bungwe Lolamulira anakamba. Zimenezi zinamuthandiza kuti ayambe kuika patsogolo kutumikira Yehova. Sime anati: “Ndinkaopa kwambiri kusiya ntchito yangayo.” Komabe anaisiya n’kubwerera ku Philippines. Panopa, Sime ndi mkazi wake Haidee amatumikira m’dera la Davao del Sur kum’mwera kwa Philippines. Kumeneko kuli gawo lalikulu kwambiri ndipo kukufunika ofalitsa ambiri. Sime anati: “Ndikusangalala kwambiri kuti sindinaopenso kusiya ntchito yangayo ndipo ndinayamba kuika patsogolo kutumikira Yehova. Palibe chosangalatsa pa moyo kuposa kutumikira Yehova ndi zonse zimene tili nazo.”

Sime ndi Haidee

“KUMASANGALATSA KWAMBIRI”

Ramilo ndi Juliet ndi apainiya azaka zoposa 30. Iwo atamva kuti mpingo womwe uli pa mtunda wa makilomita 30 kuchokera kwawo ukufunikira thandizo, anadzipereka kuti akathandize. Choncho mlungu uliwonse, ngakhale pamene nyengo sili bwino, Ramilo ndi Juliet amapita kumeneko pa njinga yawo yamoto kukasonkhana komanso kukalalikira. Iwo amadutsa m’misewu yokumbikakumbika komanso m’milatho yoopsa. Komabe, akusangalala kuti akuchita zambiri mu utumiki. Ramilo anati: “Ine ndi mkazi wanga tili ndi maphunziro a Baibulo okwana 11. Kutumikira kumene kukufunika ofalitsa ambiri si kophweka, koma kumasangalatsa kwambiri.”—1 Akor. 15:58.

Juliet ndi Ramilo

Kodi mungakonde kudziwa zimene mungachite kuti mukatumikire kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri m’dziko lanu kapena m’dziko lina? Ngati ndi choncho, kambiranani ndi woyang’anira dera wanu, komanso werengani nkhani yakuti “Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2011.