Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
“Mulungu wa Yakobo . . . akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”—YES. 2:3.
1, 2. Kodi zitsanzo za anthu omwe analembedwa m’Baibulo zingatithandize bwanji?
MOSAKAYIKIRA mukudziwa kuti mukhoza kupindula ndi zimene zalembedwa m’Baibulo. M’Baibulo muli zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika amene anasonyeza makhalidwe abwino ofunika kuwatsanzira. (Aheb. 11:32-34) Mukhoza kuwerenganso za amuna ndi akazi amene sitiyenera kutengera maganizo ndiponso zochita zawo chifukwa zinalembedwa kuti zitichenjeze.
2 Ndiyeno pali anthu ena otchulidwa m’Baibulo amene anachita zinthu zabwino kwambiri komanso zinthu zoipa zimene tiyenera kupewa. Taganizirani za Davide amene anali m’busa wamba koma n’kusintha kukhala mfumu yamphamvu. Iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokonda choonadi komanso kukhulupirira Yehova. Koma Davide yemweyo anachita machimo akuluakulu monga kuchita chigololo ndi Bateseba, kuphetsa Uriya komanso kuwerenga anthu pa zifukwa zosayenera. Koma panopa tiyeni tikambirane za mwana wake Solomo amene anali mfumu komanso wolemba Baibulo. Tiyamba n’kukambirana mbali ziwiri zimene anapereka chitsanzo chabwino.
“Nzeru za Solomo”
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Solomo ndi chitsanzo chabwino kwa ife?
3 Yesu Khristu, yemwe ndi Solomo Wamkulu, anayamikira kwambiri Mfumu Solomo ndipo anasonyeza kuti iye anali chitsanzo chabwino. Yesu anauza Ayuda ena amene sankamukhulupirira kuti: “Mfumukazi ya kum’mwera adzaiukitsa kwa akufa limodzi ndi m’badwo uwu ndipo idzautsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.” (Mat. 12:42) Solomo anadziwika kwambiri chifukwa cha nzeru zake ndipo anatilimbikitsa kupeza nzeru.
4, 5. Kodi Solomo anapeza bwanji nzeru zake ndipo zikusiyana bwanji ndi mmene ifeyo tingapezere nzeru?
4 Kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Mulungu anaonekera kwa Solomo m’maloto n’kumuuza kuti apemphe zimene akufuna. Chifukwa chakuti Solomo ankazindikira zoti sadziwa zambiri iye anapempha nzeru. (Werengani 1 Mafumu 3:5-9.) Ndiyeno Mulungu anasangalala kuti Solomo wapempha nzeru osati chuma kapena ulemerero choncho anamupatsa “mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu” komanso chuma. (1 Maf. 3:10-14) Malinga ndi zimene Yesu ananena, nzeru za Solomo zinamveka patali kwambiri moti mfumukazi ya ku Sheba inamva n’kuyenda mtunda wautali kwambiri kuti ikadzionere yokha.—1 Maf. 10:1, 4-9.
5 Ife sitiyembekezera kulandira nzeru m’njira yozizwitsa. Solomo ananena kuti “Yehova amapereka nzeru” koma analemba kuti tiyenera kuchita khama kuti tipeze nzeruzo. Iye anati tiyenera ‘kumvetsera nzeru ndi khutu lathu ndi kuika mtima wathu pa kuzindikira.’ Pa nkhani yopeza nzeruyi, iye anagwiritsanso ntchito mawu ngati ‘kuitana,’ ‘kufunafuna’ ndiponso ‘kufufuza.’ (Miy. 2:1-6) Izi zikusonyezeratu kuti tikhoza kupeza nzeru.
6. Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo chabwino cha Solomo pa nkhani ya nzeru?
6 Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikutsatira chitsanzo cha Solomo pa nkhani yoona kuti Miy. 2:9.
nzeru yochokera kwa Mulungu ndi yamtengo wapatali?’ Mavuto a zachuma achititsa anthu ambiri kuganizira kwambiri za ntchito komanso ndalama zawo. Ena amalola kuti zimenezi ziwachititse kusankha maphunziro apamwamba. Nanga bwanji za inu ndi banja lanu? Kodi zosankha zanu zimasonyeza kuti mumaona kuti nzeru yochokera kwa Mulungu ndi yamtengo wapatali ndipo mukufuna kuipeza? Kodi kusintha zolinga zanu kungakuthandizeni kuti mupeze nzeru zambiri? Dziwani kuti kupeza nzeru ndiponso kuitsatira kudzakuthandizani kwa moyo wanu wonse. Solomo analemba kuti: “Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.”—Kulimbikitsa Kulambira Koona Kunabweretsa Mtendere
7. Kodi panali dongosolo lotani kuti kachisi wa Mulungu amangidwe?
7 Chakumayambiriro kwa ulamuliro wake, Solomo anamanga kachisi wokongola kwambiri kuti alowe m’malo mwa chihema chimene chinkagwiritsidwa ntchito kuyambira masiku a Mose. (1 Maf. 6:1) N’zoona kuti kachisiyu amatchedwa kachisi wa Solomo, koma sikuti iye anam’manga kuti atchuke. Ndipo si iye amene anayambitsa nzeru zomanga kachisiyo. Davide ndi amene anayamba kukhala ndi maganizo omanga kachisi. Ndipo Mulungu ndi amene anauza Davide mapulani onse a kachisiyo. Davide ndi amenenso anapereka ndalama zambiri zomangira kachisiyu. (2 Sam. 7:2, 12, 13; 1 Mbiri 22:14-16) Koma Solomo ndi amene anagwira ntchito yomanga kachisiyu ndipo inatenga zaka 7 ndi hafu.—1 Maf. 6:37, 38; 7:51.
8, 9. (a) Kodi Solomo anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yosaleka kugwira ntchito zabwino? (b) Kodi chinachitika n’chiyani Solomo atalimbikitsa kulambira koona?
8 Solomo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yosaleka kugwira ntchito zabwino ndipo ankaika ntchitozo pamalo oyamba pa moyo wake. Atamaliza kumanga kachisi n’kuikamo likasa la pangano, Solomo anapereka pemphero pagulu. M’pempherolo ananena kuti: “Maso anu akhale akuyang’ana nyumba ino usiku ndi usana. Akhale akuyang’ana malo amene munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala kumeneko,’ kuti mumvere pemphero limene mtumiki wanu akupemphera atayang’ana kumalo ano.” (1 Maf. 8:6, 29) Aisiraeli ndiponso alendo akanatha kupemphera akuyang’ana nyumba imeneyi yomwe inali ndi dzina la Mulungu.—1 Maf. 8:30, 41-43, 60.
9 Kodi chinachitika n’chiyani Solomo atalimbikitsa 1 Maf. 8:65, 66) Pa zaka 40 zimene Solomo analamulira kunali mtendere ndipo zinthu zinkayenda bwino. (Werengani 1 Mafumu 4:20, 21, 25.) Salimo 72 limanena za mtendere umenewu ndipo limatithandiza kumvetsa kwambiri madalitso amene tidzasangalala nawo mu ulamuliro wa Yesu Khristu, yemwe ndi Solomo Wamkulu.—Sal. 72:6-8, 16.
kulambira koona? Pambuyo pa chikondwerero chotsegulira kachisi, anthu “anapita akusangalala, chimwemwe chitadzaza mumtima, chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake ndi anthu ake Aisiraeli.” (Chenjezo pa Zimene Solomo Anachita
10. Kodi ndi zinthu ziti zimene Solomo analakwitsa zomwe ambiri amazidziwa kwambiri?
10 N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zina zimene Solomo anachita ndi chenjezo kwa ife? Poyamba taganizirani za akazi ake ndiponso akazi apambali achilendo. Pa nkhani imeneyi Baibulo limati: “Pamene iye anali kukalamba, akazi ake anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 11:1-6) N’zodziwikiratu kuti inuyo simungafune kuchita zinthu zopanda nzeru ngati zimenezi. Koma kodi ndi chenjezo lokhali limene tikupeza pa nkhani ya Solomo? Tiyeni tione zinthu zina zimene anachita pa moyo wake, zomwe anthu saziganizira kwenikweni, n’kukambirana machenjezo amene tingapeze.
11. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza banja loyamba la Solomo?
11 Solomo analamulira zaka 40. (2 Mbiri 9:30) Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo ya pa 1 Mafumu 14:21? (Werengani.) Vesili likusonyeza kuti Solomo atamwalira, mwana wake Rehobowamu anayamba kulamulira ali ndi zaka 41. Mayi ake anali a Naama omwe anali “Muamoni.” Izi zikutanthauza kuti Solomo asanakhale mfumu anakwatira mkazi wachilendo wa mtundu wolambira mafano umene unali pa chidani ndi Aisiraeli. (Ower. 10:6; 2 Sam. 10:6) Kodi mkaziyu ankalambira mafano? Kaya poyambapo ankalambira mafano, ayenera kuti anasiya n’kuyamba kulambira koona ngati mmene anachitira Rahabi ndi Rute. (Rute 1:16; 4:13-17; Mat. 1:5, 6) Koma Solomo ayenera kuti anali ndi apongozi, alamu ake ndiponso achibale achiamoni amene sankatumikira Yehova.
12, 13. Kodi Solomo analakwitsa chiyani kumayambiriro kwa ulamuliro wake ndipo n’kutheka kuti ankaganiza bwanji?
12 Koma zinthu zinasintha kwambiri Solomo atakhala mfumu. Iye “anachita mgwirizano wa ukwati ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anatenga mwana wamkazi wa Faraoyo n’kubwera naye ku Mzinda wa Davide.” (1 Maf. 3:1) Kodi mkazi wa ku Iguputoyu anayamba kulambira koona ngati mmene anachitira Rute? Baibulo silinena kuti anachita zimenezi. M’malomwake Solomo anamumangira nyumba iyeyo (mwinanso ndi antchito ake ochokera ku Iguputo) kunja kwa Mzinda wa Davide. N’chifukwa chiyani anamanga kunja kwa mzindawu? Malemba amati iye anachita zimenezi chifukwa chakuti sizinali zoyenera kuti munthu wolambira mafano azikhala pafupi ndi likasa la pangano.—2 Mbiri 8:11.
13 Mwina Solomo ankaganiza kuti zimenezi zingamuthandize kuti pakhale ubale wabwino pakati pa dziko lake ndi la Iguputo. Koma kodi chimenechi ndi chifukwa chomveka? Izi zisanachitike, Mulungu anali ataletsa kukwatirana ndi Akanani ndipo anachita kutchula mwachindunji mitundu ina. (Eks. 34:11-16) Kodi Solomo ankaganiza kuti Aiguputo sanatchulidwe pa mndandanda wa mitunduyi? Ngati ankaganiza choncho kodi tingati n’chifukwa chomveka? Pochita zimenezi ananyalanyaza chenjezo limene Yehova anapereka loti anthu oterewa angapatutse Mwisiraeli kuti ayambe kulambira konyenga.—Werengani Deuteronomo 7:1-4.
14. Kodi kuganizira zinthu zolakwika zimene Solomo anachita kungatithandize kupewa chiyani?
14 Kodi tikuphunzira chiyani pa zinthu zolakwika zimene Solomo anachitazi? Mlongo angaganize kuti palibe vuto kuchita chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira n’kunyalanyaza malangizo a Mulungu akuti azikwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Munthu angadzikhululukirenso pochita masewera kapena zochita zina kusukulu zomwe si mbali ya maphunziro. Wina angakane kuuza boma ndalama zonse zimene wapeza n’cholinga choti apewe msonkho kapena anganame pamene wafunsidwa za chinthu chochititsa manyazi chimene wachita. Apa mfundo ndi yakuti Solomo ankaganiza molakwika n’kuyamba kunyalanyaza malamulo a Mulungu ndipo izi zingathe kutichitikira ifenso.
15. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chifundo kwa Solomo koma sitiyenera kuiwala za chiyani?
15 N’zochititsa chidwi kuti pambuyo pofotokoza za ukwati wa Solomo ndi mwana wa Faraoyu, Baibulo limanena kuti Mulungu anamupatsa nzeru zimene anapempha komanso chuma. (1 Maf. 3:10-13) Solomo ananyalanyaza malangizo a Mulungu koma Baibulo silinena kuti Yehova anamukaniratu nthawi yomweyo kapena kumudzudzula mwamphamvu. Izi zikusonyeza kuti Mulungu amadziwa kuti ndife opanda ungwiro ndipo tinapangidwa kuchokera ku fumbi. (Sal. 103:10, 13, 14) Chomwe sitiyenera kuiwala n’chakuti zotsatira za zochita zathu zikhoza kuonekera panopa kapena m’tsogolo.
Solomo Anakwatira Akazi Ambirimbiri
16. Kodi Solomo ananyalanyaza lamulo liti pamene anakwatira akazi ambirimbiri?
16 M’buku la Nyimbo ya Solomo, mfumuyi inachemerera namwali wina n’kumanena kuti anali wokongola kwambiri kuposa mfumukazi 60 ndi adzakazi 80. (Nyimbo 6:1, 8-10) Ngati Solomo ankanena zochitikadi pa moyo wake ndiye kuti pa nthawiyo anali ndi akazi ambiri. Ngakhale akazi ambiri kapena onsewo akanakhala olambira Mulungu woona, Mulungu ananena kudzera mwa Mose kuti mfumu ya Isiraeli siyenera ‘kuchulukitsa akazi kuti mtima wake ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Apanso Yehova sanasiyiretu Solomo moti anamudalitsa pomugwiritsa ntchito kuti alembe buku la m’Baibulo la Nyimbo ya Solomo.
17. Kodi ndi mfundo yoona iti imene sitiyenera kuiiwala?
17 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Solomo akanatha kunyalanyaza malamulo a Mulungu popanda kukumana ndi vuto lililonse? Ayi. Ndi mmenenso zilili masiku ano. Zikungosonyeza kuti Mulungu amapirira zochita za anthu kwa nthawi ndithu. Koma sizikutanthauza kuti ngati munthu sanakumane ndi mavuto nthawi imene wanyalanyaza malangizo a Mulungu ndiye kuti basi sadzakumana nawo. Pajatu Solomo analemba kuti: “Popeza anthu ochita zoipa sanalangidwe msanga, n’chifukwa chake mtima wa ana a anthu wakhazikika pa kuchita zoipa.” Ndiyeno anapitiriza kuti: “Ine ndikudziwa kuti anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino, chifukwa chakuti anali kumuopa.”—Mlal. 8:11, 12.
18. Kodi zimene Solomo anachita zikutsimikizira bwanji mfundo ya pa Agalatiya 6:7?
18 N’zomvetsa chisoni kuti Solomo sanapitirize kutsatira mfundo yoona imeneyi. N’zoona kuti anachita zinthu zabwino zambiri ndipo Mulungu anamudalitsa kwambiri. Koma kenako anangoyamba kuchita zoipa ndipo ichi chinangokhala chizolowezi chake. Uwu ndi umboni wakuti zimene Paulo analemba n’zoona. Iye anati: “Musanyengedwe, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agal. 6:7) Patapita nthawi, Solomo anakumana ndi mavuto chifukwa chonyalanyaza malangizo a Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Mfumu Solomo inakonda akazi ambiri achilendo kuphatikiza pa mwana wamkazi wa Farao. Inakonda akazi achimowabu, achiamoni, achiedomu, achisidoni, ndi achihiti.” (1 Maf. 11:1) Akazi ambiri a Solomo ayenera kuti anapitiriza kulambira milungu yonyenga ndipo zimenezi zinakhudzanso Solomo. Iye anasochera ndipo Mulungu, yemwe anakhala akumulezera mtima, anasiya kumukonda.—Werengani 1 Mafumu 11:4-8.
Zimene Tikuphunzira pa Chitsanzo cha Solomo Chabwino Ndiponso Choipa
19. Kodi m’Baibulo muli zitsanzo zabwino ziti?
19 Chifukwa cha kukoma mtima, Yehova anauzira Paulo kulemba kuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa Aroma 15:4) Zinthu zolembedwazo zikuphatikizapo amuna ndi akazi a chikhulupiriro cholimba amene anapereka chitsanzo chabwino. Paulo ananenanso kuti: “Nanga ndinenenso chiyani pamenepa? Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni, Baraki, Samisoni, Yefita, Davide, komanso Samueli ndi aneneri enanso. Mwa chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pa nkhondo, anachita chilungamo, analandira malonjezo, . . . anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu.” (Aheb. 11:32-34) Tiyenera kuphunzirapo kanthu pa zitsanzo zabwino za m’Baibulo n’kumayesetsa kuzitsanzira.
malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” (20, 21. N’chifukwa chiyani mukufunika kuphunzirapo kanthu pa zitsanzo za m’Mawu a Mulungu?
20 Koma nkhani zina za m’Baibulo zinalembedwa kuti zitichenjeze. Mwachitsanzo, pali amuna ndi akazi ena amene pa nthawi ina ankakondedwa ndi Yehova ndipo ankagwiritsidwa ntchito monga atumiki ake. Tikamawerenga Baibulo timaona zimene zinachititsa kuti anthu ena amene ankatumikira Mulungu asochere ndipo zingatithandize kuti tisachite zimenezo. Tikhoza kuona kuti anthu ena anayamba pang’onopang’ono kukhala ndi maganizo olakwika ndipo kenako anadzasankha zinthu zolakwika n’kukumana ndi mavuto. Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amenewa? Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zinayamba bwanji? Kodi inenso zikhoza kundichitikira? Kodi chitsanzo chimenechi chingandithandize bwanji kupewa zoterezi?’
21 Tiyenera kuganizira kwambiri zitsanzo zimenezi chifukwa Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.”—1 Akor. 10:11.
Kodi Mwaphunzira Chiyani?
• N’chifukwa chiyani m’Baibulo muli zitsanzo zabwino ndi zoipa zomwe?
• Kodi Solomo anayamba bwanji kuchita zoipa?
• Kodi mukuphunzira chiyani pa zinthu zimene Solomo analakwitsa?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 9]
Solomo anagwiritsa ntchito nzeru yochokera kwa Mulungu
[Zithunzi patsamba 12]
Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene Solomo analakwitsa?