Mulungu Akuonetsa Chikondi Chake kwa Ife
Mulungu Akuonetsa Chikondi Chake kwa Ife
“Kukoma mtima kwakukulu [kudzalamulira] monga mfumu kudzera m’chilungamo. Zimenezi zichitike kuti moyo wosatha ubwere.”—AROMA 5:21.
1, 2. Kodi ndi mphatso ziwiri ziti zimene zatchulidwa, ndipo pa ziwirizi yofunika kwambiri ndi iti?
PULOFESA wina anati: “Mphatso yofunika kwambiri imene Aroma anasiyira anthu inali malamulo awo ndiponso mfundo yakuti anthu ayenera kukhala moyo wogwirizana ndi malamulo.” (Dr. David J. Williams wa ku yunivesite ya Melbourne ku Australia) Ngakhale kuti anthu angaone mphatso imeneyi kukhala yofunika, pali mphatso ina imene ndi yofunika kwambiri. Mphatso imeneyi ndi njira ya Mulungu yothandizira anthu kukhala ovomerezeka komanso olungama pamaso pake. Imathandizanso anthu kukhala ndi chiyembekezo chodzapulumuka n’kupeza moyo wosatha.
2 N’zoona kuti Mulungu anatsatira malamulo kuti apereke mphatso imeneyi. Koma m’chaputala 5 cha buku la Aroma, mtumwi Paulo sanangofotokoza za mmene Mulungu anatsatirira malamulowo. M’malomwake, iye anayamba ndi mawu olimbikitsa kwambiri akuti: “Tayesedwa olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro, [choncho] tiyeni tikhale pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.” Anthu amene amalandira mphatso ya Mulungu imeneyi amayambanso kumukonda kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Paulo. Iye analemba kuti: “Mulungu wadzaza chikondi chake m’mitima yathu kudzera mwa mzimu woyera.”—Aroma 5:1, 5.
3. Kodi tingafunse mafunso ati?
3 N’chifukwa chiyani mphatso imeneyi inafunika kuperekedwa? Kodi Mulungu anayenera kuchita chiyani kuti aipereke mwachilungamo? Kodi anthu ayenera kuchita chiyani kuti akhale oyenerera kulandira mphatsoyi? Tiyeni tipeze mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa ndipo tione mmene amasonyezera chikondi cha Mulungu.
Mulungu Wasonyeza Chikondi kwa Anthu Ochimwa
4, 5. (a) Kodi Yehova anasonyeza chikondi chake m’njira yaikulu iti? (b) Kodi tiyenera kudziwa chiyani kuti timvetse lemba la Aroma 5:12?
4 Yehova anasonyeza chikondi chachikulu kwambiri pamene anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kuti adzathandize anthu. Paulo anafotokoza zimenezi ponena kuti: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Taganizirani mawu amene ananena akuti: “Pamene tinali ochimwa.” Aliyense amafunika kudziwa mmene tinakhalira ochimwa.
5 Poyamba Paulo anafotokoza kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Timadziwa bwino zimenezi chifukwa chakuti Mulungu anauzira anthu kuti alembe mmene moyo wa anthu unayambira. Yehova analenga anthu awiri oyambirira, omwe ndi Adamu ndi Hava. Mlengi ndi wangwiro ndipo makolo athu oyambirirawo analinso angwiro. Mulungu anawapatsa lamulo limodzi lokha ndipo anawauza kuti ngati samvera lamulolo adzafa. (Gen. 2:17) Koma iwo anasankha kuchita zinthu zowawonongetsa. Anaphwanya lamulo losavuta kutsatirali ndipo pochita zimenezi anakana zoti Mulungu ndi woyenera kuwapatsa malamulo ndiponso kuwalamulira.—Deut. 32:4, 5.
6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani ana a Adamu ankamwalira Mulungu asanapereke Chilamulo cha Mose ndiponso atapereka? (b) Kodi zotsatira za uchimo umene tinatengera tingaziyerekeze ndi chiyani?
6 Adamu anayamba kukhala ndi ana atachimwa kale choncho anapatsira anawo uchimo ndiponso zotsatira zake. Anawo sanaphwanye lamulo la Mulungu limene Adamu anaphwanya chotero iwo sanaimbidwe mlandu wofanana ndi iyeyo. Komanso pa nthawiyo anali asanapatsidwe malamulo. (Gen. 2:17) Komabe ana a Adamu anatengera uchimowo. Choncho uchimo ndi imfa zinalamulira mpaka nthawi imene Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo. Malamulowo anawathandiza kuzindikira kuti ndi ochimwa. (Werengani Aroma 5:13, 14.) Zotsatira za uchimo umene tinatengera tingaziyerekeze ndi matenda amene munthu amapatsira mwana wake. N’zoona kuti si ana onse amene amatengera ngakhale ngati makolo awo akudwala matendawo. Koma si mmene zilili ndi uchimo. Mwana aliyense amatengera ndipo amavutika nawo. Nthawi zonse zotsatira zake ndi imfa. Kodi pali njira iliyonse yothetsera vutoli?
Zimene Mulungu Anapereka Kudzera mwa Yesu Khristu
7, 8. Kodi zochita za anthu awiri angwiro zinali ndi zotsatira zosiyana ziti?
7 Chifukwa cha chikondi, Yehova anakonza njira yoti anthu amasuke ku uchimo umene anatengera. Paulo anafotokoza kuti zimenezi n’zotheka ndi munthu wina wangwiro amene anadzakhala ngati Adamu wachiwiri. (1 Akor. 15:45) Koma zochita za munthu wangwiro ameneyu zinali ndi zotsatira zosiyana kwambiri ndi za Adamu woyamba, yemwe analinso wangwiro. Kodi zinasiyana bwanji?—Werengani Aroma 5:15, 16.
8 Paulo analemba kuti: “Mmene zilili ndi mphatsoyi si mmene zinalili ndi uchimowo.” Adamu anachimwa ndipo analandira chilango choyenera, chomwe chinali imfa. Koma imfa sinangokhudza iye yekha. Paulo anati: “Mwa uchimo wa munthu mmodzi [ameneyu] ambiri anafa.” Choncho ana onse a Adamu, kuphatikizapo ifeyo, ayenera kufa chifukwa nawonso ndi ochimwa. Komabe n’zolimbikitsa kudziwa kuti zochita za munthu wangwiro, yemwe ndi Yesu, zinali ndi zotsatira zosiyana kwambiri ndi za Adamu. Kodi zotsatira zake n’zotani? Paulo anayankha ponena kuti: “Anthu kaya akhale amtundu wotani akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.”—Aroma 5:18.
9. Kodi mawu a pa Aroma 5:16, 18 onena kuti anthu akuyesedwa kapena kuti akutchedwa olungama akutanthauza kuti Mulungu anachita chiyani?
9 Kodi mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “atchedwe olungama” ndiponso akuti
“akuyesedwa olungama” akutanthauza chiyani? Munthu wina womasulira Baibulo anati: “Mawu amenewa akufotokoza zinthu ngati zikuchitika m’khoti motsatira malamulo. Mawuwa akusonyeza kuti Mulungu wasintha mmene akuonera munthu osati kuti munthuyo wasintha . . . Zili ngati kuti munthu akuimbidwa mlandu wakuti ndi wosalungama ndipo Mulungu ndi woweruza yemwe wagamula kuti munthuyu amasulidwe.”10. Kodi Yesu anachita chiyani kuti anthu ayesedwe olungama?
10 Kodi “Woweruza wa dziko lonse lapansi” angamasule munthu wosalungama pa zifukwa ziti? (Gen. 18:25) Kuti izi zitheke, Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kudziko lapansi. Anachita zimenezi chifukwa cha chikondi. Yesu anachita chifuniro cha Atate ake popanda kulakwitsa kalikonse, ngakhale kuti anayesedwa, kunyozedwa kwambiri ndiponso kuzunzidwa. Iye anakhalabe wokhulupirika mpaka pamene anaphedwa pamtengo wozunzikirapo. (Aheb. 2:10) Yesu anapereka moyo wake wangwiro monga dipo lomasula kapena kuwombola ana a Adamu ku uchimo ndi imfa.—Mat. 20:28; Aroma 5:6-8.
11. Kodi dipo ndi lokwanira ndendende m’njira yotani?
11 Pa lemba lina, Paulo ananena kuti limeneli ndi “dipo lokwanira ndendende.” (1 Tim. 2:6) Kodi linali lokwanira ndendende m’njira yotani? Adamu anabweretsa uchimo ndi imfa kwa anthu mabiliyoni ambiri, omwe ndi ana ake. N’zoona kuti Yesu, monga munthu wangwiro, akanatha kukhala ndi ana angwiro mabiliyoni ambiri. * Choncho m’mbuyomu tinkaganiza kuti moyo wa Yesu limodzi ndi ana angwiro amene akanakhala nawo inali nsembe yokwanira ndendende moyo wa Adamu ndi ana ake opanda ungwiro. Koma Baibulo silinena kuti ana amene Yesu akanakhala nawo ndi mbali ya dipo. Lemba la Aroma 5:15-19 limanena momveka bwino kuti imfa ya “munthu mmodzi” inamasula anthu. Choncho moyo wangwiro wa Yesu ndi wokwanira ndendende moyo wa Adamu. Yesu Khristu yekha ndi amene anapereka moyo wake dipo. Yesu anachita “chinthu chimodzi cholungamitsa” ndipo anakhala womvera komanso wokhulupirika mpaka imfa. Izi zinachititsa kuti anthu amitundu yonse alandire mphatso yaulere yoti ayesedwe olungama ndiponso kulandira moyo. (2 Akor. 5:14, 15; 1 Pet. 3:18) Kodi zimenezi zinatheka bwanji?
Mulungu Amatikhululukira Kudzera mu Dipo
12, 13. N’chifukwa chiyani anthu amene amayesedwa olungama amafunikira chifundo ndi chikondi cha Mulungu?
12 Yehova Mulungu analandira nsembe ya dipo imene Mwana wake anapereka. (Aheb. 9:24; 10:10, 12) Komabe, ophunzira a Yesu padziko lapansi, ngakhale atumwi ake okhulupirika, anakhalabe opanda ungwiro. Ngakhale kuti ankayesetsa kupewa zoipa, nthawi zina ankalephera. N’chifukwa chiyani ankalephera? Chifukwa chakuti anatengera uchimo. (Aroma 7:18-20) Koma Mulungu anali ndi mphamvu yowathandiza pa vutoli ndipo anachitadi zimenezi. Iye analandira “dipo lokwanira ndendende” ndipo analigwiritsa ntchito kuti athandize anthu omutumikira.
13 Sikuti Mulungu anagwiritsa ntchito dipolo kuti akhululukire atumwi ndiponso anthu ena chifukwa chakuti iwo anachita zinthu zina zabwino ndipo anali oyenerera kukhululukidwa. M’malomwake, Mulungu analigwiritsa ntchito chifukwa cha chifundo ndi chikondi chake chachikulu. Iye anasankha kumasula atumwiwo ndiponso anthu ena ku mlandu wa uchimo umene anatengera n’kumawaona kuti ndi olungama. Paulo anatsindika mfundoyi ponena kuti: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kumeneku, ndithudi mwapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro, osati mwa inu nokha, koma monga mphatso ya Mulungu.”—Aef. 2:8.
14, 15. Kodi anthu amene amatchedwa olungama ndi Mulungu amakhala ndi chiyembekezo chotani koma iwo amayenerabe kuchita chiyani?
14 Kukhululukidwa uchimo umene tinatengera komanso machimo amene tachita ndi mphatso yaikulu kwambiri yochokera kwa Wamphamvuyonse. Munthu asanakhale Mkhristu amachita machimo osawerengeka, koma Mulungu amatha kukhululukira machimo onsewa chifukwa cha dipo. Paulo analemba kuti: “Mphatso imene inatsatira machimo ambiri, inachititsa kuti anthu atchedwe olungama.” (Aroma 5:16) Atumwi ndiponso anthu ena amene alandira mphatso imeneyi (ya kutchedwa olungama) ayenera kukhalabe ndi chikhulupiriro polambira Mulungu woona. Kodi iwo ali ndi chiyembekezo chotani? Anthu “amene alandira kukoma mtima kwakukulu kochuluka ndiponso mphatso yaulere yaikuluyo ya chilungamo, adzakhala ndi moyo ndi kulamulira monga mafumu kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.” Mphatso ya chilungamo imachita zosiyana kwambiri ndi uchimo. Zotsatira za mphatsoyi ndi moyo.—Aroma 5:17; werengani Luka 22:28-30.
15 Anthu amene amalandira mphatso ya kutchedwa olungama imeneyi amakhala ana auzimu a Mulungu. Popeza kuti iwo ndi olandira cholowa anzake a Khristu, ali ndi chiyembekezo choukitsidwa n’kupita kumwamba kukakhala ana auzimu enieni ndiponso “kulamulira monga mafumu” limodzi ndi Yesu Khristu.—Werengani Aroma 8:15-17, 23.
Mulungu Wasonyeza Chikondi kwa Anthu Enanso
16. Kodi anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi angalandire mphatso yotani?
16 Sikuti anthu onse amene amakhulupirira Mulungu n’kumamutumikira mokhulupirika amayembekeza “kulamulira monga mafumu” ndi Khristu kumwamba. Anthu ambiri ali ndi chiyembekezo chotchulidwa m’Baibulo chofanana ndi cha atumiki a Mulungu amene anakhalapo Chikhristu chisanayambe. Iwo amayembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Kodi iwo angalandire mphatso ya Mulungu panopa n’kumaonedwa kuti ndi olungama pamene akuyembekezera moyo padziko lapansi? Malinga ndi zimene Paulo analembera Aroma, yankho lolimbikitsa ndi lakuti inde.
17, 18. (a) Kodi Mulungu ankaona bwanji Abulahamu chifukwa cha chikhulupiriro chake? (b) Kodi zinatheka bwanji kuti Yehova aziona Abulahamu kukhala wolungama?
17 Paulo anapereka chitsanzo chabwino cha Abulahamu pa nkhani imeneyi. Abulahamu anakhala wokhulupirika Yehova asanapereke malamulo kwa Aisiraeli ndiponso Khristu asanatsegule njira yopita kumwamba. (Aheb. 10:19, 20) Baibulo limati: “Abulahamu kapena mbewu yake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha chilamulo ayi. Analandira lonjezolo chifukwa chakuti anali wolungama mwa chikhulupiriro.” (Aroma 4:13; Yak. 2:23, 24) Choncho Mulungu ankaona Abulahamu, yemwe anali wokhulupirika, kukhala wolungama.—Werengani Aroma 4:20-22.
18 Mawu akuti anali wolungama sakutanthauza kuti pa zaka zonse zimene Abulahamu ankatumikira Yehova sankachimwa. (Aroma 3:10, 23) Koma popeza Yehova ali ndi nzeru zopanda malire, anachita zinthu moganizira chikhulupiriro champhamvu chimene Abulahamu anali nacho ndiponso zimene anachita chifukwa cha chikhulupirirocho. Kwenikweni Abulahamu ankakhulupirira “mbewu” imene inali kudzabadwa mu mzera wa mbadwa zake. Mbewu imeneyi inadzakhala Mesiya, kapena kuti Khristu. (Gen. 15:6; 22:15-18) Choncho chifukwa cha “dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu,” Mulungu yemwe ndi woweruza angakhululukire machimo amene anachitidwa m’mbuyomu. Izi zachititsa kuti Abulahamu ndiponso anthu ena okhulupirika amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, adzaukitsidwe.—Werengani Aroma 3:24, 25; Sal. 32:1, 2.
Panopa Tingaonedwe Kukhala Olungama
19. N’chifukwa chiyani mfundo yakuti Mulungu anaona Abulahamu kukhala wolungama ndi yolimbikitsa kwa anthu ambiri masiku ano?
19 Mfundo yakuti Mulungu wachikondi ankaona kuti Abulahamu ndi wolungama ndi yolimbikitsa kwa Akhristu oona masiku ano. Abulahamu sanatchedwe wolungama ndi Yehova m’njira yofanana ndi anthu amene Mulungu amawadzoza ndi mzimu wake kuti akhale “olandira cholowa anzake a Khristu.” Anthu a m’kagulu kameneka ndi “oitanidwa kukhala oyera” ndipo amavomerezedwa kukhala “ana a Mulungu.” (Aroma 1:7; 8:14, 17, 33) Mosiyana ndi zimenezi, Abulahamu anakhala “bwenzi la Yehova” ngakhale kuti nsembe ya dipo inali isanaperekedwe. (Yak. 2:23; Yes. 41:8) Nanga bwanji za Akhristu oona amene akuyembekezera kudzakhala m’Paradaiso padziko lapansi?
20. Kodi anthu amene Mulungu amawaona kuti ndi olungama, ngati mmene ankamuonera Abulahamu, amachita zotani?
20 Iwo sanalandire ‘mphatso yaulere ya chilungamo’ ndipo sayembekezera moyo wa kumwamba chifukwa chomasulidwa ndi “dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu.” (Aroma 3:24; 5:15, 17) Ngakhale zili choncho, iwo amakhulupirira kwambiri Mulungu ndiponso zinthu zimene wapereka. Iwo amagwira ntchito zabwino posonyeza chikhulupirirocho. Ntchito ina yabwino imene amagwira ndi ‘kulalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.’ (Mac. 28:31) Chifukwa cha zimenezi, Yehova amawaona kuti ndi olungama ngati mmene anachitira ndi Abulahamu. Mphatso imene iwowo amalandira, yomwe ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, ndi yosiyana ndi “mphatso yaulere” imene Akhristu odzozedwa amalandira. Koma iwo amayamikira kwambiri mphatso imeneyi.
21. Kodi ndi mwayi uti umene ulipo chifukwa cha chikondi ndi chilungamo cha Yehova?
21 Ngati muli ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, muyenera kuzindikira kuti chiyembekezo chimenechi n’chosiyana ndi zinthu zimene olamulira padziko lapansi amalonjeza. Mphatso imeneyi tailandira chifukwa cha cholinga chanzeru cha Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Yehova wachita zinthu zosiyanasiyana kuti akwaniritse cholinga chakechi. Zinthu zimene wachita n’zogwirizana ndi chilungamo chenicheni ndipo zasonyeza kuti Mulungu ali ndi chikondi chachikulu. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.”—Aroma 5:8.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Mwachitsanzo, zimenezi zinafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2000, tsamba 4, ndime 4 ndiponso m’buku lakuti Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 736, ndime 4 ndi 5.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ana a Adamu anatengera chiyani ndipo zotsatira zake n’zotani?
• Kodi dipo lokwanira ndendende linaperekedwa bwanji ndipo ndi lokwanira m’njira yotani?
• Kodi muli ndi chiyembekezo chotani chifukwa cholandira mphatso ya kutchedwa olungama?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 13]
Adamu, yemwe anali munthu wangwiro, anachimwa. Yesu, yemwe analinso wangwiro, anapereka “dipo lokwanira ndendende”
[Chithunzi patsamba 15]
Tingayesedwe olungama kudzera mwa Yesu. Umenewutu ndi uthenga wabwino kwambiri